Exodus 32 (BOGWICC)

1 Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.” 2 Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” 3 Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. 4 Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.” 5 Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.” 6 Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo. 7 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri. 8 Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” 9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndikuwadziwa anthu amenewa. Iwowa ndi ankhutukumve. 10 Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.” 11 Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. 12 Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. 13 Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ” 14 Choncho Yehova analeka ndipo sanawachitire choyipa anthu ake monga anaopsezera. 15 Mose anatembenuka ndi kutsika phiri miyala iwiri ya pangano ili mʼmanja mwake. Miyalayi inalembedwa mbali zonse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. 16 Miyalayi anayikonza ndi Mulungu. Malembawo analemba ndi Mulungu mozokota pa miyalapo. 17 Pamene Yoswa anamva phokoso la anthu anati kwa Mose, “Ku msasa kuli phokoso la nkhondo.” 18 Mose anayankha kuti,“Phokoso limeneli sindikulimvangati phokoso la opambana nkhondo,kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.” 19 Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri. 20 Ndipo iye anatenga mwana wangʼombe amene anthu anapanga uja ndi kumuwotcha pa moto ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi. Kenaka anawaza fumbilo mʼmadzi ndi kuwamwetsa Aisraeli madziwo. 21 Tsono Mose anafunsa Aaroni kuti, “Kodi anthu awa anakuchita chiyani kuti uwachimwitse koopsa chotere?” 22 Aaroni anayankha kuti, “Musakwiye mbuye wanga. Inu mukudziwa kuti anthu awa ndi ovuta. 23 Iwo anati kwa ine, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’ 24 Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.” 25 Mose anaona kuti anthuwo anali osokonezekadi chifukwa Aaroni anawalekerera mpaka kusanduka anthu osekedwa pakati pa adani awo. 26 Choncho iye anayima pa chipata cholowera mu msasa ndipo anati, “Aliyense amene ali mbali ya Yehova abwere kwa ine.” Ndipo Alevi onse anapita mbali yake. 27 Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ” 28 Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000. 29 Kenaka Mose anati, “Lero mwadzipatula nokha kukhala ansembe otumikira Yehova. Mwachita izi popeza aliyense wa inu wapha mwana wake kapena mʼbale wake. Tsono lero Yehova wakudalitsani.” 30 Mmawa mwake Mose anati kwa anthu onse, “Inu mwachita tchimo lalikulu. Koma tsopano ine ndipita ku phiri kwa Yehova mwina ndikatha kukupepeserani chifukwa cha tchimo lanu.” 31 Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide. 32 Koma tsopano, chonde akhululukireni tchimo lawo. Ngati simutero, ndiye mundifute ine mʼbuku limene mwalemba.” 33 Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira. 34 Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.” 35 Ndipo Yehova anawakantha anthuwo ndi mliri chifukwa anawumiriza Aaroni kuti awapangire fano la mwana wangʼombe.

In Other Versions

Exodus 32 in the ANGEFD

Exodus 32 in the ANTPNG2D

Exodus 32 in the AS21

Exodus 32 in the BAGH

Exodus 32 in the BBPNG

Exodus 32 in the BBT1E

Exodus 32 in the BDS

Exodus 32 in the BEV

Exodus 32 in the BHAD

Exodus 32 in the BIB

Exodus 32 in the BLPT

Exodus 32 in the BNT

Exodus 32 in the BNTABOOT

Exodus 32 in the BNTLV

Exodus 32 in the BOATCB

Exodus 32 in the BOATCB2

Exodus 32 in the BOBCV

Exodus 32 in the BOCNT

Exodus 32 in the BOECS

Exodus 32 in the BOHCB

Exodus 32 in the BOHCV

Exodus 32 in the BOHLNT

Exodus 32 in the BOHNTLTAL

Exodus 32 in the BOICB

Exodus 32 in the BOILNTAP

Exodus 32 in the BOITCV

Exodus 32 in the BOKCV

Exodus 32 in the BOKCV2

Exodus 32 in the BOKHWOG

Exodus 32 in the BOKSSV

Exodus 32 in the BOLCB

Exodus 32 in the BOLCB2

Exodus 32 in the BOMCV

Exodus 32 in the BONAV

Exodus 32 in the BONCB

Exodus 32 in the BONLT

Exodus 32 in the BONUT2

Exodus 32 in the BOPLNT

Exodus 32 in the BOSCB

Exodus 32 in the BOSNC

Exodus 32 in the BOTLNT

Exodus 32 in the BOVCB

Exodus 32 in the BOYCB

Exodus 32 in the BPBB

Exodus 32 in the BPH

Exodus 32 in the BSB

Exodus 32 in the CCB

Exodus 32 in the CUV

Exodus 32 in the CUVS

Exodus 32 in the DBT

Exodus 32 in the DGDNT

Exodus 32 in the DHNT

Exodus 32 in the DNT

Exodus 32 in the ELBE

Exodus 32 in the EMTV

Exodus 32 in the ESV

Exodus 32 in the FBV

Exodus 32 in the FEB

Exodus 32 in the GGMNT

Exodus 32 in the GNT

Exodus 32 in the HARY

Exodus 32 in the HNT

Exodus 32 in the IRVA

Exodus 32 in the IRVB

Exodus 32 in the IRVG

Exodus 32 in the IRVH

Exodus 32 in the IRVK

Exodus 32 in the IRVM

Exodus 32 in the IRVM2

Exodus 32 in the IRVO

Exodus 32 in the IRVP

Exodus 32 in the IRVT

Exodus 32 in the IRVT2

Exodus 32 in the IRVU

Exodus 32 in the ISVN

Exodus 32 in the JSNT

Exodus 32 in the KAPI

Exodus 32 in the KBT1ETNIK

Exodus 32 in the KBV

Exodus 32 in the KJV

Exodus 32 in the KNFD

Exodus 32 in the LBA

Exodus 32 in the LBLA

Exodus 32 in the LNT

Exodus 32 in the LSV

Exodus 32 in the MAAL

Exodus 32 in the MBV

Exodus 32 in the MBV2

Exodus 32 in the MHNT

Exodus 32 in the MKNFD

Exodus 32 in the MNG

Exodus 32 in the MNT

Exodus 32 in the MNT2

Exodus 32 in the MRS1T

Exodus 32 in the NAA

Exodus 32 in the NASB

Exodus 32 in the NBLA

Exodus 32 in the NBS

Exodus 32 in the NBVTP

Exodus 32 in the NET2

Exodus 32 in the NIV11

Exodus 32 in the NNT

Exodus 32 in the NNT2

Exodus 32 in the NNT3

Exodus 32 in the PDDPT

Exodus 32 in the PFNT

Exodus 32 in the RMNT

Exodus 32 in the SBIAS

Exodus 32 in the SBIBS

Exodus 32 in the SBIBS2

Exodus 32 in the SBICS

Exodus 32 in the SBIDS

Exodus 32 in the SBIGS

Exodus 32 in the SBIHS

Exodus 32 in the SBIIS

Exodus 32 in the SBIIS2

Exodus 32 in the SBIIS3

Exodus 32 in the SBIKS

Exodus 32 in the SBIKS2

Exodus 32 in the SBIMS

Exodus 32 in the SBIOS

Exodus 32 in the SBIPS

Exodus 32 in the SBISS

Exodus 32 in the SBITS

Exodus 32 in the SBITS2

Exodus 32 in the SBITS3

Exodus 32 in the SBITS4

Exodus 32 in the SBIUS

Exodus 32 in the SBIVS

Exodus 32 in the SBT

Exodus 32 in the SBT1E

Exodus 32 in the SCHL

Exodus 32 in the SNT

Exodus 32 in the SUSU

Exodus 32 in the SUSU2

Exodus 32 in the SYNO

Exodus 32 in the TBIAOTANT

Exodus 32 in the TBT1E

Exodus 32 in the TBT1E2

Exodus 32 in the TFTIP

Exodus 32 in the TFTU

Exodus 32 in the TGNTATF3T

Exodus 32 in the THAI

Exodus 32 in the TNFD

Exodus 32 in the TNT

Exodus 32 in the TNTIK

Exodus 32 in the TNTIL

Exodus 32 in the TNTIN

Exodus 32 in the TNTIP

Exodus 32 in the TNTIZ

Exodus 32 in the TOMA

Exodus 32 in the TTENT

Exodus 32 in the UBG

Exodus 32 in the UGV

Exodus 32 in the UGV2

Exodus 32 in the UGV3

Exodus 32 in the VBL

Exodus 32 in the VDCC

Exodus 32 in the YALU

Exodus 32 in the YAPE

Exodus 32 in the YBVTP

Exodus 32 in the ZBP