Psalms 53 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide. 1 Chitsiru chimati mu mtima mwake,“Kulibe Mulungu.”Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino. 2 Mulungu kumwamba amayangʼana pansi panopa ana a anthukuti aone ngati alipo wina wanzeru,wofunafuna Mulungu. 3 Aliyense wabwerera,iwo onse pamodzi akhala oyipa;palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,ngakhale mmodzi. 4 Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,ndipo sapemphera kwa Mulungu? 5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulupamene panalibe kanthu kochititsa mantha.Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza. 6 Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!