Psalms 63 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. 1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,moona mtima ine ndimakufunafunani;moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,thupi langa likulakalaka inu,mʼdziko lowuma ndi lotopetsakumene kulibe madzi. 2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulikandipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. 3 Chifukwa chikondi chanundi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani. 4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga. 5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya. 6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku. 7 Chifukwa ndinu thandizo langa,ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu. 8 Moyo wanga umakangamira Inu;dzanja lanu lamanja limandigwiriziza. 9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi. 10 Iwo adzaperekedwa ku lupangandi kukhala chakudya cha ankhandwe. 11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.