Psalms 62 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide. 1 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;chipulumutso changa chimachokera kwa Iye. 2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka. 3 Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,ngati mpanda wogwedezeka? 4 Iwo akufunitsitsa kumugwetsakuti achoke pa malo ake apamwamba.Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.Ndi pakamwa pawo amadalitsakoma mʼmitima yawo amatemberera. 5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;chiyembekezo changa chichokera mwa Iye. 6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka. 7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga. 8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;khuthulani mitima yanu kwa Iye,pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. Sela 9 Anthu wamba ndi mpweya chabe;anthu apamwamba ndi bodza chabe;ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe 10 Musadalire kulanda mwachinyengokapena katundu wobedwa;ngakhale chuma chanu chichuluke,musayike mtima wanu pa icho. 11 Mulungu wayankhula kamodzi,ine ndamvapo zinthu ziwiri;choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu, 12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthumolingana ndi ntchito zake.