1 Samuel 4 (BOGWICC)

1 Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse.Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. 2 Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo. 3 Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.” 4 Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu. 5 Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka. 6 Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?”Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako, 7 Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe. 8 Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu. 9 Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” 10 Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. 11 Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa. 12 Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni. 13 Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira. 14 Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?”Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera. 15 Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona. 16 Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.”Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?” 17 Iye anayankha kuti, “Aisraeli athawa pamaso pa Afilisti. Anthu ambirimbiri aphedwa. Ana anunso Hofini ndi Finehasi aphedwa. Bokosi la Mulungu nalonso lalandidwa.” 18 Atangotchula Bokosi la Yehova, Eli anagwa chagada, kuchoka pa mpando wake umene unali mʼmbali mwa chitseko cha mpanda. Khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali okalamba ndi onenepa kwambiri. Iye anatsogolera Israeli zaka makumi anayi. 19 Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana. 20 Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako. 21 Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake. 22 Ananena momwemo kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli, pakuti Bokosi la Mulungu lalandidwa.”

In Other Versions

1 Samuel 4 in the ANGEFD

1 Samuel 4 in the ANTPNG2D

1 Samuel 4 in the AS21

1 Samuel 4 in the BAGH

1 Samuel 4 in the BBPNG

1 Samuel 4 in the BBT1E

1 Samuel 4 in the BDS

1 Samuel 4 in the BEV

1 Samuel 4 in the BHAD

1 Samuel 4 in the BIB

1 Samuel 4 in the BLPT

1 Samuel 4 in the BNT

1 Samuel 4 in the BNTABOOT

1 Samuel 4 in the BNTLV

1 Samuel 4 in the BOATCB

1 Samuel 4 in the BOATCB2

1 Samuel 4 in the BOBCV

1 Samuel 4 in the BOCNT

1 Samuel 4 in the BOECS

1 Samuel 4 in the BOHCB

1 Samuel 4 in the BOHCV

1 Samuel 4 in the BOHLNT

1 Samuel 4 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 4 in the BOICB

1 Samuel 4 in the BOILNTAP

1 Samuel 4 in the BOITCV

1 Samuel 4 in the BOKCV

1 Samuel 4 in the BOKCV2

1 Samuel 4 in the BOKHWOG

1 Samuel 4 in the BOKSSV

1 Samuel 4 in the BOLCB

1 Samuel 4 in the BOLCB2

1 Samuel 4 in the BOMCV

1 Samuel 4 in the BONAV

1 Samuel 4 in the BONCB

1 Samuel 4 in the BONLT

1 Samuel 4 in the BONUT2

1 Samuel 4 in the BOPLNT

1 Samuel 4 in the BOSCB

1 Samuel 4 in the BOSNC

1 Samuel 4 in the BOTLNT

1 Samuel 4 in the BOVCB

1 Samuel 4 in the BOYCB

1 Samuel 4 in the BPBB

1 Samuel 4 in the BPH

1 Samuel 4 in the BSB

1 Samuel 4 in the CCB

1 Samuel 4 in the CUV

1 Samuel 4 in the CUVS

1 Samuel 4 in the DBT

1 Samuel 4 in the DGDNT

1 Samuel 4 in the DHNT

1 Samuel 4 in the DNT

1 Samuel 4 in the ELBE

1 Samuel 4 in the EMTV

1 Samuel 4 in the ESV

1 Samuel 4 in the FBV

1 Samuel 4 in the FEB

1 Samuel 4 in the GGMNT

1 Samuel 4 in the GNT

1 Samuel 4 in the HARY

1 Samuel 4 in the HNT

1 Samuel 4 in the IRVA

1 Samuel 4 in the IRVB

1 Samuel 4 in the IRVG

1 Samuel 4 in the IRVH

1 Samuel 4 in the IRVK

1 Samuel 4 in the IRVM

1 Samuel 4 in the IRVM2

1 Samuel 4 in the IRVO

1 Samuel 4 in the IRVP

1 Samuel 4 in the IRVT

1 Samuel 4 in the IRVT2

1 Samuel 4 in the IRVU

1 Samuel 4 in the ISVN

1 Samuel 4 in the JSNT

1 Samuel 4 in the KAPI

1 Samuel 4 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 4 in the KBV

1 Samuel 4 in the KJV

1 Samuel 4 in the KNFD

1 Samuel 4 in the LBA

1 Samuel 4 in the LBLA

1 Samuel 4 in the LNT

1 Samuel 4 in the LSV

1 Samuel 4 in the MAAL

1 Samuel 4 in the MBV

1 Samuel 4 in the MBV2

1 Samuel 4 in the MHNT

1 Samuel 4 in the MKNFD

1 Samuel 4 in the MNG

1 Samuel 4 in the MNT

1 Samuel 4 in the MNT2

1 Samuel 4 in the MRS1T

1 Samuel 4 in the NAA

1 Samuel 4 in the NASB

1 Samuel 4 in the NBLA

1 Samuel 4 in the NBS

1 Samuel 4 in the NBVTP

1 Samuel 4 in the NET2

1 Samuel 4 in the NIV11

1 Samuel 4 in the NNT

1 Samuel 4 in the NNT2

1 Samuel 4 in the NNT3

1 Samuel 4 in the PDDPT

1 Samuel 4 in the PFNT

1 Samuel 4 in the RMNT

1 Samuel 4 in the SBIAS

1 Samuel 4 in the SBIBS

1 Samuel 4 in the SBIBS2

1 Samuel 4 in the SBICS

1 Samuel 4 in the SBIDS

1 Samuel 4 in the SBIGS

1 Samuel 4 in the SBIHS

1 Samuel 4 in the SBIIS

1 Samuel 4 in the SBIIS2

1 Samuel 4 in the SBIIS3

1 Samuel 4 in the SBIKS

1 Samuel 4 in the SBIKS2

1 Samuel 4 in the SBIMS

1 Samuel 4 in the SBIOS

1 Samuel 4 in the SBIPS

1 Samuel 4 in the SBISS

1 Samuel 4 in the SBITS

1 Samuel 4 in the SBITS2

1 Samuel 4 in the SBITS3

1 Samuel 4 in the SBITS4

1 Samuel 4 in the SBIUS

1 Samuel 4 in the SBIVS

1 Samuel 4 in the SBT

1 Samuel 4 in the SBT1E

1 Samuel 4 in the SCHL

1 Samuel 4 in the SNT

1 Samuel 4 in the SUSU

1 Samuel 4 in the SUSU2

1 Samuel 4 in the SYNO

1 Samuel 4 in the TBIAOTANT

1 Samuel 4 in the TBT1E

1 Samuel 4 in the TBT1E2

1 Samuel 4 in the TFTIP

1 Samuel 4 in the TFTU

1 Samuel 4 in the TGNTATF3T

1 Samuel 4 in the THAI

1 Samuel 4 in the TNFD

1 Samuel 4 in the TNT

1 Samuel 4 in the TNTIK

1 Samuel 4 in the TNTIL

1 Samuel 4 in the TNTIN

1 Samuel 4 in the TNTIP

1 Samuel 4 in the TNTIZ

1 Samuel 4 in the TOMA

1 Samuel 4 in the TTENT

1 Samuel 4 in the UBG

1 Samuel 4 in the UGV

1 Samuel 4 in the UGV2

1 Samuel 4 in the UGV3

1 Samuel 4 in the VBL

1 Samuel 4 in the VDCC

1 Samuel 4 in the YALU

1 Samuel 4 in the YAPE

1 Samuel 4 in the YBVTP

1 Samuel 4 in the ZBP