Psalms 103 (BOGWICC)

undefined Salimo la Davide. 1 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera. 2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,ndipo usayiwale zabwino zake zonse. 3 Amene amakhululuka machimo ako onsendi kuchiritsa nthenda zako zonse, 4 amene awombola moyo wako ku dzenjendi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu, 5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu. 6 Yehova amachita chilungamondipo amaweruza molungama onse opsinjika. 7 Iye anadziwitsa Mose njira zake,ntchito zake kwa Aisraeli. 8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka. 9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse,kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya; 10 satichitira molingana ndi machimo athu,kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu. 11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa; 12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe. 13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa; 14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,amakumbukira kuti ndife fumbi. 15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,amaphuka ngati duwa la mʼmunda; 16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekansondipo malo ake sakumbukirikanso. 17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyayachikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo; 18 iwo amene amasunga pangano lakendi kukumbukira kumvera malangizo ake. 19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwambandipo ufumu wake umalamulira onse. 20 Tamandani Yehova, inu angelo ake,amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,amene mumamvera mawu ake. 21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake. 22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonsekulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

In Other Versions

Psalms 103 in the ANGEFD

Psalms 103 in the ANTPNG2D

Psalms 103 in the AS21

Psalms 103 in the BAGH

Psalms 103 in the BBPNG

Psalms 103 in the BBT1E

Psalms 103 in the BDS

Psalms 103 in the BEV

Psalms 103 in the BHAD

Psalms 103 in the BIB

Psalms 103 in the BLPT

Psalms 103 in the BNT

Psalms 103 in the BNTABOOT

Psalms 103 in the BNTLV

Psalms 103 in the BOATCB

Psalms 103 in the BOATCB2

Psalms 103 in the BOBCV

Psalms 103 in the BOCNT

Psalms 103 in the BOECS

Psalms 103 in the BOHCB

Psalms 103 in the BOHCV

Psalms 103 in the BOHLNT

Psalms 103 in the BOHNTLTAL

Psalms 103 in the BOICB

Psalms 103 in the BOILNTAP

Psalms 103 in the BOITCV

Psalms 103 in the BOKCV

Psalms 103 in the BOKCV2

Psalms 103 in the BOKHWOG

Psalms 103 in the BOKSSV

Psalms 103 in the BOLCB

Psalms 103 in the BOLCB2

Psalms 103 in the BOMCV

Psalms 103 in the BONAV

Psalms 103 in the BONCB

Psalms 103 in the BONLT

Psalms 103 in the BONUT2

Psalms 103 in the BOPLNT

Psalms 103 in the BOSCB

Psalms 103 in the BOSNC

Psalms 103 in the BOTLNT

Psalms 103 in the BOVCB

Psalms 103 in the BOYCB

Psalms 103 in the BPBB

Psalms 103 in the BPH

Psalms 103 in the BSB

Psalms 103 in the CCB

Psalms 103 in the CUV

Psalms 103 in the CUVS

Psalms 103 in the DBT

Psalms 103 in the DGDNT

Psalms 103 in the DHNT

Psalms 103 in the DNT

Psalms 103 in the ELBE

Psalms 103 in the EMTV

Psalms 103 in the ESV

Psalms 103 in the FBV

Psalms 103 in the FEB

Psalms 103 in the GGMNT

Psalms 103 in the GNT

Psalms 103 in the HARY

Psalms 103 in the HNT

Psalms 103 in the IRVA

Psalms 103 in the IRVB

Psalms 103 in the IRVG

Psalms 103 in the IRVH

Psalms 103 in the IRVK

Psalms 103 in the IRVM

Psalms 103 in the IRVM2

Psalms 103 in the IRVO

Psalms 103 in the IRVP

Psalms 103 in the IRVT

Psalms 103 in the IRVT2

Psalms 103 in the IRVU

Psalms 103 in the ISVN

Psalms 103 in the JSNT

Psalms 103 in the KAPI

Psalms 103 in the KBT1ETNIK

Psalms 103 in the KBV

Psalms 103 in the KJV

Psalms 103 in the KNFD

Psalms 103 in the LBA

Psalms 103 in the LBLA

Psalms 103 in the LNT

Psalms 103 in the LSV

Psalms 103 in the MAAL

Psalms 103 in the MBV

Psalms 103 in the MBV2

Psalms 103 in the MHNT

Psalms 103 in the MKNFD

Psalms 103 in the MNG

Psalms 103 in the MNT

Psalms 103 in the MNT2

Psalms 103 in the MRS1T

Psalms 103 in the NAA

Psalms 103 in the NASB

Psalms 103 in the NBLA

Psalms 103 in the NBS

Psalms 103 in the NBVTP

Psalms 103 in the NET2

Psalms 103 in the NIV11

Psalms 103 in the NNT

Psalms 103 in the NNT2

Psalms 103 in the NNT3

Psalms 103 in the PDDPT

Psalms 103 in the PFNT

Psalms 103 in the RMNT

Psalms 103 in the SBIAS

Psalms 103 in the SBIBS

Psalms 103 in the SBIBS2

Psalms 103 in the SBICS

Psalms 103 in the SBIDS

Psalms 103 in the SBIGS

Psalms 103 in the SBIHS

Psalms 103 in the SBIIS

Psalms 103 in the SBIIS2

Psalms 103 in the SBIIS3

Psalms 103 in the SBIKS

Psalms 103 in the SBIKS2

Psalms 103 in the SBIMS

Psalms 103 in the SBIOS

Psalms 103 in the SBIPS

Psalms 103 in the SBISS

Psalms 103 in the SBITS

Psalms 103 in the SBITS2

Psalms 103 in the SBITS3

Psalms 103 in the SBITS4

Psalms 103 in the SBIUS

Psalms 103 in the SBIVS

Psalms 103 in the SBT

Psalms 103 in the SBT1E

Psalms 103 in the SCHL

Psalms 103 in the SNT

Psalms 103 in the SUSU

Psalms 103 in the SUSU2

Psalms 103 in the SYNO

Psalms 103 in the TBIAOTANT

Psalms 103 in the TBT1E

Psalms 103 in the TBT1E2

Psalms 103 in the TFTIP

Psalms 103 in the TFTU

Psalms 103 in the TGNTATF3T

Psalms 103 in the THAI

Psalms 103 in the TNFD

Psalms 103 in the TNT

Psalms 103 in the TNTIK

Psalms 103 in the TNTIL

Psalms 103 in the TNTIN

Psalms 103 in the TNTIP

Psalms 103 in the TNTIZ

Psalms 103 in the TOMA

Psalms 103 in the TTENT

Psalms 103 in the UBG

Psalms 103 in the UGV

Psalms 103 in the UGV2

Psalms 103 in the UGV3

Psalms 103 in the VBL

Psalms 103 in the VDCC

Psalms 103 in the YALU

Psalms 103 in the YAPE

Psalms 103 in the YBVTP

Psalms 103 in the ZBP