Judges 18 (BOGWICC)

1 Masiku amenewo munalibe mfumu mu Israeli.Ndipo anthu a fuko la Dani amafunafuna malo okhalamo ngati cholowa chawo, chifukwa kufikira nthawi imeneyo anali asanalandire cholowa chawo pakati pa mafuko a Israeli. 2 Choncho fuko la Dani linatumiza kuchokera ku mabanja awo onse anthu olimba mtima asanu. Anthuwa anachokera ku Zora ndi ku Esitaoli ndipo anatumidwa kukazonda ndi kuliyendera dzikolo. Anthu amenewa ankayimira fuko lonse la Dani. Anthuwa anawawuza kuti, “Pitani mukazonde dzikolo.”Anthuwa anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ndi kupita ku nyumba ya Mika komwe anakagona. 3 Ali ku nyumba ya Mika anazindikira mawu a mnyamata, Mlevi uja. Choncho anapita kwa iye namufunsa kuti, “Unabwera ndi ndani kuno? Nanga ukuchita chiyani ku malo ano? Komanso nʼchifukwa chiyani uli kuno?” 4 Iye anawawuza zimene Mika anamuchitira ndipo anati, “Iye anandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.” 5 Kenaka iwo anati kwa iye, “Chonde tifunsire kwa Mulungu kuti tidziwe ngati ulendo wathuwu tiyende bwino.” 6 Wansembeyo anawayankha kuti, “Pitani mu mtendere, Yehova ali ndi inu pa ulendo wanuwu.” 7 Choncho anthu asanuwo ananyamuka ndipo anafika ku Laisi, kumene anaona kuti anthu ankakhala mwabata monga anthu a ku Sidoni. Anali anthu opanda chowavuta ndiponso aphee. Tsono popeza mʼdziko mwawo analibe chosowa, iwo anali a chuma. Anaonanso kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Sidoni ndipo analibe ubale ndi wina aliyense. 8 Ozonda dziko aja atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi Esitaoli, abale awowo anawafunsa kuti, “Mwaonako zotani?” 9 “Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo popeza taliona dziko lawolo kuti ndi lachonde kwambiri. Kodi simuchitapo kanthu? Musachite mphwayi kupita mʼdzikomo ndi kukalilanda. 10 Mukalowa, mukapeza anthu amene ali osatekeseka ndi dziko lalikulu. Yehova wakupatsani dziko limeneli. Malowo ngosasowa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.” 11 Kenaka anthu 600 a fuko la Dani ananyamuka ku Zora ndi Esitaoli atanyamula zida za nkhondo. 12 Tsono anakamanga msasa ku Kiriati-Yearimu mʼdziko la Yuda. Malowa ali kumadzulo kwa Kiriati-Yearimu. Ichi ndi chifukwa chake malowo akutchedwa Mahane Dani mpaka lero. 13 Kuchokera kumeneko anapita ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anafika ku nyumba ya Mika. 14 Anthu asanu amene anakazonda dziko la Laisi anati kwa abale awo, “Kodi mukudziwa kuti imodzi mwa nyumba izi muli efodi, mafano a mʼnyumba otchedwa terafimu, fano losema ndiponso fano lokuta ndi siliva? Ndiye mudziwe chochita.” 15 Choncho anthuwa anapatuka napita ku nyumba ya Mika kumene mnyamata, Mlevi uja ankakhala ndipo anamufunsa za mmene zinthu zilili. 16 Nthawi imeneyi nʼkuti anthu 600 a fuko la Dani aja atayima pa chipata atanyamula zida za nkhondo. 17 Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata. 18 Anthuwo atalowa mʼnyumba ya Mika ndi kutenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba, ndi fano lokutidwa ndi siliva, wansembeyo anawafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani?” 19 Iwo anamuyankha kuti, “Khala chete usayankhule. Tsagana nafe ndipo udzakhala mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino kwa iwe kukhala wansembe wa fuko lonse la Israeli mʼmalo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?” 20 Wansembeyo anakondwera ndipo anatenga efodi, fano la mʼnyumba ndi fano losema natsagana nawo. 21 Choncho iwo anatembenuka nachoka, atatsogoza ana, zoweta ndi katundu wawo yense. 22 Atayenda mtunda pangʼono kuchokera pa nyumba ya Mika, anthu amene amakhala pafupi ndi nyumba ya Mika anasonkhana kulondola a fuko la Dani aja, ndipo anawapeza. 23 Atawafuwulira, a fuko la Dani aja anachewuka ndipo anafunsa Mika kuti, “Chavuta nʼchiyani kuti usonkhanitse anthu chotere?” 24 Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?” 25 Anthu a fuko la Dani aja anayankha kuti, “Usayankhuleponso kanthu chifukwa anthu awa angapse mtima nakumenya ndipo iwe ndi banja lako lonse nʼkutayapo miyoyo yanu.” 26 Choncho anthu a fuko la Dani anapitiriza ulendo wawo. Mika ataona kuti anthuwo anali amphamvu kuposa iye, anangotembenuka kubwerera kwawo. 27 Anthu a fuko la Dani aja anatenga zinthu zimene Mika anapanga pamodzi ndi wansembe uja. Iwo anakafika ku Laisi kwa anthu a phee, osatekeseka aja ndipo anawathira nkhondo, nawapha ndi kutentha mzindawo ndi moto. 28 Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu.Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo. 29 Iwo anawutcha mzindawo Dani, kutengera dzina la kholo lawo Dani, amene anali mwana wa Israeli, ngakhale kuti mzindawo poyamba unali Laisi. 30 Anthu a fuko la Dani anayimiritsa fano losema lija. Yonatani mwana wa Geresomu, mwana wa Mose pamodzi ndi ana ake onse anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo. 31 Choncho anthu a fuko la Dani ankapembedza fano limene Mika anapanga nthawi yonse pamene nyumba ya Mulungu inali ku Silo.

In Other Versions

Judges 18 in the ANGEFD

Judges 18 in the ANTPNG2D

Judges 18 in the AS21

Judges 18 in the BAGH

Judges 18 in the BBPNG

Judges 18 in the BBT1E

Judges 18 in the BDS

Judges 18 in the BEV

Judges 18 in the BHAD

Judges 18 in the BIB

Judges 18 in the BLPT

Judges 18 in the BNT

Judges 18 in the BNTABOOT

Judges 18 in the BNTLV

Judges 18 in the BOATCB

Judges 18 in the BOATCB2

Judges 18 in the BOBCV

Judges 18 in the BOCNT

Judges 18 in the BOECS

Judges 18 in the BOHCB

Judges 18 in the BOHCV

Judges 18 in the BOHLNT

Judges 18 in the BOHNTLTAL

Judges 18 in the BOICB

Judges 18 in the BOILNTAP

Judges 18 in the BOITCV

Judges 18 in the BOKCV

Judges 18 in the BOKCV2

Judges 18 in the BOKHWOG

Judges 18 in the BOKSSV

Judges 18 in the BOLCB

Judges 18 in the BOLCB2

Judges 18 in the BOMCV

Judges 18 in the BONAV

Judges 18 in the BONCB

Judges 18 in the BONLT

Judges 18 in the BONUT2

Judges 18 in the BOPLNT

Judges 18 in the BOSCB

Judges 18 in the BOSNC

Judges 18 in the BOTLNT

Judges 18 in the BOVCB

Judges 18 in the BOYCB

Judges 18 in the BPBB

Judges 18 in the BPH

Judges 18 in the BSB

Judges 18 in the CCB

Judges 18 in the CUV

Judges 18 in the CUVS

Judges 18 in the DBT

Judges 18 in the DGDNT

Judges 18 in the DHNT

Judges 18 in the DNT

Judges 18 in the ELBE

Judges 18 in the EMTV

Judges 18 in the ESV

Judges 18 in the FBV

Judges 18 in the FEB

Judges 18 in the GGMNT

Judges 18 in the GNT

Judges 18 in the HARY

Judges 18 in the HNT

Judges 18 in the IRVA

Judges 18 in the IRVB

Judges 18 in the IRVG

Judges 18 in the IRVH

Judges 18 in the IRVK

Judges 18 in the IRVM

Judges 18 in the IRVM2

Judges 18 in the IRVO

Judges 18 in the IRVP

Judges 18 in the IRVT

Judges 18 in the IRVT2

Judges 18 in the IRVU

Judges 18 in the ISVN

Judges 18 in the JSNT

Judges 18 in the KAPI

Judges 18 in the KBT1ETNIK

Judges 18 in the KBV

Judges 18 in the KJV

Judges 18 in the KNFD

Judges 18 in the LBA

Judges 18 in the LBLA

Judges 18 in the LNT

Judges 18 in the LSV

Judges 18 in the MAAL

Judges 18 in the MBV

Judges 18 in the MBV2

Judges 18 in the MHNT

Judges 18 in the MKNFD

Judges 18 in the MNG

Judges 18 in the MNT

Judges 18 in the MNT2

Judges 18 in the MRS1T

Judges 18 in the NAA

Judges 18 in the NASB

Judges 18 in the NBLA

Judges 18 in the NBS

Judges 18 in the NBVTP

Judges 18 in the NET2

Judges 18 in the NIV11

Judges 18 in the NNT

Judges 18 in the NNT2

Judges 18 in the NNT3

Judges 18 in the PDDPT

Judges 18 in the PFNT

Judges 18 in the RMNT

Judges 18 in the SBIAS

Judges 18 in the SBIBS

Judges 18 in the SBIBS2

Judges 18 in the SBICS

Judges 18 in the SBIDS

Judges 18 in the SBIGS

Judges 18 in the SBIHS

Judges 18 in the SBIIS

Judges 18 in the SBIIS2

Judges 18 in the SBIIS3

Judges 18 in the SBIKS

Judges 18 in the SBIKS2

Judges 18 in the SBIMS

Judges 18 in the SBIOS

Judges 18 in the SBIPS

Judges 18 in the SBISS

Judges 18 in the SBITS

Judges 18 in the SBITS2

Judges 18 in the SBITS3

Judges 18 in the SBITS4

Judges 18 in the SBIUS

Judges 18 in the SBIVS

Judges 18 in the SBT

Judges 18 in the SBT1E

Judges 18 in the SCHL

Judges 18 in the SNT

Judges 18 in the SUSU

Judges 18 in the SUSU2

Judges 18 in the SYNO

Judges 18 in the TBIAOTANT

Judges 18 in the TBT1E

Judges 18 in the TBT1E2

Judges 18 in the TFTIP

Judges 18 in the TFTU

Judges 18 in the TGNTATF3T

Judges 18 in the THAI

Judges 18 in the TNFD

Judges 18 in the TNT

Judges 18 in the TNTIK

Judges 18 in the TNTIL

Judges 18 in the TNTIN

Judges 18 in the TNTIP

Judges 18 in the TNTIZ

Judges 18 in the TOMA

Judges 18 in the TTENT

Judges 18 in the UBG

Judges 18 in the UGV

Judges 18 in the UGV2

Judges 18 in the UGV3

Judges 18 in the VBL

Judges 18 in the VDCC

Judges 18 in the YALU

Judges 18 in the YAPE

Judges 18 in the YBVTP

Judges 18 in the ZBP