Psalms 72 (BOGWICC)
undefined Salimo la Solomoni. 1 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu. 2 Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,anthu anu ozunzika mosakondera. 3 Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo. 4 Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthundi kupulumutsa ana a anthu osowa;adzaphwanya ozunza anzawo. 5 Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala. 6 Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwangati mivumbi yothirira dziko lapansi. 7 Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala. 8 Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inandiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi. 9 Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pakendipo adani ake adzanyambita fumbi. 10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutaliadzabweretsa mitulo kwa iye,mafumu a ku Seba ndi Sebaadzapereka mphatso kwa iyeyo. 11 Mafumu onse adzamuweramirandipo mitundu yonse idzamutumikira. 12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,wozunzika amene alibe wina womuthandiza. 13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowandi kupulumutsa osowa ku imfa. 14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawapakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake. 15 Iye akhale ndi moyo wautali;golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.Anthu amupempherere nthawi zonsendi kumudalitsa tsiku lonse. 16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;zichuluke ngati udzu wakuthengo 17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iyendipo iwo adzamutcha iye wodala. 18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeliamene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa. 19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyayadziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.Ameni ndi Ameni. 20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.