Psalms 32 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Malangizo. 1 Ngodala munthuamene zolakwa zake zakhululukidwa;amene machimo ake aphimbidwa. 2 Ngodala munthuamene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iyendipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo. 3 Pamene ndinali chete,mafupa anga anakalambachifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse. 4 Pakuti usana ndi usikudzanja lanu linandipsinja;mphamvu zanga zinathamonga nthawi yotentha yachilimwe. Sela 5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,sindinabise mphulupulu zanga.Ndinati, “Ine ndidzawululazolakwa zanga kwa Yehova,ndipo Inu munandikhululukiramlandu wa machimo anga.” Sela 6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyopomwe mukupezeka;ndithu pamene madzi amphamvu auka,sadzamupeza. 7 Inu ndi malo anga obisala;muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizingandi nyimbo zachipulumutso. Sela 8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. 9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu,zimene zilibe nzeru,koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,ukapanda kutero sizibwera kwa iwe. 10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipakoma chikondi chosatha cha Yehovachimamuzinga munthu amene amadalira Iye. 11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!