Daniel 3 (BOGWICC)

1 Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. 2 Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija. 3 Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati: 4 “Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse 5 mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. 6 Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.” 7 Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. 8 Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda. 9 Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 10 Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, 11 ndi kuti aliyense osalambira ndi kupembedza adzaponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.” 13 Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, 14 ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? 15 Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?” 16 Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. 17 Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. 18 Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.” 19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, 20 ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. 21 Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 22 Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, 23 ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto. 24 Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?”Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.” 25 Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.” 26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!”Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, 27 ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto. 28 Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo. 29 Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.” 30 Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni.

In Other Versions

Daniel 3 in the ANGEFD

Daniel 3 in the ANTPNG2D

Daniel 3 in the AS21

Daniel 3 in the BAGH

Daniel 3 in the BBPNG

Daniel 3 in the BBT1E

Daniel 3 in the BDS

Daniel 3 in the BEV

Daniel 3 in the BHAD

Daniel 3 in the BIB

Daniel 3 in the BLPT

Daniel 3 in the BNT

Daniel 3 in the BNTABOOT

Daniel 3 in the BNTLV

Daniel 3 in the BOATCB

Daniel 3 in the BOATCB2

Daniel 3 in the BOBCV

Daniel 3 in the BOCNT

Daniel 3 in the BOECS

Daniel 3 in the BOHCB

Daniel 3 in the BOHCV

Daniel 3 in the BOHLNT

Daniel 3 in the BOHNTLTAL

Daniel 3 in the BOICB

Daniel 3 in the BOILNTAP

Daniel 3 in the BOITCV

Daniel 3 in the BOKCV

Daniel 3 in the BOKCV2

Daniel 3 in the BOKHWOG

Daniel 3 in the BOKSSV

Daniel 3 in the BOLCB

Daniel 3 in the BOLCB2

Daniel 3 in the BOMCV

Daniel 3 in the BONAV

Daniel 3 in the BONCB

Daniel 3 in the BONLT

Daniel 3 in the BONUT2

Daniel 3 in the BOPLNT

Daniel 3 in the BOSCB

Daniel 3 in the BOSNC

Daniel 3 in the BOTLNT

Daniel 3 in the BOVCB

Daniel 3 in the BOYCB

Daniel 3 in the BPBB

Daniel 3 in the BPH

Daniel 3 in the BSB

Daniel 3 in the CCB

Daniel 3 in the CUV

Daniel 3 in the CUVS

Daniel 3 in the DBT

Daniel 3 in the DGDNT

Daniel 3 in the DHNT

Daniel 3 in the DNT

Daniel 3 in the ELBE

Daniel 3 in the EMTV

Daniel 3 in the ESV

Daniel 3 in the FBV

Daniel 3 in the FEB

Daniel 3 in the GGMNT

Daniel 3 in the GNT

Daniel 3 in the HARY

Daniel 3 in the HNT

Daniel 3 in the IRVA

Daniel 3 in the IRVB

Daniel 3 in the IRVG

Daniel 3 in the IRVH

Daniel 3 in the IRVK

Daniel 3 in the IRVM

Daniel 3 in the IRVM2

Daniel 3 in the IRVO

Daniel 3 in the IRVP

Daniel 3 in the IRVT

Daniel 3 in the IRVT2

Daniel 3 in the IRVU

Daniel 3 in the ISVN

Daniel 3 in the JSNT

Daniel 3 in the KAPI

Daniel 3 in the KBT1ETNIK

Daniel 3 in the KBV

Daniel 3 in the KJV

Daniel 3 in the KNFD

Daniel 3 in the LBA

Daniel 3 in the LBLA

Daniel 3 in the LNT

Daniel 3 in the LSV

Daniel 3 in the MAAL

Daniel 3 in the MBV

Daniel 3 in the MBV2

Daniel 3 in the MHNT

Daniel 3 in the MKNFD

Daniel 3 in the MNG

Daniel 3 in the MNT

Daniel 3 in the MNT2

Daniel 3 in the MRS1T

Daniel 3 in the NAA

Daniel 3 in the NASB

Daniel 3 in the NBLA

Daniel 3 in the NBS

Daniel 3 in the NBVTP

Daniel 3 in the NET2

Daniel 3 in the NIV11

Daniel 3 in the NNT

Daniel 3 in the NNT2

Daniel 3 in the NNT3

Daniel 3 in the PDDPT

Daniel 3 in the PFNT

Daniel 3 in the RMNT

Daniel 3 in the SBIAS

Daniel 3 in the SBIBS

Daniel 3 in the SBIBS2

Daniel 3 in the SBICS

Daniel 3 in the SBIDS

Daniel 3 in the SBIGS

Daniel 3 in the SBIHS

Daniel 3 in the SBIIS

Daniel 3 in the SBIIS2

Daniel 3 in the SBIIS3

Daniel 3 in the SBIKS

Daniel 3 in the SBIKS2

Daniel 3 in the SBIMS

Daniel 3 in the SBIOS

Daniel 3 in the SBIPS

Daniel 3 in the SBISS

Daniel 3 in the SBITS

Daniel 3 in the SBITS2

Daniel 3 in the SBITS3

Daniel 3 in the SBITS4

Daniel 3 in the SBIUS

Daniel 3 in the SBIVS

Daniel 3 in the SBT

Daniel 3 in the SBT1E

Daniel 3 in the SCHL

Daniel 3 in the SNT

Daniel 3 in the SUSU

Daniel 3 in the SUSU2

Daniel 3 in the SYNO

Daniel 3 in the TBIAOTANT

Daniel 3 in the TBT1E

Daniel 3 in the TBT1E2

Daniel 3 in the TFTIP

Daniel 3 in the TFTU

Daniel 3 in the TGNTATF3T

Daniel 3 in the THAI

Daniel 3 in the TNFD

Daniel 3 in the TNT

Daniel 3 in the TNTIK

Daniel 3 in the TNTIL

Daniel 3 in the TNTIN

Daniel 3 in the TNTIP

Daniel 3 in the TNTIZ

Daniel 3 in the TOMA

Daniel 3 in the TTENT

Daniel 3 in the UBG

Daniel 3 in the UGV

Daniel 3 in the UGV2

Daniel 3 in the UGV3

Daniel 3 in the VBL

Daniel 3 in the VDCC

Daniel 3 in the YALU

Daniel 3 in the YAPE

Daniel 3 in the YBVTP

Daniel 3 in the ZBP