Psalms 141 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine.Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu. 2 Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani;kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo. 3 Yehova ikani mlonda pakamwa panga;londerani khomo la pa milomo yanga. 4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa;kuchita ntchito zonyansapamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa;musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo. 5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo;andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga.Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa. 6 Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri,ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino. 7 Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza,ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.” 8 Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse;ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa. 9 Mundipulumutse ku misampha imene anditchera,ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera. 10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo,mpaka ine nditadutsa mwamtendere.