2 Kings 2 (BOGWICC)

1 Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala. 2 Eliya anawuza Elisa kuti, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Beteli.”Koma Elisa anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Beteli. 3 Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.” 4 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.”Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko. 5 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.” 6 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.”Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo. 7 Anthu makumi asanu mwa ana a aneneri anawatsatira nayima chapatali moyangʼanana nawo ndipo Eliya ndi Elisa anayima mʼmphepete mwa Yorodani. 8 Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma. 9 Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.” 10 Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.” 11 Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. 12 Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati. 13 Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani. 14 Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka. 15 Ndipo ana a aneneri ochokera ku Yeriko atamuona anati, “Mzimu wa Eliya wakhazikika pa Elisa.” Ndipo anapita kukakumana naye nagwada ndi kuweramitsa mitu yawo pansi pamaso pake. 16 Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.”Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.” 17 Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze. 18 Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?” 19 Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.” 20 Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye. 21 Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ” 22 Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula. 23 Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi” 24 Iye anatembenuka nawayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Nthawi yomweyo panatulukira zimbalangondo ziwiri kuchokera kuthengo, ndi kuphapo anyamata 42. 25 Ndipo iye anapita ku phiri la Karimeli. Pochoka kumeneko anabwerera ku Samariya.

In Other Versions

2 Kings 2 in the ANGEFD

2 Kings 2 in the ANTPNG2D

2 Kings 2 in the AS21

2 Kings 2 in the BAGH

2 Kings 2 in the BBPNG

2 Kings 2 in the BBT1E

2 Kings 2 in the BDS

2 Kings 2 in the BEV

2 Kings 2 in the BHAD

2 Kings 2 in the BIB

2 Kings 2 in the BLPT

2 Kings 2 in the BNT

2 Kings 2 in the BNTABOOT

2 Kings 2 in the BNTLV

2 Kings 2 in the BOATCB

2 Kings 2 in the BOATCB2

2 Kings 2 in the BOBCV

2 Kings 2 in the BOCNT

2 Kings 2 in the BOECS

2 Kings 2 in the BOHCB

2 Kings 2 in the BOHCV

2 Kings 2 in the BOHLNT

2 Kings 2 in the BOHNTLTAL

2 Kings 2 in the BOICB

2 Kings 2 in the BOILNTAP

2 Kings 2 in the BOITCV

2 Kings 2 in the BOKCV

2 Kings 2 in the BOKCV2

2 Kings 2 in the BOKHWOG

2 Kings 2 in the BOKSSV

2 Kings 2 in the BOLCB

2 Kings 2 in the BOLCB2

2 Kings 2 in the BOMCV

2 Kings 2 in the BONAV

2 Kings 2 in the BONCB

2 Kings 2 in the BONLT

2 Kings 2 in the BONUT2

2 Kings 2 in the BOPLNT

2 Kings 2 in the BOSCB

2 Kings 2 in the BOSNC

2 Kings 2 in the BOTLNT

2 Kings 2 in the BOVCB

2 Kings 2 in the BOYCB

2 Kings 2 in the BPBB

2 Kings 2 in the BPH

2 Kings 2 in the BSB

2 Kings 2 in the CCB

2 Kings 2 in the CUV

2 Kings 2 in the CUVS

2 Kings 2 in the DBT

2 Kings 2 in the DGDNT

2 Kings 2 in the DHNT

2 Kings 2 in the DNT

2 Kings 2 in the ELBE

2 Kings 2 in the EMTV

2 Kings 2 in the ESV

2 Kings 2 in the FBV

2 Kings 2 in the FEB

2 Kings 2 in the GGMNT

2 Kings 2 in the GNT

2 Kings 2 in the HARY

2 Kings 2 in the HNT

2 Kings 2 in the IRVA

2 Kings 2 in the IRVB

2 Kings 2 in the IRVG

2 Kings 2 in the IRVH

2 Kings 2 in the IRVK

2 Kings 2 in the IRVM

2 Kings 2 in the IRVM2

2 Kings 2 in the IRVO

2 Kings 2 in the IRVP

2 Kings 2 in the IRVT

2 Kings 2 in the IRVT2

2 Kings 2 in the IRVU

2 Kings 2 in the ISVN

2 Kings 2 in the JSNT

2 Kings 2 in the KAPI

2 Kings 2 in the KBT1ETNIK

2 Kings 2 in the KBV

2 Kings 2 in the KJV

2 Kings 2 in the KNFD

2 Kings 2 in the LBA

2 Kings 2 in the LBLA

2 Kings 2 in the LNT

2 Kings 2 in the LSV

2 Kings 2 in the MAAL

2 Kings 2 in the MBV

2 Kings 2 in the MBV2

2 Kings 2 in the MHNT

2 Kings 2 in the MKNFD

2 Kings 2 in the MNG

2 Kings 2 in the MNT

2 Kings 2 in the MNT2

2 Kings 2 in the MRS1T

2 Kings 2 in the NAA

2 Kings 2 in the NASB

2 Kings 2 in the NBLA

2 Kings 2 in the NBS

2 Kings 2 in the NBVTP

2 Kings 2 in the NET2

2 Kings 2 in the NIV11

2 Kings 2 in the NNT

2 Kings 2 in the NNT2

2 Kings 2 in the NNT3

2 Kings 2 in the PDDPT

2 Kings 2 in the PFNT

2 Kings 2 in the RMNT

2 Kings 2 in the SBIAS

2 Kings 2 in the SBIBS

2 Kings 2 in the SBIBS2

2 Kings 2 in the SBICS

2 Kings 2 in the SBIDS

2 Kings 2 in the SBIGS

2 Kings 2 in the SBIHS

2 Kings 2 in the SBIIS

2 Kings 2 in the SBIIS2

2 Kings 2 in the SBIIS3

2 Kings 2 in the SBIKS

2 Kings 2 in the SBIKS2

2 Kings 2 in the SBIMS

2 Kings 2 in the SBIOS

2 Kings 2 in the SBIPS

2 Kings 2 in the SBISS

2 Kings 2 in the SBITS

2 Kings 2 in the SBITS2

2 Kings 2 in the SBITS3

2 Kings 2 in the SBITS4

2 Kings 2 in the SBIUS

2 Kings 2 in the SBIVS

2 Kings 2 in the SBT

2 Kings 2 in the SBT1E

2 Kings 2 in the SCHL

2 Kings 2 in the SNT

2 Kings 2 in the SUSU

2 Kings 2 in the SUSU2

2 Kings 2 in the SYNO

2 Kings 2 in the TBIAOTANT

2 Kings 2 in the TBT1E

2 Kings 2 in the TBT1E2

2 Kings 2 in the TFTIP

2 Kings 2 in the TFTU

2 Kings 2 in the TGNTATF3T

2 Kings 2 in the THAI

2 Kings 2 in the TNFD

2 Kings 2 in the TNT

2 Kings 2 in the TNTIK

2 Kings 2 in the TNTIL

2 Kings 2 in the TNTIN

2 Kings 2 in the TNTIP

2 Kings 2 in the TNTIZ

2 Kings 2 in the TOMA

2 Kings 2 in the TTENT

2 Kings 2 in the UBG

2 Kings 2 in the UGV

2 Kings 2 in the UGV2

2 Kings 2 in the UGV3

2 Kings 2 in the VBL

2 Kings 2 in the VDCC

2 Kings 2 in the YALU

2 Kings 2 in the YAPE

2 Kings 2 in the YBVTP

2 Kings 2 in the ZBP