2 Samuel 17 (BOGWICC)

1 Ahitofele anati kwa Abisalomu, “Mundilole ndisankhe asilikali 12,000, ndinyamuke usiku womwe uno kuti ndithamangire Davide. 2 Ndipo ndikamuthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima. Ndikamuchititsa mantha ndipo anthu onse amene ali naye akathawa. Ine ndikakantha mfumu yokhayo, 3 ndipo anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” 4 Malangizo awa anaoneka abwino kwa Abisalomu ndi kwa akuluakulu onse a Israeli. 5 Koma Abisalomu anati, “Muyitanenso Husai Mwariki kuti timve zimene iye adzanena.” 6 Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.” 7 Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino. 8 Inu mukudziwa bwino abambo anu ali ndi ankhondo awo. Iwo ndi anthu ankhondo komanso ndi woopsa ngati chimbalangondo chimene chalandidwa ana ake. Kuwonjezera apa abambo anu ndi katswiri wa nkhondo. Iwo sanagone pamodzi ndi asilikali awo. 9 Onani, ngakhale tsopano lino abisala mʼphanga lina ku malo ena ake. Ngati iwo atayamba kuthira nkhondo asilikali anu, aliyense amene adzamve zimenezi adzati, ‘Gulu lalikulu lankhondo lotsatira Abisalomu laphedwa.’ 10 Tsono ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri, amene mtima wake uli ngati wa mkango, adzagwidwa ndi mantha aakulu pakuti Aisraeli akudziwa kuti abambo anu ndi ankhondo ndipo kuti iwo amene ali nawo ndi anthu olimba mtima. 11 “Kotero ine ndikukulangizani kuti: Aisraeli onse, kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba; ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja, asonkhane kwa inu ndipo muwatsogolera kupita ku nkhondo. 12 Ndipo ife tidzapita kukamuthira nkhondo kulikonse kumene tikamupeze, ndipo ife tikamuthira nkhondo ngati mame pa nthaka. Palibe amene adzakhale wamoyo kaya iye kapena ankhondo ake. 13 Iye akakathawira mu mzinda, Aisraeli onse adzabweretsa zingwe ku mzindawo, ndipo ife tidzawugwetsera ku chigwa mpaka sipadzapezeka ngakhale kachidutswa.” 14 Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu. 15 Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti. 16 Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ” 17 Yonatani ndi Ahimaazi amakhala ku Eni Rogeli. Tsono wantchito wamkazi ndiye amapita kukawawuza ndipo iwo amayenera kupita kukamuwuza mfumu Davide, pakuti iwowo sankayenera kuonekera polowa mu mzinda. 18 Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo. 19 Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi. 20 Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?”Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu. 21 Anthu aja atapita, awiriwo anatuluka mʼchitsimemo ndipo anapita kukawuza mfumu Davide nati kwa iye, “Nyamukani, muwoloke mtsinje msangamsanga. Ahitofele wapereka malangizo akutiakuti kutsutsana nanu.” 22 Kotero Davide ndi anthu onse amene anali nawo ananyamuka ndi kuwoloka Yorodani. Pofika mmamawa, panalibe munthu amene anatsala asanawoloke Yorodani! 23 Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake. 24 Davide anapita ku Mahanaimu, ndipo Abisalomu anawoloka Yorodani pamodzi ndi ankhondo ena onse a Israeli. 25 Abisalomu anasankha Amasa kukhala mkulu wa ankhondo mʼmalo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wotchedwa Itira Mwisraeli amene anakwatira Abigayeli mwana wa Nahasi mlongo wake wa Zeruya, amayi ake a Yowabu. 26 Aisraeli ndi Abisalomu anamanga zithando mʼdziko la Giliyadi. 27 Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wochokera ku Raba ku dziko la Amoni ndi Makiri mwana wa Amieli wochokera ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu 28 anabweretsa zofunda, mabeseni ndi miphika. Iwo anabweretsanso kwa Davide ndi anthu ake zakudya izi: tirigu ndi barele, ufa ndi tirigu wokazinga, nyemba ndi mphodza, 29 uchi ndi chambiko, nkhosa ndi mafuta olimba a mkaka wangʼombe. Pakuti anati, “Anthuwa ali ndi njala ndipo atopa, alinso ndi ludzu muno mʼchipululu.”

In Other Versions

2 Samuel 17 in the ANGEFD

2 Samuel 17 in the ANTPNG2D

2 Samuel 17 in the AS21

2 Samuel 17 in the BAGH

2 Samuel 17 in the BBPNG

2 Samuel 17 in the BBT1E

2 Samuel 17 in the BDS

2 Samuel 17 in the BEV

2 Samuel 17 in the BHAD

2 Samuel 17 in the BIB

2 Samuel 17 in the BLPT

2 Samuel 17 in the BNT

2 Samuel 17 in the BNTABOOT

2 Samuel 17 in the BNTLV

2 Samuel 17 in the BOATCB

2 Samuel 17 in the BOATCB2

2 Samuel 17 in the BOBCV

2 Samuel 17 in the BOCNT

2 Samuel 17 in the BOECS

2 Samuel 17 in the BOHCB

2 Samuel 17 in the BOHCV

2 Samuel 17 in the BOHLNT

2 Samuel 17 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 17 in the BOICB

2 Samuel 17 in the BOILNTAP

2 Samuel 17 in the BOITCV

2 Samuel 17 in the BOKCV

2 Samuel 17 in the BOKCV2

2 Samuel 17 in the BOKHWOG

2 Samuel 17 in the BOKSSV

2 Samuel 17 in the BOLCB

2 Samuel 17 in the BOLCB2

2 Samuel 17 in the BOMCV

2 Samuel 17 in the BONAV

2 Samuel 17 in the BONCB

2 Samuel 17 in the BONLT

2 Samuel 17 in the BONUT2

2 Samuel 17 in the BOPLNT

2 Samuel 17 in the BOSCB

2 Samuel 17 in the BOSNC

2 Samuel 17 in the BOTLNT

2 Samuel 17 in the BOVCB

2 Samuel 17 in the BOYCB

2 Samuel 17 in the BPBB

2 Samuel 17 in the BPH

2 Samuel 17 in the BSB

2 Samuel 17 in the CCB

2 Samuel 17 in the CUV

2 Samuel 17 in the CUVS

2 Samuel 17 in the DBT

2 Samuel 17 in the DGDNT

2 Samuel 17 in the DHNT

2 Samuel 17 in the DNT

2 Samuel 17 in the ELBE

2 Samuel 17 in the EMTV

2 Samuel 17 in the ESV

2 Samuel 17 in the FBV

2 Samuel 17 in the FEB

2 Samuel 17 in the GGMNT

2 Samuel 17 in the GNT

2 Samuel 17 in the HARY

2 Samuel 17 in the HNT

2 Samuel 17 in the IRVA

2 Samuel 17 in the IRVB

2 Samuel 17 in the IRVG

2 Samuel 17 in the IRVH

2 Samuel 17 in the IRVK

2 Samuel 17 in the IRVM

2 Samuel 17 in the IRVM2

2 Samuel 17 in the IRVO

2 Samuel 17 in the IRVP

2 Samuel 17 in the IRVT

2 Samuel 17 in the IRVT2

2 Samuel 17 in the IRVU

2 Samuel 17 in the ISVN

2 Samuel 17 in the JSNT

2 Samuel 17 in the KAPI

2 Samuel 17 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 17 in the KBV

2 Samuel 17 in the KJV

2 Samuel 17 in the KNFD

2 Samuel 17 in the LBA

2 Samuel 17 in the LBLA

2 Samuel 17 in the LNT

2 Samuel 17 in the LSV

2 Samuel 17 in the MAAL

2 Samuel 17 in the MBV

2 Samuel 17 in the MBV2

2 Samuel 17 in the MHNT

2 Samuel 17 in the MKNFD

2 Samuel 17 in the MNG

2 Samuel 17 in the MNT

2 Samuel 17 in the MNT2

2 Samuel 17 in the MRS1T

2 Samuel 17 in the NAA

2 Samuel 17 in the NASB

2 Samuel 17 in the NBLA

2 Samuel 17 in the NBS

2 Samuel 17 in the NBVTP

2 Samuel 17 in the NET2

2 Samuel 17 in the NIV11

2 Samuel 17 in the NNT

2 Samuel 17 in the NNT2

2 Samuel 17 in the NNT3

2 Samuel 17 in the PDDPT

2 Samuel 17 in the PFNT

2 Samuel 17 in the RMNT

2 Samuel 17 in the SBIAS

2 Samuel 17 in the SBIBS

2 Samuel 17 in the SBIBS2

2 Samuel 17 in the SBICS

2 Samuel 17 in the SBIDS

2 Samuel 17 in the SBIGS

2 Samuel 17 in the SBIHS

2 Samuel 17 in the SBIIS

2 Samuel 17 in the SBIIS2

2 Samuel 17 in the SBIIS3

2 Samuel 17 in the SBIKS

2 Samuel 17 in the SBIKS2

2 Samuel 17 in the SBIMS

2 Samuel 17 in the SBIOS

2 Samuel 17 in the SBIPS

2 Samuel 17 in the SBISS

2 Samuel 17 in the SBITS

2 Samuel 17 in the SBITS2

2 Samuel 17 in the SBITS3

2 Samuel 17 in the SBITS4

2 Samuel 17 in the SBIUS

2 Samuel 17 in the SBIVS

2 Samuel 17 in the SBT

2 Samuel 17 in the SBT1E

2 Samuel 17 in the SCHL

2 Samuel 17 in the SNT

2 Samuel 17 in the SUSU

2 Samuel 17 in the SUSU2

2 Samuel 17 in the SYNO

2 Samuel 17 in the TBIAOTANT

2 Samuel 17 in the TBT1E

2 Samuel 17 in the TBT1E2

2 Samuel 17 in the TFTIP

2 Samuel 17 in the TFTU

2 Samuel 17 in the TGNTATF3T

2 Samuel 17 in the THAI

2 Samuel 17 in the TNFD

2 Samuel 17 in the TNT

2 Samuel 17 in the TNTIK

2 Samuel 17 in the TNTIL

2 Samuel 17 in the TNTIN

2 Samuel 17 in the TNTIP

2 Samuel 17 in the TNTIZ

2 Samuel 17 in the TOMA

2 Samuel 17 in the TTENT

2 Samuel 17 in the UBG

2 Samuel 17 in the UGV

2 Samuel 17 in the UGV2

2 Samuel 17 in the UGV3

2 Samuel 17 in the VBL

2 Samuel 17 in the VDCC

2 Samuel 17 in the YALU

2 Samuel 17 in the YAPE

2 Samuel 17 in the YBVTP

2 Samuel 17 in the ZBP