Psalms 52 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.” 1 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu? 2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,ntchito yako nʼkunyenga. 3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. Sela 4 Umakonda mawu onse opweteka,iwe lilime lachinyengo! 5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo. 6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;adzamuseka nʼkumanena kuti, 7 “Pano tsopano pali munthuamene sanayese Mulungu linga lake,koma anakhulupirira chuma chake chambirinalimbika kuchita zoyipa!” 8 Koma ine ndili ngati mtengo wa oliviwobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungukwa nthawi za nthawi. 9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezerapakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.