2 Chronicles 34 (BOGWICC)

1 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 31. 2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndi kutsata makhalidwe a Davide abambo ake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere. 3 Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa. 4 Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo. 5 Iye anatentha mafupa a ansembe pa maguwa awo, kotero iye anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu. 6 Ku mizinda ya Manase, Efereimu ndi Simeoni mpaka kufika ku Nafutali, ndiponso malo a mabanja owazungulira, 7 iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu. 8 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake. 9 Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu. 10 Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu. 11 Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka. 12 Anthuwa anagwira ntchitoyi mokhulupirika. Amene ankawayangʼanira anali Yahati ndi Obadiya, Alevi ochokera ku banja la Merari, ndi Zekariya ndi Mesulamu ochokera ku banja la Kohati. Alevi onse amene anali aluso loyimbira zida za nyimbo 13 ankayangʼanira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitawo ndiponso alonda apamakomo. 14 Pa nthawi imene ankatulutsa ndalama zimene anabwera nazo ku Nyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya anapeza Buku la Malamulo limene linaperekedwa kudzera mwa Mose. 15 Hilikiya anati kwa Safani, mlembi wa zochitika, “Ine ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Iye analipereka kwa Safani. 16 Ndipo Safani anapita nalo bukulo kwa mfumu ndi kumufotokozera kuti: “Akuluakulu anu akuchita zonse zimene zinapatsidwa kwa iwo. 17 Iwo alipira ndalama zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo azipereka kwa akapitawo ndi anthu antchito.” 18 Kenaka Safani, mlembi wa zochitika anawuza mfumu, “Wansembe, Hilikiya wandipatsa ine buku ili.” Ndipo Safani anawerenga bukulo pamaso pa mfumu. 19 Mfumu itamva mawu a Buku la Malamulo, inangʼamba mkanjo wake. 20 Iye analamula izi kwa Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi wa zochitika ndi Asaya mtumiki wa mfumu: 21 “Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.” 22 Hilikiya pamodzi ndi anthu amene anawatuma aja, anapita kukayankhula ndi mneneri wamkazi Hulida, amene anali mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira, wosunga zovala zaufumu. Hulida ankakhala mu Yerusalemu, mʼdera lachiwiri la mzindawo. 23 Iye anati kwa anthuwo, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, muwuzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti, 24 ‘Yehova akunena kuti, Ine ndidzabweretsa mavuto pamalo pano ndi pa anthu ake, matemberero onse amene alembedwa mʼbukuli amene awerengedwa pamaso pa mfumu ya Yuda. 25 Chifukwa iwo anasiya Ine ndi kufukiza lubani kwa milungu ina ndi kuwutsa mkwiyo wanga ndi zonse zimene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzatsanulidwa pamalo pano ndipo sudzazimitsidwa.’ 26 Uzani mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova Mulungu wa Israeli, ‘Chimene Yehova, Mulungu wa Israeli akunena mokhudzana ndi mawu amene mwamva ndi ichi: 27 Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova. 28 Tsono Ine ndidzakutengera kwa makolo ako, ndipo udzayikidwa mʼmanda mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene Ine ndidzabweretsa pa malo ano ndi pa iwo amene amakhala pano.’ ”Choncho iwo anatenga yankho lakelo ndi kubwerera kwa mfumu. 29 Ndipo mfumu inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu. 30 Iye anapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu a Yuda, anthu a mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Iye anawerenga pamaso pawo mawu onse a Buku la Chipangano, limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova. 31 Mfumu inayimirira pa chipilala chake ndipo inachitanso pangano pamaso pa Yehova: kutsatira Yehova, ndi kusunga malamulo ake, machitidwe ake ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndi kumvera mawu a pangano olembedwa mʼbukulo. 32 Tsono Yosiya anawuza aliyense amene anali mu Yerusalemu ndi Benjamini kuti azisunga panganoli. Anthu a mu Yerusalemu anachita izi motsata pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo. 33 Yosiya anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse limene linali la Aisraeli ndipo anawuza onse amene anali mu Israeli kutumikira Yehova Mulungu wawo. Pa masiku onse a moyo wake, iye sanaleke kutsatira Yehova, Mulungu wa makolo awo.

In Other Versions

2 Chronicles 34 in the ANGEFD

2 Chronicles 34 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 34 in the AS21

2 Chronicles 34 in the BAGH

2 Chronicles 34 in the BBPNG

2 Chronicles 34 in the BBT1E

2 Chronicles 34 in the BDS

2 Chronicles 34 in the BEV

2 Chronicles 34 in the BHAD

2 Chronicles 34 in the BIB

2 Chronicles 34 in the BLPT

2 Chronicles 34 in the BNT

2 Chronicles 34 in the BNTABOOT

2 Chronicles 34 in the BNTLV

2 Chronicles 34 in the BOATCB

2 Chronicles 34 in the BOATCB2

2 Chronicles 34 in the BOBCV

2 Chronicles 34 in the BOCNT

2 Chronicles 34 in the BOECS

2 Chronicles 34 in the BOHCB

2 Chronicles 34 in the BOHCV

2 Chronicles 34 in the BOHLNT

2 Chronicles 34 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 34 in the BOICB

2 Chronicles 34 in the BOILNTAP

2 Chronicles 34 in the BOITCV

2 Chronicles 34 in the BOKCV

2 Chronicles 34 in the BOKCV2

2 Chronicles 34 in the BOKHWOG

2 Chronicles 34 in the BOKSSV

2 Chronicles 34 in the BOLCB

2 Chronicles 34 in the BOLCB2

2 Chronicles 34 in the BOMCV

2 Chronicles 34 in the BONAV

2 Chronicles 34 in the BONCB

2 Chronicles 34 in the BONLT

2 Chronicles 34 in the BONUT2

2 Chronicles 34 in the BOPLNT

2 Chronicles 34 in the BOSCB

2 Chronicles 34 in the BOSNC

2 Chronicles 34 in the BOTLNT

2 Chronicles 34 in the BOVCB

2 Chronicles 34 in the BOYCB

2 Chronicles 34 in the BPBB

2 Chronicles 34 in the BPH

2 Chronicles 34 in the BSB

2 Chronicles 34 in the CCB

2 Chronicles 34 in the CUV

2 Chronicles 34 in the CUVS

2 Chronicles 34 in the DBT

2 Chronicles 34 in the DGDNT

2 Chronicles 34 in the DHNT

2 Chronicles 34 in the DNT

2 Chronicles 34 in the ELBE

2 Chronicles 34 in the EMTV

2 Chronicles 34 in the ESV

2 Chronicles 34 in the FBV

2 Chronicles 34 in the FEB

2 Chronicles 34 in the GGMNT

2 Chronicles 34 in the GNT

2 Chronicles 34 in the HARY

2 Chronicles 34 in the HNT

2 Chronicles 34 in the IRVA

2 Chronicles 34 in the IRVB

2 Chronicles 34 in the IRVG

2 Chronicles 34 in the IRVH

2 Chronicles 34 in the IRVK

2 Chronicles 34 in the IRVM

2 Chronicles 34 in the IRVM2

2 Chronicles 34 in the IRVO

2 Chronicles 34 in the IRVP

2 Chronicles 34 in the IRVT

2 Chronicles 34 in the IRVT2

2 Chronicles 34 in the IRVU

2 Chronicles 34 in the ISVN

2 Chronicles 34 in the JSNT

2 Chronicles 34 in the KAPI

2 Chronicles 34 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 34 in the KBV

2 Chronicles 34 in the KJV

2 Chronicles 34 in the KNFD

2 Chronicles 34 in the LBA

2 Chronicles 34 in the LBLA

2 Chronicles 34 in the LNT

2 Chronicles 34 in the LSV

2 Chronicles 34 in the MAAL

2 Chronicles 34 in the MBV

2 Chronicles 34 in the MBV2

2 Chronicles 34 in the MHNT

2 Chronicles 34 in the MKNFD

2 Chronicles 34 in the MNG

2 Chronicles 34 in the MNT

2 Chronicles 34 in the MNT2

2 Chronicles 34 in the MRS1T

2 Chronicles 34 in the NAA

2 Chronicles 34 in the NASB

2 Chronicles 34 in the NBLA

2 Chronicles 34 in the NBS

2 Chronicles 34 in the NBVTP

2 Chronicles 34 in the NET2

2 Chronicles 34 in the NIV11

2 Chronicles 34 in the NNT

2 Chronicles 34 in the NNT2

2 Chronicles 34 in the NNT3

2 Chronicles 34 in the PDDPT

2 Chronicles 34 in the PFNT

2 Chronicles 34 in the RMNT

2 Chronicles 34 in the SBIAS

2 Chronicles 34 in the SBIBS

2 Chronicles 34 in the SBIBS2

2 Chronicles 34 in the SBICS

2 Chronicles 34 in the SBIDS

2 Chronicles 34 in the SBIGS

2 Chronicles 34 in the SBIHS

2 Chronicles 34 in the SBIIS

2 Chronicles 34 in the SBIIS2

2 Chronicles 34 in the SBIIS3

2 Chronicles 34 in the SBIKS

2 Chronicles 34 in the SBIKS2

2 Chronicles 34 in the SBIMS

2 Chronicles 34 in the SBIOS

2 Chronicles 34 in the SBIPS

2 Chronicles 34 in the SBISS

2 Chronicles 34 in the SBITS

2 Chronicles 34 in the SBITS2

2 Chronicles 34 in the SBITS3

2 Chronicles 34 in the SBITS4

2 Chronicles 34 in the SBIUS

2 Chronicles 34 in the SBIVS

2 Chronicles 34 in the SBT

2 Chronicles 34 in the SBT1E

2 Chronicles 34 in the SCHL

2 Chronicles 34 in the SNT

2 Chronicles 34 in the SUSU

2 Chronicles 34 in the SUSU2

2 Chronicles 34 in the SYNO

2 Chronicles 34 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 34 in the TBT1E

2 Chronicles 34 in the TBT1E2

2 Chronicles 34 in the TFTIP

2 Chronicles 34 in the TFTU

2 Chronicles 34 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 34 in the THAI

2 Chronicles 34 in the TNFD

2 Chronicles 34 in the TNT

2 Chronicles 34 in the TNTIK

2 Chronicles 34 in the TNTIL

2 Chronicles 34 in the TNTIN

2 Chronicles 34 in the TNTIP

2 Chronicles 34 in the TNTIZ

2 Chronicles 34 in the TOMA

2 Chronicles 34 in the TTENT

2 Chronicles 34 in the UBG

2 Chronicles 34 in the UGV

2 Chronicles 34 in the UGV2

2 Chronicles 34 in the UGV3

2 Chronicles 34 in the VBL

2 Chronicles 34 in the VDCC

2 Chronicles 34 in the YALU

2 Chronicles 34 in the YAPE

2 Chronicles 34 in the YBVTP

2 Chronicles 34 in the ZBP