2 Kings 25 (BOGWICC)

1 Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo. 2 Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya. 3 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya. 4 Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba, 5 koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. 6 Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo. 7 Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni. 8 Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 9 Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika. 10 Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu. 11 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 12 Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina. 13 Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni. 14 Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo. 15 Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva. 16 Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka. 17 Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde. 18 Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo. 19 Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo. 20 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula. 21 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha.Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo. 22 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala woyangʼanira anthu amene anatsala ku Yuda. 23 Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo. 24 Gedaliya analumbira powatsimikizira iwo ndi anthu awo. Iye anati, “Musachite mantha ndi atsogoleri Ababuloniwa. Khalani mʼdziko muno ndipo tumikirani mfumu ya Babuloni. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino.” 25 Koma pa mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, anabwera ndi anthu khumi ndipo anapha Gedaliya pamodzi ndi Ayuda ndi anthu a ku Babuloni amene anali naye limodzi ku Mizipa. 26 Chifukwa cha zimenezi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo anathawira ku Igupto chifukwa choopa Ababuloni. 27 Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27. 28 Anamukomera mtima namukweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye ku Babuloni. 29 Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake. 30 Mfumu inkamupatsa Yehoyakini chakudya tsiku lililonse pa moyo wake wonse.

In Other Versions

2 Kings 25 in the ANGEFD

2 Kings 25 in the ANTPNG2D

2 Kings 25 in the AS21

2 Kings 25 in the BAGH

2 Kings 25 in the BBPNG

2 Kings 25 in the BBT1E

2 Kings 25 in the BDS

2 Kings 25 in the BEV

2 Kings 25 in the BHAD

2 Kings 25 in the BIB

2 Kings 25 in the BLPT

2 Kings 25 in the BNT

2 Kings 25 in the BNTABOOT

2 Kings 25 in the BNTLV

2 Kings 25 in the BOATCB

2 Kings 25 in the BOATCB2

2 Kings 25 in the BOBCV

2 Kings 25 in the BOCNT

2 Kings 25 in the BOECS

2 Kings 25 in the BOHCB

2 Kings 25 in the BOHCV

2 Kings 25 in the BOHLNT

2 Kings 25 in the BOHNTLTAL

2 Kings 25 in the BOICB

2 Kings 25 in the BOILNTAP

2 Kings 25 in the BOITCV

2 Kings 25 in the BOKCV

2 Kings 25 in the BOKCV2

2 Kings 25 in the BOKHWOG

2 Kings 25 in the BOKSSV

2 Kings 25 in the BOLCB

2 Kings 25 in the BOLCB2

2 Kings 25 in the BOMCV

2 Kings 25 in the BONAV

2 Kings 25 in the BONCB

2 Kings 25 in the BONLT

2 Kings 25 in the BONUT2

2 Kings 25 in the BOPLNT

2 Kings 25 in the BOSCB

2 Kings 25 in the BOSNC

2 Kings 25 in the BOTLNT

2 Kings 25 in the BOVCB

2 Kings 25 in the BOYCB

2 Kings 25 in the BPBB

2 Kings 25 in the BPH

2 Kings 25 in the BSB

2 Kings 25 in the CCB

2 Kings 25 in the CUV

2 Kings 25 in the CUVS

2 Kings 25 in the DBT

2 Kings 25 in the DGDNT

2 Kings 25 in the DHNT

2 Kings 25 in the DNT

2 Kings 25 in the ELBE

2 Kings 25 in the EMTV

2 Kings 25 in the ESV

2 Kings 25 in the FBV

2 Kings 25 in the FEB

2 Kings 25 in the GGMNT

2 Kings 25 in the GNT

2 Kings 25 in the HARY

2 Kings 25 in the HNT

2 Kings 25 in the IRVA

2 Kings 25 in the IRVB

2 Kings 25 in the IRVG

2 Kings 25 in the IRVH

2 Kings 25 in the IRVK

2 Kings 25 in the IRVM

2 Kings 25 in the IRVM2

2 Kings 25 in the IRVO

2 Kings 25 in the IRVP

2 Kings 25 in the IRVT

2 Kings 25 in the IRVT2

2 Kings 25 in the IRVU

2 Kings 25 in the ISVN

2 Kings 25 in the JSNT

2 Kings 25 in the KAPI

2 Kings 25 in the KBT1ETNIK

2 Kings 25 in the KBV

2 Kings 25 in the KJV

2 Kings 25 in the KNFD

2 Kings 25 in the LBA

2 Kings 25 in the LBLA

2 Kings 25 in the LNT

2 Kings 25 in the LSV

2 Kings 25 in the MAAL

2 Kings 25 in the MBV

2 Kings 25 in the MBV2

2 Kings 25 in the MHNT

2 Kings 25 in the MKNFD

2 Kings 25 in the MNG

2 Kings 25 in the MNT

2 Kings 25 in the MNT2

2 Kings 25 in the MRS1T

2 Kings 25 in the NAA

2 Kings 25 in the NASB

2 Kings 25 in the NBLA

2 Kings 25 in the NBS

2 Kings 25 in the NBVTP

2 Kings 25 in the NET2

2 Kings 25 in the NIV11

2 Kings 25 in the NNT

2 Kings 25 in the NNT2

2 Kings 25 in the NNT3

2 Kings 25 in the PDDPT

2 Kings 25 in the PFNT

2 Kings 25 in the RMNT

2 Kings 25 in the SBIAS

2 Kings 25 in the SBIBS

2 Kings 25 in the SBIBS2

2 Kings 25 in the SBICS

2 Kings 25 in the SBIDS

2 Kings 25 in the SBIGS

2 Kings 25 in the SBIHS

2 Kings 25 in the SBIIS

2 Kings 25 in the SBIIS2

2 Kings 25 in the SBIIS3

2 Kings 25 in the SBIKS

2 Kings 25 in the SBIKS2

2 Kings 25 in the SBIMS

2 Kings 25 in the SBIOS

2 Kings 25 in the SBIPS

2 Kings 25 in the SBISS

2 Kings 25 in the SBITS

2 Kings 25 in the SBITS2

2 Kings 25 in the SBITS3

2 Kings 25 in the SBITS4

2 Kings 25 in the SBIUS

2 Kings 25 in the SBIVS

2 Kings 25 in the SBT

2 Kings 25 in the SBT1E

2 Kings 25 in the SCHL

2 Kings 25 in the SNT

2 Kings 25 in the SUSU

2 Kings 25 in the SUSU2

2 Kings 25 in the SYNO

2 Kings 25 in the TBIAOTANT

2 Kings 25 in the TBT1E

2 Kings 25 in the TBT1E2

2 Kings 25 in the TFTIP

2 Kings 25 in the TFTU

2 Kings 25 in the TGNTATF3T

2 Kings 25 in the THAI

2 Kings 25 in the TNFD

2 Kings 25 in the TNT

2 Kings 25 in the TNTIK

2 Kings 25 in the TNTIL

2 Kings 25 in the TNTIN

2 Kings 25 in the TNTIP

2 Kings 25 in the TNTIZ

2 Kings 25 in the TOMA

2 Kings 25 in the TTENT

2 Kings 25 in the UBG

2 Kings 25 in the UGV

2 Kings 25 in the UGV2

2 Kings 25 in the UGV3

2 Kings 25 in the VBL

2 Kings 25 in the VDCC

2 Kings 25 in the YALU

2 Kings 25 in the YAPE

2 Kings 25 in the YBVTP

2 Kings 25 in the ZBP