1 Kings 12 (BOGWICC)

1 Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse nʼkuti atapita kumeneko kukamulonga ufumu. 2 Yeroboamu mwana wa Nebati anamva zimenezi. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamuyo akukhala ku Igupto, pakuti atathawa Mfumu Solomoni iyeyo anakakhala ku Igupto. 3 Tsono anthu anayitanitsa Yeroboamu, ndipo iye pamodzi ndi gulu lonse la ku Israeli anapita kwa Rehobowamu ndipo anamuwuza kuti, 4 “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri, koma inu chepetsani ntchito yowawa pa ife ndipo peputsani goli lolemetsa limene anatisenzetsa. Mukatero tidzakutumikirani.” 5 Rehobowamu anayankha kuti, “Pitani, ndipo pakatha masiku atatu, mudzabwerenso.” Choncho anthuwo anapitadi. 6 Ndipo Mfumu Rehobowamu anapempha nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira Solomoni abambo ake pamene anali ndi moyo. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu amenewa?” 7 Iwo anayankha kuti, “Ngati lero mudzakhala mtumiki wa anthu amenewa ndi kuwatumikira ndipo mukawayankha bwino, iwowo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.” 8 Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakuluwo anamupatsa ndipo anafunsira nzeru kwa anyamata anzake amene anakulira nawo limodzi omwe ankamutumikira. 9 Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ngotani? Kodi ndiwayankhe chiyani anthu amene akunena kwa ine kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anatisenzetsa’?” 10 Anyamata anzake amene anakula nawo limodzi aja anamuyankha kuti, “Anthu amene ananena kwa iwe kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa, koma inu peputsani goli lathu,’ uwawuze kuti ‘Chala changa chakanise nʼchachikulu kupambana chiwuno cha abambo anga. 11 Abambo anga ankakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzachititsa kuti likhale lolemera kwambiri. Abambo anga ankakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’ ” 12 Patapita masiku atatu, Yeroboamu pamodzi ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu, monga momwe inanenera mfumu kuti, “Mudzabwere pakatha masiku atatu.” 13 Mfumuyo inawayankha anthuwo mwankhanza. Kukana malangizo amene akuluakulu anayipatsa. 14 Anatsatira malangizo amene anyamata anzake anamupatsa ndipo anati “Abambo anga ankakusenzetsani goli lolemetsa. Ine ndidzachititsa kuti likhale lolemera kwambiri. Abambo anga ankakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” 15 Choncho mfumu sinamvere pempho la anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Yehova, kukwaniritsa mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo. 16 Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kumva zopempha zawo, iwo anayankha mfumu kuti,“Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide,ndi gawo lanjinso mwa mwana wa Yese?Inu Aisraeli, bwererani ku matenti anu!Ziyangʼanira nyumba yako, Iwe Davide!”Kotero Aisraeli anachoka napita ku nyumba zawo. 17 Koma Aisraeli amene ankakhala mʼmizinda ya Yuda ankalamuliridwa ndi Rehobowamu. 18 Mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli onse anamugeda ndi miyala mpaka kumupha. Koma Mfumu Rehobowamu anakwera msangamsanga galeta wake nathawira ku Yerusalemu. 19 Choncho Aisraeli akhala akuwukira nyumba ya Davide mpaka lero lino. 20 Aisraeli onse atamva kuti Yeroboamu wabwerera kuchokera ku Igupto, anatumiza mawu okamuyitana kuti abwere ku msonkhano ndipo anamuyika kukhala mfumu ya Aisraeli onse. Fuko la Yuda lokha ndi lomwe linkatsatira nyumba ya Davide. 21 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini, nasankha ankhondo okwanira 180,000, kuti akamenyane ndi nyumba ya Israeli kuti amubwezere Rehobowamu mwana wa Solomoni ufumu wake. 22 Koma Mulungu anayankhula ndi Semaya, munthu wa Mulungu kuti, 23 “Nena kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, kwa nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini, ndiponso kwa anthu ena onse kuti, 24 ‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu Aisraeli. Aliyense wa inu abwerere kwawo, pakuti zimenezi ndachita ndine.’ ” Choncho anthuwo anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera kwawo, monga analamulira Yehova. 25 Tsono Yeroboamu anamanga mzinda wa Sekemu mʼdziko la mapiri la Efereimu ndipo anakhala kumeneko. Kuchokera kumeneko anapita kukamanga mzinda wa Penueli. 26 Yeroboamu anaganiza mu mtima mwake kuti, “Ndithu, ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide. 27 Ngati anthuwa azipitabe kukapereka nsembe ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, adzayambanso kutsatira mbuye wawo Rehobowamu, mfumu ya Yuda. Adzandipha ndi kubwerera kwa Mfumu Rehobowamu.” 28 Itapempha nzeru, mfumuyo inapanga mafano awiri a ana angʼombe. Mfumuyo inati kwa anthuwo, “Mwakhala mukupita ku Yerusalemu nthawi yayitali. Iwe Israeli, nayi milungu yako imene inakutulutsa mʼdziko la Igupto.” 29 Fano lina analiyika ku Beteli ndipo lina analiyika ku Dani. 30 Ndipo zimenezi zinachimwitsa anthu pakuti anthu ankapita mpaka ku Dani kukapembedza fano limene linali kumeneko. 31 Yeroboamu anamanga Nyumba za Mulungu pa malo azipembedzo nasankha ansembe kuchokera pakati pa anthu wamba, ngakhale sanali Alevi. 32 Iye anakhazikitsa chikondwerero pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanana ndi tsiku la chikondwerero cha ku Yuda, ndipo ankapereka nsembe pa guwa. Izi ankachita ku Beteli, kupereka nsembe kwa ana angʼombe amene anapanga. Ndipo ku Beteliko anayikako ansembe pa malo achipembedzo amene anamanga. 33 Tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, mwezi umene anawusankha yekha, anapereka nsembe pa guwa limene analimanga ku Beteli. Motero anakhazikitsa chikondwerero cha Aisraeli ndipo iye ankapita kukapereka nsembe yofukiza lubani pa guwa.

In Other Versions

1 Kings 12 in the ANGEFD

1 Kings 12 in the ANTPNG2D

1 Kings 12 in the AS21

1 Kings 12 in the BAGH

1 Kings 12 in the BBPNG

1 Kings 12 in the BBT1E

1 Kings 12 in the BDS

1 Kings 12 in the BEV

1 Kings 12 in the BHAD

1 Kings 12 in the BIB

1 Kings 12 in the BLPT

1 Kings 12 in the BNT

1 Kings 12 in the BNTABOOT

1 Kings 12 in the BNTLV

1 Kings 12 in the BOATCB

1 Kings 12 in the BOATCB2

1 Kings 12 in the BOBCV

1 Kings 12 in the BOCNT

1 Kings 12 in the BOECS

1 Kings 12 in the BOHCB

1 Kings 12 in the BOHCV

1 Kings 12 in the BOHLNT

1 Kings 12 in the BOHNTLTAL

1 Kings 12 in the BOICB

1 Kings 12 in the BOILNTAP

1 Kings 12 in the BOITCV

1 Kings 12 in the BOKCV

1 Kings 12 in the BOKCV2

1 Kings 12 in the BOKHWOG

1 Kings 12 in the BOKSSV

1 Kings 12 in the BOLCB

1 Kings 12 in the BOLCB2

1 Kings 12 in the BOMCV

1 Kings 12 in the BONAV

1 Kings 12 in the BONCB

1 Kings 12 in the BONLT

1 Kings 12 in the BONUT2

1 Kings 12 in the BOPLNT

1 Kings 12 in the BOSCB

1 Kings 12 in the BOSNC

1 Kings 12 in the BOTLNT

1 Kings 12 in the BOVCB

1 Kings 12 in the BOYCB

1 Kings 12 in the BPBB

1 Kings 12 in the BPH

1 Kings 12 in the BSB

1 Kings 12 in the CCB

1 Kings 12 in the CUV

1 Kings 12 in the CUVS

1 Kings 12 in the DBT

1 Kings 12 in the DGDNT

1 Kings 12 in the DHNT

1 Kings 12 in the DNT

1 Kings 12 in the ELBE

1 Kings 12 in the EMTV

1 Kings 12 in the ESV

1 Kings 12 in the FBV

1 Kings 12 in the FEB

1 Kings 12 in the GGMNT

1 Kings 12 in the GNT

1 Kings 12 in the HARY

1 Kings 12 in the HNT

1 Kings 12 in the IRVA

1 Kings 12 in the IRVB

1 Kings 12 in the IRVG

1 Kings 12 in the IRVH

1 Kings 12 in the IRVK

1 Kings 12 in the IRVM

1 Kings 12 in the IRVM2

1 Kings 12 in the IRVO

1 Kings 12 in the IRVP

1 Kings 12 in the IRVT

1 Kings 12 in the IRVT2

1 Kings 12 in the IRVU

1 Kings 12 in the ISVN

1 Kings 12 in the JSNT

1 Kings 12 in the KAPI

1 Kings 12 in the KBT1ETNIK

1 Kings 12 in the KBV

1 Kings 12 in the KJV

1 Kings 12 in the KNFD

1 Kings 12 in the LBA

1 Kings 12 in the LBLA

1 Kings 12 in the LNT

1 Kings 12 in the LSV

1 Kings 12 in the MAAL

1 Kings 12 in the MBV

1 Kings 12 in the MBV2

1 Kings 12 in the MHNT

1 Kings 12 in the MKNFD

1 Kings 12 in the MNG

1 Kings 12 in the MNT

1 Kings 12 in the MNT2

1 Kings 12 in the MRS1T

1 Kings 12 in the NAA

1 Kings 12 in the NASB

1 Kings 12 in the NBLA

1 Kings 12 in the NBS

1 Kings 12 in the NBVTP

1 Kings 12 in the NET2

1 Kings 12 in the NIV11

1 Kings 12 in the NNT

1 Kings 12 in the NNT2

1 Kings 12 in the NNT3

1 Kings 12 in the PDDPT

1 Kings 12 in the PFNT

1 Kings 12 in the RMNT

1 Kings 12 in the SBIAS

1 Kings 12 in the SBIBS

1 Kings 12 in the SBIBS2

1 Kings 12 in the SBICS

1 Kings 12 in the SBIDS

1 Kings 12 in the SBIGS

1 Kings 12 in the SBIHS

1 Kings 12 in the SBIIS

1 Kings 12 in the SBIIS2

1 Kings 12 in the SBIIS3

1 Kings 12 in the SBIKS

1 Kings 12 in the SBIKS2

1 Kings 12 in the SBIMS

1 Kings 12 in the SBIOS

1 Kings 12 in the SBIPS

1 Kings 12 in the SBISS

1 Kings 12 in the SBITS

1 Kings 12 in the SBITS2

1 Kings 12 in the SBITS3

1 Kings 12 in the SBITS4

1 Kings 12 in the SBIUS

1 Kings 12 in the SBIVS

1 Kings 12 in the SBT

1 Kings 12 in the SBT1E

1 Kings 12 in the SCHL

1 Kings 12 in the SNT

1 Kings 12 in the SUSU

1 Kings 12 in the SUSU2

1 Kings 12 in the SYNO

1 Kings 12 in the TBIAOTANT

1 Kings 12 in the TBT1E

1 Kings 12 in the TBT1E2

1 Kings 12 in the TFTIP

1 Kings 12 in the TFTU

1 Kings 12 in the TGNTATF3T

1 Kings 12 in the THAI

1 Kings 12 in the TNFD

1 Kings 12 in the TNT

1 Kings 12 in the TNTIK

1 Kings 12 in the TNTIL

1 Kings 12 in the TNTIN

1 Kings 12 in the TNTIP

1 Kings 12 in the TNTIZ

1 Kings 12 in the TOMA

1 Kings 12 in the TTENT

1 Kings 12 in the UBG

1 Kings 12 in the UGV

1 Kings 12 in the UGV2

1 Kings 12 in the UGV3

1 Kings 12 in the VBL

1 Kings 12 in the VDCC

1 Kings 12 in the YALU

1 Kings 12 in the YAPE

1 Kings 12 in the YBVTP

1 Kings 12 in the ZBP