1 Chronicles 2 (BOGWICC)
1 Ana a Israeli anali awa:Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, 2 Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri. 3 Ana a Yuda anali awa:Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha. 4 Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu. 5 Ana a Perezi anali awa:Hezironi ndi Hamuli. 6 Ana a Zera anali awa:Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu. 7 Mwana wa Karimi analiAkani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa. 8 Mwana wa Etani analiAzariya. 9 Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali:Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai. 10 Ramu anaberekaAminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda. 11 Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi, 12 Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese. 13 Yese anaberekaEliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea, 14 wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15 wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide. 16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli. 17 Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli. 18 Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. 19 Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri. 20 Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli. 21 Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu. 22 Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi. 23 (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi. 24 Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa. 25 Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali:Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya. 26 Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu. 27 Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa:Maazi, Yamini ndi Ekeri. 28 Ana a Onamu anali awa:Shamai ndi Yada.Ana a Shamai anali awa:Nadabu ndi Abisuri. 29 Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi. 30 Ana a Nadabu anali awa:Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana. 31 Ana a Apaimu anali awa:Isi, amene anabereka Sesani.Sesani anabereka Ahilai. 32 Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa:Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana. 33 Ana a Yonatani anali awa:Peleti ndi Zaza.Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli. 34 Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha.Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha. 35 Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi. 36 Atayi anali abambo ake a Natani,Natani anali abambo ake a Zabadi, 37 Zabadi anali abambo a Efilali,Efilali anali abambo a Obedi, 38 Obedi anali abambo a Yehu,Yehu anali abambo a Azariya, 39 Azariya anali abambo a Helezi,Helezi anali abambo a Eleasa, 40 Eleasa anali abambo ake a Sisimai,Sisimai anali abambo a Salumu, 41 Salumu anali abambo a Yekamiya,Yekamiya anali abambo a Elisama. 42 Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa:Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni. 43 Ana a Hebroni anali awa:Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. 44 Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai. 45 Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri. 46 Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi. 47 Ana a Yahidai anali awa:Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi. 48 Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana. 49 Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. 50 Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa:Sobala abambo a Kiriati Yearimu, 51 Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera. 52 Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi:Harowe, theka la banja la Manahati, 53 ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa. 54 Zidzukulu za Salima zinali izi:Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori, 55 ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
In Other Versions
1 Chronicles 2 in the ANTPNG2D
1 Chronicles 2 in the BNTABOOT
1 Chronicles 2 in the BOHNTLTAL
1 Chronicles 2 in the BOILNTAP
1 Chronicles 2 in the KBT1ETNIK
1 Chronicles 2 in the TBIAOTANT