Daniel 11 (BOGWICC)

1 Ndipo chaka choyamba cha Dariyo Mmedi ine Mikayeli ndinabwera kumuthandiza ndi kumuteteza Gabrieli. 2 “Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi. 3 Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna. 4 Koma ufumu wake ukadzafika pachimake, udzawonongedwa ndi kugawidwa mʼzigawo zinayi. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa zidzukulu zake, ndipo olowa mʼmalo mwake sadzakhala ndi mphamvu monga anali nazo, chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena. 5 “Mfumu ya kummwera idzakhala yamphamvu, koma mmodzi mwa akalonga ake adzakhala ndi mphamvu kuposa iyo; adzalamulira ufumu wake waukulu kwambiri. 6 Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani. 7 “Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana. 8 Iye adzalandanso milungu yawo, mafano awo achitsulo, ndi ziwiya zawo zamtengowapatali zasiliva ndi golide ndi kubwerera nazo ku Igupto. Adzaleka osayithira nkhondo mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo. 9 Kenaka mfumu ya kumpoto idzathira nkhondo dziko la mfumu ya kummwera koma idzalephera ndi kubwerera kwawo. 10 Ana ake adzakonzekera nkhondo ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, limene lidzathira nkhondo mfumu yakummwera ngati chigumula mpaka kumalo ake otetezedwa. 11 “Kenaka mfumu yakummwera idzatuluka mokwiya ndi kumenya nkhondo ndi mfumu yakumpoto, imene idzasonkhanitsa gulu lalikulu la nkhondo, koma idzayigonjetsa. 12 Gulu la nkhondoli likadzagwidwa, mfumu yakummwera idzayamba kudzikuza ndipo idzapha anthu miyandamiyanda, koma kupambanaku sikudzapitirira. 13 Popeza mfumu ya kumpoto idzasonkhanitsa gulu lina lankhondo, lochulukirapo kuposa loyamba; ndipo patapita zaka zingapo idzabwera ndi chigulu chachikulu cha nkhondo chokonzekeratu ndi zida. 14 “Nthawi imeneyo ambiri adzawukira mfumu ya kummwera. Anthu achisokonezo pakati panu nawonso adzawukira pokwaniritsa masomphenya, koma sadzapambana. 15 Kenaka mfumu ya kumpoto idzafika ndikuzinga mzinda powunda nthumbira za nkhondo ndipo idzagonjetsa mzinda wotetezedwa. Gulu lankhondo la kummwera lidzasowa mphamvu; ngakhale akatswiri awo ankhondo sadzakhala ndi mphamvu zogonjetsera ankhondo a kumpoto. 16 Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija. 17 Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza. 18 Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye. 19 Zikadzatha izi, mfumu idzabwerera ku malo otetezedwa a dziko la kwawo koma idzapunthwa ndi kugwa osapezekanso. 20 “Mfumu imene idzatenga malo ake idzatumiza wokhometsa msonkho kuti chuma cha ufumu wake chichuluke. Komabe mʼzaka zochepa mfumuyo idzawonongedwa osati mu mkwiyo kapena ku nkhondo. 21 “Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo. 22 Kenaka adzagonetsa gulu lalikulu lankhondo kuphatikizapo Mkulu wa Ansembe wapangano. 23 Atatha kuchita naye pangano, iye adzachita monyenga, ndipo ngakhale adzakhale ndi anthu ochepa adzakhalabe ndi mphamvu. 24 Mwadzidzidzi, iye adzazithira nkhondo zigawo zolemera kwambiri ndipo adzachita zimene makolo ake ngakhale agogo ake sanachitepo. Iye adzagawira zolanda, zofunkha ndi chuma kwa omutsatira. Adzachita chiwembu cholanda mizinda yotetezedwa koma kwa kanthawi kochepa. 25 “Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera. 26 Amene amadya chakudya ndi mfumu adzamuukira; gulu lake lankhondo lidzagonjetsedwa, ndipo ambiri adzafera ku nkhondo. 27 Mafumu awiriwa mitima yawo idzalinga ku zoyipa. Azidzanamizana ali pa tebulo limodzi, koma zolinga zawo sizidzatheka chifukwa nthawi idzakhala isanakwane. 28 Mfumu ya kumpoto idzabwerera ku dziko la kwawo ndi chuma chambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa pangano lopatulika. Idzawononga panganolo ndipo kenaka idzabwerera ku dziko lake. 29 “Patapita nthawi mfumu ya kumpoto idzabwereranso kummwera koma sidzapambana monga inachitira kale. 30 Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera. 31 “Ankhondo ake adzayipitsa linga la Nyumba ya Mulungu ndipo adzathetsa nsembe za tsiku ndi tsiku. Kenaka adzakhazikitsa chonyansa chimene chabweretsa chiwonongeko. 32 Ndi mawu oshashalika mfumuyo idzakopa amene anaphwanya pangano, koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzalimbika ndipo adzayikana mfumuyo kwathunthu. 33 “Amene ndi anzeru adzalangiza ambiri. Koma patapita kanthawi adzaphedwa ndi lupanga kapena kutenthedwa, kapena kugwidwa kapena kulandidwa katundu. 34 Pa nthawi yozunzikayi ena adzawathandiza pangʼono, koma ambiri othandizawo adzakhala achinyengo. 35 Ena mwa anzeruwo adzaphedwa ndi cholinga chakuti ayengedwe, otsala mwa iwo ayeretsedwe ndi kukhala wopanda banga kufikira nthawi yomaliza, popeza idzafika ndithu nthawi imene Mulungu wayika. 36 “Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika. 37 Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse. 38 Mʼmalo mwa onsewo, idzachitira ulemu mulungu wachitetezo; mulungu wosadziwika ndi makolo ake. Iyo idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, ndi miyala yokongola, ndiponso mphatso za pamwamba kwambiri. 39 Anthu opembedza mulungu wachilendo adzakhala ngati linga lake. Idzalemekeza iwowa kwambiri, ndipo idzawayika kuti alamulire anthu ambiri. Idzawagawira dziko ngati malipiro awo. 40 “Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira. 41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka. 42 Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka. 43 Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo. 44 Koma uthenga wochokera kummawa ndi kumpoto udzayiopsa, ndipo idzapita ndi ukali kukawononga ndi kutheratu anthu ambiri. 45 Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”

In Other Versions

Daniel 11 in the ANGEFD

Daniel 11 in the ANTPNG2D

Daniel 11 in the AS21

Daniel 11 in the BAGH

Daniel 11 in the BBPNG

Daniel 11 in the BBT1E

Daniel 11 in the BDS

Daniel 11 in the BEV

Daniel 11 in the BHAD

Daniel 11 in the BIB

Daniel 11 in the BLPT

Daniel 11 in the BNT

Daniel 11 in the BNTABOOT

Daniel 11 in the BNTLV

Daniel 11 in the BOATCB

Daniel 11 in the BOATCB2

Daniel 11 in the BOBCV

Daniel 11 in the BOCNT

Daniel 11 in the BOECS

Daniel 11 in the BOHCB

Daniel 11 in the BOHCV

Daniel 11 in the BOHLNT

Daniel 11 in the BOHNTLTAL

Daniel 11 in the BOICB

Daniel 11 in the BOILNTAP

Daniel 11 in the BOITCV

Daniel 11 in the BOKCV

Daniel 11 in the BOKCV2

Daniel 11 in the BOKHWOG

Daniel 11 in the BOKSSV

Daniel 11 in the BOLCB

Daniel 11 in the BOLCB2

Daniel 11 in the BOMCV

Daniel 11 in the BONAV

Daniel 11 in the BONCB

Daniel 11 in the BONLT

Daniel 11 in the BONUT2

Daniel 11 in the BOPLNT

Daniel 11 in the BOSCB

Daniel 11 in the BOSNC

Daniel 11 in the BOTLNT

Daniel 11 in the BOVCB

Daniel 11 in the BOYCB

Daniel 11 in the BPBB

Daniel 11 in the BPH

Daniel 11 in the BSB

Daniel 11 in the CCB

Daniel 11 in the CUV

Daniel 11 in the CUVS

Daniel 11 in the DBT

Daniel 11 in the DGDNT

Daniel 11 in the DHNT

Daniel 11 in the DNT

Daniel 11 in the ELBE

Daniel 11 in the EMTV

Daniel 11 in the ESV

Daniel 11 in the FBV

Daniel 11 in the FEB

Daniel 11 in the GGMNT

Daniel 11 in the GNT

Daniel 11 in the HARY

Daniel 11 in the HNT

Daniel 11 in the IRVA

Daniel 11 in the IRVB

Daniel 11 in the IRVG

Daniel 11 in the IRVH

Daniel 11 in the IRVK

Daniel 11 in the IRVM

Daniel 11 in the IRVM2

Daniel 11 in the IRVO

Daniel 11 in the IRVP

Daniel 11 in the IRVT

Daniel 11 in the IRVT2

Daniel 11 in the IRVU

Daniel 11 in the ISVN

Daniel 11 in the JSNT

Daniel 11 in the KAPI

Daniel 11 in the KBT1ETNIK

Daniel 11 in the KBV

Daniel 11 in the KJV

Daniel 11 in the KNFD

Daniel 11 in the LBA

Daniel 11 in the LBLA

Daniel 11 in the LNT

Daniel 11 in the LSV

Daniel 11 in the MAAL

Daniel 11 in the MBV

Daniel 11 in the MBV2

Daniel 11 in the MHNT

Daniel 11 in the MKNFD

Daniel 11 in the MNG

Daniel 11 in the MNT

Daniel 11 in the MNT2

Daniel 11 in the MRS1T

Daniel 11 in the NAA

Daniel 11 in the NASB

Daniel 11 in the NBLA

Daniel 11 in the NBS

Daniel 11 in the NBVTP

Daniel 11 in the NET2

Daniel 11 in the NIV11

Daniel 11 in the NNT

Daniel 11 in the NNT2

Daniel 11 in the NNT3

Daniel 11 in the PDDPT

Daniel 11 in the PFNT

Daniel 11 in the RMNT

Daniel 11 in the SBIAS

Daniel 11 in the SBIBS

Daniel 11 in the SBIBS2

Daniel 11 in the SBICS

Daniel 11 in the SBIDS

Daniel 11 in the SBIGS

Daniel 11 in the SBIHS

Daniel 11 in the SBIIS

Daniel 11 in the SBIIS2

Daniel 11 in the SBIIS3

Daniel 11 in the SBIKS

Daniel 11 in the SBIKS2

Daniel 11 in the SBIMS

Daniel 11 in the SBIOS

Daniel 11 in the SBIPS

Daniel 11 in the SBISS

Daniel 11 in the SBITS

Daniel 11 in the SBITS2

Daniel 11 in the SBITS3

Daniel 11 in the SBITS4

Daniel 11 in the SBIUS

Daniel 11 in the SBIVS

Daniel 11 in the SBT

Daniel 11 in the SBT1E

Daniel 11 in the SCHL

Daniel 11 in the SNT

Daniel 11 in the SUSU

Daniel 11 in the SUSU2

Daniel 11 in the SYNO

Daniel 11 in the TBIAOTANT

Daniel 11 in the TBT1E

Daniel 11 in the TBT1E2

Daniel 11 in the TFTIP

Daniel 11 in the TFTU

Daniel 11 in the TGNTATF3T

Daniel 11 in the THAI

Daniel 11 in the TNFD

Daniel 11 in the TNT

Daniel 11 in the TNTIK

Daniel 11 in the TNTIL

Daniel 11 in the TNTIN

Daniel 11 in the TNTIP

Daniel 11 in the TNTIZ

Daniel 11 in the TOMA

Daniel 11 in the TTENT

Daniel 11 in the UBG

Daniel 11 in the UGV

Daniel 11 in the UGV2

Daniel 11 in the UGV3

Daniel 11 in the VBL

Daniel 11 in the VDCC

Daniel 11 in the YALU

Daniel 11 in the YAPE

Daniel 11 in the YBVTP

Daniel 11 in the ZBP