Esther 10 (BOGWICC)
1 Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. 2 Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? 3 Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.