1 Samuel 27 (BOGWICC)
1 Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.” 2 Choncho Davide ndi anthu 600 amene anali nawo anachoka napita kwa Akisi mwana wa Maoki mfumu ya ku Gati. 3 Davide anakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi ankhondo ake, aliyense ndi banja lake. Davide ali ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wamasiye wa Nabala. 4 Sauli anamva kuti Davide wathawira ku Gati, ndipo sanamufunefunenso. 5 Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?” 6 Choncho tsiku limenelo Akisi anamupatsa Zikilagi ndipo mzindawo wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero. 7 Davide anakhala mʼdziko la Afilisti kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi. 8 Tsono Davide ndi anthu ake ankapita kukathira nkhondo Agesuri, Agirizi ndi Aamaleki. (Mitundu ya anthu imeneyi kuyambira kale inkakhala mʼdziko la pakati pa Suri ndi Igupto). 9 Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi. 10 Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.” 11 Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi wamoyo kuti akafotokozere anthu a ku Gati zochitikazo kuopa kuti opulumukawo akhoza kudzanena kuti “Davide watichita zakutizakuti.” Tsono izi ndi zimene Davide ankachita pamene ankakhala mʼdziko la Afilisti. 12 Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”
In Other Versions
1 Samuel 27 in the ANGEFD
1 Samuel 27 in the ANTPNG2D
1 Samuel 27 in the AS21
1 Samuel 27 in the BAGH
1 Samuel 27 in the BBPNG
1 Samuel 27 in the BBT1E
1 Samuel 27 in the BDS
1 Samuel 27 in the BEV
1 Samuel 27 in the BHAD
1 Samuel 27 in the BIB
1 Samuel 27 in the BLPT
1 Samuel 27 in the BNT
1 Samuel 27 in the BNTABOOT
1 Samuel 27 in the BNTLV
1 Samuel 27 in the BOATCB
1 Samuel 27 in the BOATCB2
1 Samuel 27 in the BOBCV
1 Samuel 27 in the BOCNT
1 Samuel 27 in the BOECS
1 Samuel 27 in the BOHCB
1 Samuel 27 in the BOHCV
1 Samuel 27 in the BOHLNT
1 Samuel 27 in the BOHNTLTAL
1 Samuel 27 in the BOICB
1 Samuel 27 in the BOILNTAP
1 Samuel 27 in the BOITCV
1 Samuel 27 in the BOKCV
1 Samuel 27 in the BOKCV2
1 Samuel 27 in the BOKHWOG
1 Samuel 27 in the BOKSSV
1 Samuel 27 in the BOLCB
1 Samuel 27 in the BOLCB2
1 Samuel 27 in the BOMCV
1 Samuel 27 in the BONAV
1 Samuel 27 in the BONCB
1 Samuel 27 in the BONLT
1 Samuel 27 in the BONUT2
1 Samuel 27 in the BOPLNT
1 Samuel 27 in the BOSCB
1 Samuel 27 in the BOSNC
1 Samuel 27 in the BOTLNT
1 Samuel 27 in the BOVCB
1 Samuel 27 in the BOYCB
1 Samuel 27 in the BPBB
1 Samuel 27 in the BPH
1 Samuel 27 in the BSB
1 Samuel 27 in the CCB
1 Samuel 27 in the CUV
1 Samuel 27 in the CUVS
1 Samuel 27 in the DBT
1 Samuel 27 in the DGDNT
1 Samuel 27 in the DHNT
1 Samuel 27 in the DNT
1 Samuel 27 in the ELBE
1 Samuel 27 in the EMTV
1 Samuel 27 in the ESV
1 Samuel 27 in the FBV
1 Samuel 27 in the FEB
1 Samuel 27 in the GGMNT
1 Samuel 27 in the GNT
1 Samuel 27 in the HARY
1 Samuel 27 in the HNT
1 Samuel 27 in the IRVA
1 Samuel 27 in the IRVB
1 Samuel 27 in the IRVG
1 Samuel 27 in the IRVH
1 Samuel 27 in the IRVK
1 Samuel 27 in the IRVM
1 Samuel 27 in the IRVM2
1 Samuel 27 in the IRVO
1 Samuel 27 in the IRVP
1 Samuel 27 in the IRVT
1 Samuel 27 in the IRVT2
1 Samuel 27 in the IRVU
1 Samuel 27 in the ISVN
1 Samuel 27 in the JSNT
1 Samuel 27 in the KAPI
1 Samuel 27 in the KBT1ETNIK
1 Samuel 27 in the KBV
1 Samuel 27 in the KJV
1 Samuel 27 in the KNFD
1 Samuel 27 in the LBA
1 Samuel 27 in the LBLA
1 Samuel 27 in the LNT
1 Samuel 27 in the LSV
1 Samuel 27 in the MAAL
1 Samuel 27 in the MBV
1 Samuel 27 in the MBV2
1 Samuel 27 in the MHNT
1 Samuel 27 in the MKNFD
1 Samuel 27 in the MNG
1 Samuel 27 in the MNT
1 Samuel 27 in the MNT2
1 Samuel 27 in the MRS1T
1 Samuel 27 in the NAA
1 Samuel 27 in the NASB
1 Samuel 27 in the NBLA
1 Samuel 27 in the NBS
1 Samuel 27 in the NBVTP
1 Samuel 27 in the NET2
1 Samuel 27 in the NIV11
1 Samuel 27 in the NNT
1 Samuel 27 in the NNT2
1 Samuel 27 in the NNT3
1 Samuel 27 in the PDDPT
1 Samuel 27 in the PFNT
1 Samuel 27 in the RMNT
1 Samuel 27 in the SBIAS
1 Samuel 27 in the SBIBS
1 Samuel 27 in the SBIBS2
1 Samuel 27 in the SBICS
1 Samuel 27 in the SBIDS
1 Samuel 27 in the SBIGS
1 Samuel 27 in the SBIHS
1 Samuel 27 in the SBIIS
1 Samuel 27 in the SBIIS2
1 Samuel 27 in the SBIIS3
1 Samuel 27 in the SBIKS
1 Samuel 27 in the SBIKS2
1 Samuel 27 in the SBIMS
1 Samuel 27 in the SBIOS
1 Samuel 27 in the SBIPS
1 Samuel 27 in the SBISS
1 Samuel 27 in the SBITS
1 Samuel 27 in the SBITS2
1 Samuel 27 in the SBITS3
1 Samuel 27 in the SBITS4
1 Samuel 27 in the SBIUS
1 Samuel 27 in the SBIVS
1 Samuel 27 in the SBT
1 Samuel 27 in the SBT1E
1 Samuel 27 in the SCHL
1 Samuel 27 in the SNT
1 Samuel 27 in the SUSU
1 Samuel 27 in the SUSU2
1 Samuel 27 in the SYNO
1 Samuel 27 in the TBIAOTANT
1 Samuel 27 in the TBT1E
1 Samuel 27 in the TBT1E2
1 Samuel 27 in the TFTIP
1 Samuel 27 in the TFTU
1 Samuel 27 in the TGNTATF3T
1 Samuel 27 in the THAI
1 Samuel 27 in the TNFD
1 Samuel 27 in the TNT
1 Samuel 27 in the TNTIK
1 Samuel 27 in the TNTIL
1 Samuel 27 in the TNTIN
1 Samuel 27 in the TNTIP
1 Samuel 27 in the TNTIZ
1 Samuel 27 in the TOMA
1 Samuel 27 in the TTENT
1 Samuel 27 in the UBG
1 Samuel 27 in the UGV
1 Samuel 27 in the UGV2
1 Samuel 27 in the UGV3
1 Samuel 27 in the VBL
1 Samuel 27 in the VDCC
1 Samuel 27 in the YALU
1 Samuel 27 in the YAPE
1 Samuel 27 in the YBVTP
1 Samuel 27 in the ZBP