Daniel 2 (BOGWICC)

1 Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona. 2 Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, 3 mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.” 4 Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.” 5 Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja. 6 Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.” 7 Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.” 8 Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita. 9 Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.” 10 Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. 11 Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.” 12 Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe. 13 Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe. 14 Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni. 15 Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli. 16 Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake. 17 Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 18 Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni. 19 Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba, 20 ndipo anati:“Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi;nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake. 21 Amasintha nthawi ndi nyengo;amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso.Amapatsa nzeru kwa anzerundi chidziwitso kwa ozindikira zinthu. 22 Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika;amadziwa zimene zili mu mdima,ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye. 23 Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga:mwandipatsa nzeru ndi mphamvu,mwandiwululira zomwe tinakupemphani,mwatiwululira maloto a mfumu.” 24 Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.” 25 Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.” 26 Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?” 27 Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, 28 koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa: 29 “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. 30 Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu. 31 “Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe. 32 Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa. 33 Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo. 34 Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya. 35 Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi. 36 “Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. 37 Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero; 38 Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo. 39 “Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. 40 Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. 41 Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. 42 Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka. 43 Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo. 44 “Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya. 45 Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa.“Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.” 46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani. 47 Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.” 48 Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru. 49 Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.

In Other Versions

Daniel 2 in the ANGEFD

Daniel 2 in the ANTPNG2D

Daniel 2 in the AS21

Daniel 2 in the BAGH

Daniel 2 in the BBPNG

Daniel 2 in the BBT1E

Daniel 2 in the BDS

Daniel 2 in the BEV

Daniel 2 in the BHAD

Daniel 2 in the BIB

Daniel 2 in the BLPT

Daniel 2 in the BNT

Daniel 2 in the BNTABOOT

Daniel 2 in the BNTLV

Daniel 2 in the BOATCB

Daniel 2 in the BOATCB2

Daniel 2 in the BOBCV

Daniel 2 in the BOCNT

Daniel 2 in the BOECS

Daniel 2 in the BOHCB

Daniel 2 in the BOHCV

Daniel 2 in the BOHLNT

Daniel 2 in the BOHNTLTAL

Daniel 2 in the BOICB

Daniel 2 in the BOILNTAP

Daniel 2 in the BOITCV

Daniel 2 in the BOKCV

Daniel 2 in the BOKCV2

Daniel 2 in the BOKHWOG

Daniel 2 in the BOKSSV

Daniel 2 in the BOLCB

Daniel 2 in the BOLCB2

Daniel 2 in the BOMCV

Daniel 2 in the BONAV

Daniel 2 in the BONCB

Daniel 2 in the BONLT

Daniel 2 in the BONUT2

Daniel 2 in the BOPLNT

Daniel 2 in the BOSCB

Daniel 2 in the BOSNC

Daniel 2 in the BOTLNT

Daniel 2 in the BOVCB

Daniel 2 in the BOYCB

Daniel 2 in the BPBB

Daniel 2 in the BPH

Daniel 2 in the BSB

Daniel 2 in the CCB

Daniel 2 in the CUV

Daniel 2 in the CUVS

Daniel 2 in the DBT

Daniel 2 in the DGDNT

Daniel 2 in the DHNT

Daniel 2 in the DNT

Daniel 2 in the ELBE

Daniel 2 in the EMTV

Daniel 2 in the ESV

Daniel 2 in the FBV

Daniel 2 in the FEB

Daniel 2 in the GGMNT

Daniel 2 in the GNT

Daniel 2 in the HARY

Daniel 2 in the HNT

Daniel 2 in the IRVA

Daniel 2 in the IRVB

Daniel 2 in the IRVG

Daniel 2 in the IRVH

Daniel 2 in the IRVK

Daniel 2 in the IRVM

Daniel 2 in the IRVM2

Daniel 2 in the IRVO

Daniel 2 in the IRVP

Daniel 2 in the IRVT

Daniel 2 in the IRVT2

Daniel 2 in the IRVU

Daniel 2 in the ISVN

Daniel 2 in the JSNT

Daniel 2 in the KAPI

Daniel 2 in the KBT1ETNIK

Daniel 2 in the KBV

Daniel 2 in the KJV

Daniel 2 in the KNFD

Daniel 2 in the LBA

Daniel 2 in the LBLA

Daniel 2 in the LNT

Daniel 2 in the LSV

Daniel 2 in the MAAL

Daniel 2 in the MBV

Daniel 2 in the MBV2

Daniel 2 in the MHNT

Daniel 2 in the MKNFD

Daniel 2 in the MNG

Daniel 2 in the MNT

Daniel 2 in the MNT2

Daniel 2 in the MRS1T

Daniel 2 in the NAA

Daniel 2 in the NASB

Daniel 2 in the NBLA

Daniel 2 in the NBS

Daniel 2 in the NBVTP

Daniel 2 in the NET2

Daniel 2 in the NIV11

Daniel 2 in the NNT

Daniel 2 in the NNT2

Daniel 2 in the NNT3

Daniel 2 in the PDDPT

Daniel 2 in the PFNT

Daniel 2 in the RMNT

Daniel 2 in the SBIAS

Daniel 2 in the SBIBS

Daniel 2 in the SBIBS2

Daniel 2 in the SBICS

Daniel 2 in the SBIDS

Daniel 2 in the SBIGS

Daniel 2 in the SBIHS

Daniel 2 in the SBIIS

Daniel 2 in the SBIIS2

Daniel 2 in the SBIIS3

Daniel 2 in the SBIKS

Daniel 2 in the SBIKS2

Daniel 2 in the SBIMS

Daniel 2 in the SBIOS

Daniel 2 in the SBIPS

Daniel 2 in the SBISS

Daniel 2 in the SBITS

Daniel 2 in the SBITS2

Daniel 2 in the SBITS3

Daniel 2 in the SBITS4

Daniel 2 in the SBIUS

Daniel 2 in the SBIVS

Daniel 2 in the SBT

Daniel 2 in the SBT1E

Daniel 2 in the SCHL

Daniel 2 in the SNT

Daniel 2 in the SUSU

Daniel 2 in the SUSU2

Daniel 2 in the SYNO

Daniel 2 in the TBIAOTANT

Daniel 2 in the TBT1E

Daniel 2 in the TBT1E2

Daniel 2 in the TFTIP

Daniel 2 in the TFTU

Daniel 2 in the TGNTATF3T

Daniel 2 in the THAI

Daniel 2 in the TNFD

Daniel 2 in the TNT

Daniel 2 in the TNTIK

Daniel 2 in the TNTIL

Daniel 2 in the TNTIN

Daniel 2 in the TNTIP

Daniel 2 in the TNTIZ

Daniel 2 in the TOMA

Daniel 2 in the TTENT

Daniel 2 in the UBG

Daniel 2 in the UGV

Daniel 2 in the UGV2

Daniel 2 in the UGV3

Daniel 2 in the VBL

Daniel 2 in the VDCC

Daniel 2 in the YALU

Daniel 2 in the YAPE

Daniel 2 in the YBVTP

Daniel 2 in the ZBP