Psalms 21 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka! 2 Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wakendipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. Sela 3 Inu munayilandira ndi madalitso ochulukandipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake. 4 Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsamasiku ochuluka kwamuyaya. 5 Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu. 6 Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu. 7 Pakuti mfumu imadalira Yehova;kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,iyo sidzagwedezeka. 8 Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu. 9 Pa nthawi ya kuonekera kwanumudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.Mu ukali wake Yehova adzawameza,ndipo moto wake udzawatha. 10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,zidzukulu zawo pakati pa anthu. 11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawosadzapambana; 12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawopamene mudzawaloza ndi mivi yanu. 13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.