Exodus 9 (BOGWICC)

1 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao ndipo ukamuwuze kuti Yehova, Mulungu wa Ahebri akuti alole anthu anga apite kuti akandipembedze. 2 Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, 3 dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri. 4 Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.” 5 Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.” 6 Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. 7 Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite. 8 Kenaka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Tapani phulusa la pa moto lodzaza dzanja ndipo Mose aliwaze mmwamba pamaso pa Farao. 9 Phulusalo lidzasanduka fumbi pa dziko lonse la Igupto. Tsono fumbilo lidzasanduka zithupsa zomaphulika nʼkukhala zilonda pa munthu aliyense ndi pa nyama zomwe mʼdziko lonse la Igupto.” 10 Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto. 11 Amatsenga sanathe kumuyandikira Mose chifukwa nawonso anali ndi zithupsa monga mmene analili Aigupto ena onse. 12 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose. 13 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze. 14 Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi. 15 Pakuti ndikanakhala nditatukula kale dzanja langa ndikupheratu iwe pamodzi ndi anthu ako onse pa dziko lapansi. 16 Koma ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga kwa iwe ndiponso kuti dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi. 17 Komabe iwe ukudzitukumula pa anthu anga osawalola kuti atuluke. 18 Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero. 19 Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.” 20 Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba. 21 Koma iwo amene ananyozera mawu a Yehova anasiya akapolo ndi ziweto zawo panja. 22 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti matalala agwe pa dziko lonse la Igupto, pa munthu aliyense, pa ziweto ndi pa zonse zomera mʼminda ya Igupto.” 23 Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. 24 Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha. 25 Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse. 26 Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli. 27 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 Upemphere kwa Mulungu chifukwa mabingu ndi matalala atikwana. Ine ndidzakulolani kuti mupite. Simuyenera kukhalabe kuno.” 29 Mose anayankha, “Ndikangotuluka mu mzinda muno, ine ndidzakweza manja anga kwa Yehova ndi kupemphera. Mabingu ndi matalalawa adzaleka ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova ndiye akulamulira dziko lapansi. 30 Koma ine ndikudziwa kuti inu ndi nduna zanu simukuopabe Yehova Mulungu.” 31 Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa. 32 Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa. 33 Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo. 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zaleka, anachimwanso. Iye ndi nduna zake anawumitsanso mitima yawo. 35 Choncho Farao sanalole kuti Aisraeli apite monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.

In Other Versions

Exodus 9 in the ANGEFD

Exodus 9 in the ANTPNG2D

Exodus 9 in the AS21

Exodus 9 in the BAGH

Exodus 9 in the BBPNG

Exodus 9 in the BBT1E

Exodus 9 in the BDS

Exodus 9 in the BEV

Exodus 9 in the BHAD

Exodus 9 in the BIB

Exodus 9 in the BLPT

Exodus 9 in the BNT

Exodus 9 in the BNTABOOT

Exodus 9 in the BNTLV

Exodus 9 in the BOATCB

Exodus 9 in the BOATCB2

Exodus 9 in the BOBCV

Exodus 9 in the BOCNT

Exodus 9 in the BOECS

Exodus 9 in the BOHCB

Exodus 9 in the BOHCV

Exodus 9 in the BOHLNT

Exodus 9 in the BOHNTLTAL

Exodus 9 in the BOICB

Exodus 9 in the BOILNTAP

Exodus 9 in the BOITCV

Exodus 9 in the BOKCV

Exodus 9 in the BOKCV2

Exodus 9 in the BOKHWOG

Exodus 9 in the BOKSSV

Exodus 9 in the BOLCB

Exodus 9 in the BOLCB2

Exodus 9 in the BOMCV

Exodus 9 in the BONAV

Exodus 9 in the BONCB

Exodus 9 in the BONLT

Exodus 9 in the BONUT2

Exodus 9 in the BOPLNT

Exodus 9 in the BOSCB

Exodus 9 in the BOSNC

Exodus 9 in the BOTLNT

Exodus 9 in the BOVCB

Exodus 9 in the BOYCB

Exodus 9 in the BPBB

Exodus 9 in the BPH

Exodus 9 in the BSB

Exodus 9 in the CCB

Exodus 9 in the CUV

Exodus 9 in the CUVS

Exodus 9 in the DBT

Exodus 9 in the DGDNT

Exodus 9 in the DHNT

Exodus 9 in the DNT

Exodus 9 in the ELBE

Exodus 9 in the EMTV

Exodus 9 in the ESV

Exodus 9 in the FBV

Exodus 9 in the FEB

Exodus 9 in the GGMNT

Exodus 9 in the GNT

Exodus 9 in the HARY

Exodus 9 in the HNT

Exodus 9 in the IRVA

Exodus 9 in the IRVB

Exodus 9 in the IRVG

Exodus 9 in the IRVH

Exodus 9 in the IRVK

Exodus 9 in the IRVM

Exodus 9 in the IRVM2

Exodus 9 in the IRVO

Exodus 9 in the IRVP

Exodus 9 in the IRVT

Exodus 9 in the IRVT2

Exodus 9 in the IRVU

Exodus 9 in the ISVN

Exodus 9 in the JSNT

Exodus 9 in the KAPI

Exodus 9 in the KBT1ETNIK

Exodus 9 in the KBV

Exodus 9 in the KJV

Exodus 9 in the KNFD

Exodus 9 in the LBA

Exodus 9 in the LBLA

Exodus 9 in the LNT

Exodus 9 in the LSV

Exodus 9 in the MAAL

Exodus 9 in the MBV

Exodus 9 in the MBV2

Exodus 9 in the MHNT

Exodus 9 in the MKNFD

Exodus 9 in the MNG

Exodus 9 in the MNT

Exodus 9 in the MNT2

Exodus 9 in the MRS1T

Exodus 9 in the NAA

Exodus 9 in the NASB

Exodus 9 in the NBLA

Exodus 9 in the NBS

Exodus 9 in the NBVTP

Exodus 9 in the NET2

Exodus 9 in the NIV11

Exodus 9 in the NNT

Exodus 9 in the NNT2

Exodus 9 in the NNT3

Exodus 9 in the PDDPT

Exodus 9 in the PFNT

Exodus 9 in the RMNT

Exodus 9 in the SBIAS

Exodus 9 in the SBIBS

Exodus 9 in the SBIBS2

Exodus 9 in the SBICS

Exodus 9 in the SBIDS

Exodus 9 in the SBIGS

Exodus 9 in the SBIHS

Exodus 9 in the SBIIS

Exodus 9 in the SBIIS2

Exodus 9 in the SBIIS3

Exodus 9 in the SBIKS

Exodus 9 in the SBIKS2

Exodus 9 in the SBIMS

Exodus 9 in the SBIOS

Exodus 9 in the SBIPS

Exodus 9 in the SBISS

Exodus 9 in the SBITS

Exodus 9 in the SBITS2

Exodus 9 in the SBITS3

Exodus 9 in the SBITS4

Exodus 9 in the SBIUS

Exodus 9 in the SBIVS

Exodus 9 in the SBT

Exodus 9 in the SBT1E

Exodus 9 in the SCHL

Exodus 9 in the SNT

Exodus 9 in the SUSU

Exodus 9 in the SUSU2

Exodus 9 in the SYNO

Exodus 9 in the TBIAOTANT

Exodus 9 in the TBT1E

Exodus 9 in the TBT1E2

Exodus 9 in the TFTIP

Exodus 9 in the TFTU

Exodus 9 in the TGNTATF3T

Exodus 9 in the THAI

Exodus 9 in the TNFD

Exodus 9 in the TNT

Exodus 9 in the TNTIK

Exodus 9 in the TNTIL

Exodus 9 in the TNTIN

Exodus 9 in the TNTIP

Exodus 9 in the TNTIZ

Exodus 9 in the TOMA

Exodus 9 in the TTENT

Exodus 9 in the UBG

Exodus 9 in the UGV

Exodus 9 in the UGV2

Exodus 9 in the UGV3

Exodus 9 in the VBL

Exodus 9 in the VDCC

Exodus 9 in the YALU

Exodus 9 in the YAPE

Exodus 9 in the YBVTP

Exodus 9 in the ZBP