Ezekiel 21 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu. 3 Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. 4 Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto. 5 Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’ 6 “Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu. 7 Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.” 8 Yehova anandiyankhulanso kuti, 9 “Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,“Izi ndi zimene Yehova akunena:Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa. 10 Lanoledwa kuti likaphe,lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi!“ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo. 11 “ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,ndi kuti linyamulidwe,lanoledwa ndi kupukutidwa,kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha. 12 Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga;zidzagweranso akalonga onse a Israeli.Adzaphedwa ndi lupangapamodzi ndi anthu anga.Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni. 13 “ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’ 14 “Tsono mwana wa munthu, nenerandipo uwombe mʼmanja.Lupanga likanthe kawiringakhale katatu.Limenelo ndilo lupanga lophera anthu.Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsalimene likuwazungulira. 15 Ndawayikira pa zipata zawo zonselupanga laphuliphulikuti ataye mtimandiponso kuti anthu ambiri agwe.Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzindi kuti azilisolola kuphera anthu. 16 Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,kenaka kumanzere,kulikonse kumene msonga yako yaloza. 17 Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,ndipo ndidzaziziritsa ukali wangaIne Yehova ndayankhula.” 18 Yehova anandiyankhulanso kuti, 19 “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda. 20 Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa. 21 Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe. 22 Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo. 23 Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo. 24 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo. 25 “ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni, 26 Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. 27 Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’ 28 “Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,“ ‘Lupanga, lupanga,alisolola kuti liphe anthu,alipukuta kuti liwonongendi kuti lingʼanime ngati mphenzi. 29 Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso.Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipaamene tsiku lawo lafika,ndiye kuti nthawiya kulangidwa kwawo komaliza. 30 “ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.Ku malo kumene inu munabadwira,mʼdziko la makolo anu,ndidzakuweruzani. 31 Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani.Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza;anthu odziwa bwino kuwononga zinthu. 32 Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe.Simudzakumbukiridwansopakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”

In Other Versions

Ezekiel 21 in the ANGEFD

Ezekiel 21 in the ANTPNG2D

Ezekiel 21 in the AS21

Ezekiel 21 in the BAGH

Ezekiel 21 in the BBPNG

Ezekiel 21 in the BBT1E

Ezekiel 21 in the BDS

Ezekiel 21 in the BEV

Ezekiel 21 in the BHAD

Ezekiel 21 in the BIB

Ezekiel 21 in the BLPT

Ezekiel 21 in the BNT

Ezekiel 21 in the BNTABOOT

Ezekiel 21 in the BNTLV

Ezekiel 21 in the BOATCB

Ezekiel 21 in the BOATCB2

Ezekiel 21 in the BOBCV

Ezekiel 21 in the BOCNT

Ezekiel 21 in the BOECS

Ezekiel 21 in the BOHCB

Ezekiel 21 in the BOHCV

Ezekiel 21 in the BOHLNT

Ezekiel 21 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 21 in the BOICB

Ezekiel 21 in the BOILNTAP

Ezekiel 21 in the BOITCV

Ezekiel 21 in the BOKCV

Ezekiel 21 in the BOKCV2

Ezekiel 21 in the BOKHWOG

Ezekiel 21 in the BOKSSV

Ezekiel 21 in the BOLCB

Ezekiel 21 in the BOLCB2

Ezekiel 21 in the BOMCV

Ezekiel 21 in the BONAV

Ezekiel 21 in the BONCB

Ezekiel 21 in the BONLT

Ezekiel 21 in the BONUT2

Ezekiel 21 in the BOPLNT

Ezekiel 21 in the BOSCB

Ezekiel 21 in the BOSNC

Ezekiel 21 in the BOTLNT

Ezekiel 21 in the BOVCB

Ezekiel 21 in the BOYCB

Ezekiel 21 in the BPBB

Ezekiel 21 in the BPH

Ezekiel 21 in the BSB

Ezekiel 21 in the CCB

Ezekiel 21 in the CUV

Ezekiel 21 in the CUVS

Ezekiel 21 in the DBT

Ezekiel 21 in the DGDNT

Ezekiel 21 in the DHNT

Ezekiel 21 in the DNT

Ezekiel 21 in the ELBE

Ezekiel 21 in the EMTV

Ezekiel 21 in the ESV

Ezekiel 21 in the FBV

Ezekiel 21 in the FEB

Ezekiel 21 in the GGMNT

Ezekiel 21 in the GNT

Ezekiel 21 in the HARY

Ezekiel 21 in the HNT

Ezekiel 21 in the IRVA

Ezekiel 21 in the IRVB

Ezekiel 21 in the IRVG

Ezekiel 21 in the IRVH

Ezekiel 21 in the IRVK

Ezekiel 21 in the IRVM

Ezekiel 21 in the IRVM2

Ezekiel 21 in the IRVO

Ezekiel 21 in the IRVP

Ezekiel 21 in the IRVT

Ezekiel 21 in the IRVT2

Ezekiel 21 in the IRVU

Ezekiel 21 in the ISVN

Ezekiel 21 in the JSNT

Ezekiel 21 in the KAPI

Ezekiel 21 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 21 in the KBV

Ezekiel 21 in the KJV

Ezekiel 21 in the KNFD

Ezekiel 21 in the LBA

Ezekiel 21 in the LBLA

Ezekiel 21 in the LNT

Ezekiel 21 in the LSV

Ezekiel 21 in the MAAL

Ezekiel 21 in the MBV

Ezekiel 21 in the MBV2

Ezekiel 21 in the MHNT

Ezekiel 21 in the MKNFD

Ezekiel 21 in the MNG

Ezekiel 21 in the MNT

Ezekiel 21 in the MNT2

Ezekiel 21 in the MRS1T

Ezekiel 21 in the NAA

Ezekiel 21 in the NASB

Ezekiel 21 in the NBLA

Ezekiel 21 in the NBS

Ezekiel 21 in the NBVTP

Ezekiel 21 in the NET2

Ezekiel 21 in the NIV11

Ezekiel 21 in the NNT

Ezekiel 21 in the NNT2

Ezekiel 21 in the NNT3

Ezekiel 21 in the PDDPT

Ezekiel 21 in the PFNT

Ezekiel 21 in the RMNT

Ezekiel 21 in the SBIAS

Ezekiel 21 in the SBIBS

Ezekiel 21 in the SBIBS2

Ezekiel 21 in the SBICS

Ezekiel 21 in the SBIDS

Ezekiel 21 in the SBIGS

Ezekiel 21 in the SBIHS

Ezekiel 21 in the SBIIS

Ezekiel 21 in the SBIIS2

Ezekiel 21 in the SBIIS3

Ezekiel 21 in the SBIKS

Ezekiel 21 in the SBIKS2

Ezekiel 21 in the SBIMS

Ezekiel 21 in the SBIOS

Ezekiel 21 in the SBIPS

Ezekiel 21 in the SBISS

Ezekiel 21 in the SBITS

Ezekiel 21 in the SBITS2

Ezekiel 21 in the SBITS3

Ezekiel 21 in the SBITS4

Ezekiel 21 in the SBIUS

Ezekiel 21 in the SBIVS

Ezekiel 21 in the SBT

Ezekiel 21 in the SBT1E

Ezekiel 21 in the SCHL

Ezekiel 21 in the SNT

Ezekiel 21 in the SUSU

Ezekiel 21 in the SUSU2

Ezekiel 21 in the SYNO

Ezekiel 21 in the TBIAOTANT

Ezekiel 21 in the TBT1E

Ezekiel 21 in the TBT1E2

Ezekiel 21 in the TFTIP

Ezekiel 21 in the TFTU

Ezekiel 21 in the TGNTATF3T

Ezekiel 21 in the THAI

Ezekiel 21 in the TNFD

Ezekiel 21 in the TNT

Ezekiel 21 in the TNTIK

Ezekiel 21 in the TNTIL

Ezekiel 21 in the TNTIN

Ezekiel 21 in the TNTIP

Ezekiel 21 in the TNTIZ

Ezekiel 21 in the TOMA

Ezekiel 21 in the TTENT

Ezekiel 21 in the UBG

Ezekiel 21 in the UGV

Ezekiel 21 in the UGV2

Ezekiel 21 in the UGV3

Ezekiel 21 in the VBL

Ezekiel 21 in the VDCC

Ezekiel 21 in the YALU

Ezekiel 21 in the YAPE

Ezekiel 21 in the YBVTP

Ezekiel 21 in the ZBP