1 Samuel 9 (BOGWICC)

1 Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. 2 Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa. 3 Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.” 4 Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe. 5 Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.” 6 Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.” 7 Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?” 8 Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” 9 (Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi). 10 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo. 11 Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?” 12 Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri. 13 Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.” 14 Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika. 15 Koma chadzulo lake Sauli asanafike, Yehova anali atamuwuza kale Samueli za zimenezi kuti, 16 “Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.” 17 Samueli atamuona Sauli, Yehova anamuwuza kuti, “Munthu ndinakuwuza uja ndi uyu. Iyeyu adzalamulira anthu anga.” 18 Tsono Sauli anayandikira Samueli pa chipata ndipo anamufunsa, “Kodi mungandiwuze kumene kuli nyumba ya mlosi?” 19 Samueli anayankha, “Ine ndine mlosiyo. Tsogolani kupita ku phiri pakuti lero mudya ndi ine, ndipo mawa mmawa ndidzakuwuzani zonse zimene zili mu mtima mwanu. 20 Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?” 21 Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?” 22 Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wake uja ndi kulowa nawo mʼchipinda chachikulu ndipo anawakhazika kutsogolo kwa anthu oyitanidwa. Onse pamodzi analipo anthu makumi atatu. 23 Tsono Samueli anati kwa wophika, “Bwera nayo nyama imene ndinakupatsa, imene ndinakuwuza kuti uyisunge pambali.” 24 Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli. 25 Atatsika kuchoka ku phiri kuja, Samueli anamukonzera Sauli malo ogona pa denga la nyumba yake, ndipo Sauli anagona pamenepo. 26 Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu. 27 Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”

In Other Versions

1 Samuel 9 in the ANGEFD

1 Samuel 9 in the ANTPNG2D

1 Samuel 9 in the AS21

1 Samuel 9 in the BAGH

1 Samuel 9 in the BBPNG

1 Samuel 9 in the BBT1E

1 Samuel 9 in the BDS

1 Samuel 9 in the BEV

1 Samuel 9 in the BHAD

1 Samuel 9 in the BIB

1 Samuel 9 in the BLPT

1 Samuel 9 in the BNT

1 Samuel 9 in the BNTABOOT

1 Samuel 9 in the BNTLV

1 Samuel 9 in the BOATCB

1 Samuel 9 in the BOATCB2

1 Samuel 9 in the BOBCV

1 Samuel 9 in the BOCNT

1 Samuel 9 in the BOECS

1 Samuel 9 in the BOHCB

1 Samuel 9 in the BOHCV

1 Samuel 9 in the BOHLNT

1 Samuel 9 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 9 in the BOICB

1 Samuel 9 in the BOILNTAP

1 Samuel 9 in the BOITCV

1 Samuel 9 in the BOKCV

1 Samuel 9 in the BOKCV2

1 Samuel 9 in the BOKHWOG

1 Samuel 9 in the BOKSSV

1 Samuel 9 in the BOLCB

1 Samuel 9 in the BOLCB2

1 Samuel 9 in the BOMCV

1 Samuel 9 in the BONAV

1 Samuel 9 in the BONCB

1 Samuel 9 in the BONLT

1 Samuel 9 in the BONUT2

1 Samuel 9 in the BOPLNT

1 Samuel 9 in the BOSCB

1 Samuel 9 in the BOSNC

1 Samuel 9 in the BOTLNT

1 Samuel 9 in the BOVCB

1 Samuel 9 in the BOYCB

1 Samuel 9 in the BPBB

1 Samuel 9 in the BPH

1 Samuel 9 in the BSB

1 Samuel 9 in the CCB

1 Samuel 9 in the CUV

1 Samuel 9 in the CUVS

1 Samuel 9 in the DBT

1 Samuel 9 in the DGDNT

1 Samuel 9 in the DHNT

1 Samuel 9 in the DNT

1 Samuel 9 in the ELBE

1 Samuel 9 in the EMTV

1 Samuel 9 in the ESV

1 Samuel 9 in the FBV

1 Samuel 9 in the FEB

1 Samuel 9 in the GGMNT

1 Samuel 9 in the GNT

1 Samuel 9 in the HARY

1 Samuel 9 in the HNT

1 Samuel 9 in the IRVA

1 Samuel 9 in the IRVB

1 Samuel 9 in the IRVG

1 Samuel 9 in the IRVH

1 Samuel 9 in the IRVK

1 Samuel 9 in the IRVM

1 Samuel 9 in the IRVM2

1 Samuel 9 in the IRVO

1 Samuel 9 in the IRVP

1 Samuel 9 in the IRVT

1 Samuel 9 in the IRVT2

1 Samuel 9 in the IRVU

1 Samuel 9 in the ISVN

1 Samuel 9 in the JSNT

1 Samuel 9 in the KAPI

1 Samuel 9 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 9 in the KBV

1 Samuel 9 in the KJV

1 Samuel 9 in the KNFD

1 Samuel 9 in the LBA

1 Samuel 9 in the LBLA

1 Samuel 9 in the LNT

1 Samuel 9 in the LSV

1 Samuel 9 in the MAAL

1 Samuel 9 in the MBV

1 Samuel 9 in the MBV2

1 Samuel 9 in the MHNT

1 Samuel 9 in the MKNFD

1 Samuel 9 in the MNG

1 Samuel 9 in the MNT

1 Samuel 9 in the MNT2

1 Samuel 9 in the MRS1T

1 Samuel 9 in the NAA

1 Samuel 9 in the NASB

1 Samuel 9 in the NBLA

1 Samuel 9 in the NBS

1 Samuel 9 in the NBVTP

1 Samuel 9 in the NET2

1 Samuel 9 in the NIV11

1 Samuel 9 in the NNT

1 Samuel 9 in the NNT2

1 Samuel 9 in the NNT3

1 Samuel 9 in the PDDPT

1 Samuel 9 in the PFNT

1 Samuel 9 in the RMNT

1 Samuel 9 in the SBIAS

1 Samuel 9 in the SBIBS

1 Samuel 9 in the SBIBS2

1 Samuel 9 in the SBICS

1 Samuel 9 in the SBIDS

1 Samuel 9 in the SBIGS

1 Samuel 9 in the SBIHS

1 Samuel 9 in the SBIIS

1 Samuel 9 in the SBIIS2

1 Samuel 9 in the SBIIS3

1 Samuel 9 in the SBIKS

1 Samuel 9 in the SBIKS2

1 Samuel 9 in the SBIMS

1 Samuel 9 in the SBIOS

1 Samuel 9 in the SBIPS

1 Samuel 9 in the SBISS

1 Samuel 9 in the SBITS

1 Samuel 9 in the SBITS2

1 Samuel 9 in the SBITS3

1 Samuel 9 in the SBITS4

1 Samuel 9 in the SBIUS

1 Samuel 9 in the SBIVS

1 Samuel 9 in the SBT

1 Samuel 9 in the SBT1E

1 Samuel 9 in the SCHL

1 Samuel 9 in the SNT

1 Samuel 9 in the SUSU

1 Samuel 9 in the SUSU2

1 Samuel 9 in the SYNO

1 Samuel 9 in the TBIAOTANT

1 Samuel 9 in the TBT1E

1 Samuel 9 in the TBT1E2

1 Samuel 9 in the TFTIP

1 Samuel 9 in the TFTU

1 Samuel 9 in the TGNTATF3T

1 Samuel 9 in the THAI

1 Samuel 9 in the TNFD

1 Samuel 9 in the TNT

1 Samuel 9 in the TNTIK

1 Samuel 9 in the TNTIL

1 Samuel 9 in the TNTIN

1 Samuel 9 in the TNTIP

1 Samuel 9 in the TNTIZ

1 Samuel 9 in the TOMA

1 Samuel 9 in the TTENT

1 Samuel 9 in the UBG

1 Samuel 9 in the UGV

1 Samuel 9 in the UGV2

1 Samuel 9 in the UGV3

1 Samuel 9 in the VBL

1 Samuel 9 in the VDCC

1 Samuel 9 in the YALU

1 Samuel 9 in the YAPE

1 Samuel 9 in the YBVTP

1 Samuel 9 in the ZBP