Leviticus 2 (BOGWICC)

1 “ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, 2 ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova. 3 Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova. 4 “ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. 5 Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. 6 Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya. 7 Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 8 Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa. 9 Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova. 10 Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova. 11 “ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. 12 Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. 13 Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse. 14 “ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. 15 Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya. 16 Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.

In Other Versions

Leviticus 2 in the ANGEFD

Leviticus 2 in the ANTPNG2D

Leviticus 2 in the AS21

Leviticus 2 in the BAGH

Leviticus 2 in the BBPNG

Leviticus 2 in the BBT1E

Leviticus 2 in the BDS

Leviticus 2 in the BEV

Leviticus 2 in the BHAD

Leviticus 2 in the BIB

Leviticus 2 in the BLPT

Leviticus 2 in the BNT

Leviticus 2 in the BNTABOOT

Leviticus 2 in the BNTLV

Leviticus 2 in the BOATCB

Leviticus 2 in the BOATCB2

Leviticus 2 in the BOBCV

Leviticus 2 in the BOCNT

Leviticus 2 in the BOECS

Leviticus 2 in the BOHCB

Leviticus 2 in the BOHCV

Leviticus 2 in the BOHLNT

Leviticus 2 in the BOHNTLTAL

Leviticus 2 in the BOICB

Leviticus 2 in the BOILNTAP

Leviticus 2 in the BOITCV

Leviticus 2 in the BOKCV

Leviticus 2 in the BOKCV2

Leviticus 2 in the BOKHWOG

Leviticus 2 in the BOKSSV

Leviticus 2 in the BOLCB

Leviticus 2 in the BOLCB2

Leviticus 2 in the BOMCV

Leviticus 2 in the BONAV

Leviticus 2 in the BONCB

Leviticus 2 in the BONLT

Leviticus 2 in the BONUT2

Leviticus 2 in the BOPLNT

Leviticus 2 in the BOSCB

Leviticus 2 in the BOSNC

Leviticus 2 in the BOTLNT

Leviticus 2 in the BOVCB

Leviticus 2 in the BOYCB

Leviticus 2 in the BPBB

Leviticus 2 in the BPH

Leviticus 2 in the BSB

Leviticus 2 in the CCB

Leviticus 2 in the CUV

Leviticus 2 in the CUVS

Leviticus 2 in the DBT

Leviticus 2 in the DGDNT

Leviticus 2 in the DHNT

Leviticus 2 in the DNT

Leviticus 2 in the ELBE

Leviticus 2 in the EMTV

Leviticus 2 in the ESV

Leviticus 2 in the FBV

Leviticus 2 in the FEB

Leviticus 2 in the GGMNT

Leviticus 2 in the GNT

Leviticus 2 in the HARY

Leviticus 2 in the HNT

Leviticus 2 in the IRVA

Leviticus 2 in the IRVB

Leviticus 2 in the IRVG

Leviticus 2 in the IRVH

Leviticus 2 in the IRVK

Leviticus 2 in the IRVM

Leviticus 2 in the IRVM2

Leviticus 2 in the IRVO

Leviticus 2 in the IRVP

Leviticus 2 in the IRVT

Leviticus 2 in the IRVT2

Leviticus 2 in the IRVU

Leviticus 2 in the ISVN

Leviticus 2 in the JSNT

Leviticus 2 in the KAPI

Leviticus 2 in the KBT1ETNIK

Leviticus 2 in the KBV

Leviticus 2 in the KJV

Leviticus 2 in the KNFD

Leviticus 2 in the LBA

Leviticus 2 in the LBLA

Leviticus 2 in the LNT

Leviticus 2 in the LSV

Leviticus 2 in the MAAL

Leviticus 2 in the MBV

Leviticus 2 in the MBV2

Leviticus 2 in the MHNT

Leviticus 2 in the MKNFD

Leviticus 2 in the MNG

Leviticus 2 in the MNT

Leviticus 2 in the MNT2

Leviticus 2 in the MRS1T

Leviticus 2 in the NAA

Leviticus 2 in the NASB

Leviticus 2 in the NBLA

Leviticus 2 in the NBS

Leviticus 2 in the NBVTP

Leviticus 2 in the NET2

Leviticus 2 in the NIV11

Leviticus 2 in the NNT

Leviticus 2 in the NNT2

Leviticus 2 in the NNT3

Leviticus 2 in the PDDPT

Leviticus 2 in the PFNT

Leviticus 2 in the RMNT

Leviticus 2 in the SBIAS

Leviticus 2 in the SBIBS

Leviticus 2 in the SBIBS2

Leviticus 2 in the SBICS

Leviticus 2 in the SBIDS

Leviticus 2 in the SBIGS

Leviticus 2 in the SBIHS

Leviticus 2 in the SBIIS

Leviticus 2 in the SBIIS2

Leviticus 2 in the SBIIS3

Leviticus 2 in the SBIKS

Leviticus 2 in the SBIKS2

Leviticus 2 in the SBIMS

Leviticus 2 in the SBIOS

Leviticus 2 in the SBIPS

Leviticus 2 in the SBISS

Leviticus 2 in the SBITS

Leviticus 2 in the SBITS2

Leviticus 2 in the SBITS3

Leviticus 2 in the SBITS4

Leviticus 2 in the SBIUS

Leviticus 2 in the SBIVS

Leviticus 2 in the SBT

Leviticus 2 in the SBT1E

Leviticus 2 in the SCHL

Leviticus 2 in the SNT

Leviticus 2 in the SUSU

Leviticus 2 in the SUSU2

Leviticus 2 in the SYNO

Leviticus 2 in the TBIAOTANT

Leviticus 2 in the TBT1E

Leviticus 2 in the TBT1E2

Leviticus 2 in the TFTIP

Leviticus 2 in the TFTU

Leviticus 2 in the TGNTATF3T

Leviticus 2 in the THAI

Leviticus 2 in the TNFD

Leviticus 2 in the TNT

Leviticus 2 in the TNTIK

Leviticus 2 in the TNTIL

Leviticus 2 in the TNTIN

Leviticus 2 in the TNTIP

Leviticus 2 in the TNTIZ

Leviticus 2 in the TOMA

Leviticus 2 in the TTENT

Leviticus 2 in the UBG

Leviticus 2 in the UGV

Leviticus 2 in the UGV2

Leviticus 2 in the UGV3

Leviticus 2 in the VBL

Leviticus 2 in the VDCC

Leviticus 2 in the YALU

Leviticus 2 in the YAPE

Leviticus 2 in the YBVTP

Leviticus 2 in the ZBP