Psalms 20 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze. 2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;akugwirizize kuchokera ku Ziyoni. 3 Iye akumbukire nsembe zako zonsendipo alandire nsembe zako zopsereza. Sela 4 Akupatse chokhumba cha mtima wakondipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike. 5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambanandipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,Yehova ayankhe zopempha zako zonse. 6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulikandi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja. 7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalokoma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu. 8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,koma ife timadzuka ndi kuyima chilili. 9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!Tiyankheni pamene tikuyitanani!