Deuteronomy 1 (BOGWICC)

1 Awa ndi mawu amene Mose anayankhula kwa Aisraeli onse mʼchipululu kummawa kwa Yorodani, ku Araba moyangʼanana ndi Sufi, pakati pa Parani ndi Tofeli, Labani, Heziroti ndi Dizahabu. 2 (Kuyenda kuchokera ku Horebu kukafika ku Kadesi Barinea kudzera njira ya ku Phiri la Seiri ndi ulendo wa masiku khumi ndi limodzi). 3 Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo. 4 Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti. 5 Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti: 6 Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino. 7 Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 8 Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.” 9 Pa nthawi imeneyi ine ndinati kwa inu, “Inu ndinu katundu olemera kwambiri woti sindingathe kumunyamula ndekha. 10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani kotero kuti lero lino ndinu ochuluka ngati nyenyezi za kumwamba. 11 Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera! 12 Koma nanga ndekha ndidzasenza bwanji zovuta ndi zipsinjo zanu komanso milandu yanu? 13 Sankhani amuna ena anzeru, ozindikira ndi amene mumawalemekeza kuchokera ku mtundu uliwonse wa mitundu yanu, ndipo ndidzawayika kuti akulamulireni.” 14 Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.” 15 Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko. 16 Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo. 17 Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.” 18 Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita. 19 Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea. 20 Ndipo ndinati kwa inu, “Mwafika ku dziko la mapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa. 21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.” 22 Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.” 23 Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse. 24 Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo. 25 Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.” 26 Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu. 27 Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge. 28 Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’ ” 29 Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa. 30 Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona, 31 ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.” 32 Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu 33 amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo. 34 Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti, 35 “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu, 36 kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.” 37 Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo. 38 Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo. 39 Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo. 40 Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.” 41 Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija. 42 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’ ” 43 Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri. 44 Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima. 45 Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni. 46 Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.

In Other Versions

Deuteronomy 1 in the ANGEFD

Deuteronomy 1 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 1 in the AS21

Deuteronomy 1 in the BAGH

Deuteronomy 1 in the BBPNG

Deuteronomy 1 in the BBT1E

Deuteronomy 1 in the BDS

Deuteronomy 1 in the BEV

Deuteronomy 1 in the BHAD

Deuteronomy 1 in the BIB

Deuteronomy 1 in the BLPT

Deuteronomy 1 in the BNT

Deuteronomy 1 in the BNTABOOT

Deuteronomy 1 in the BNTLV

Deuteronomy 1 in the BOATCB

Deuteronomy 1 in the BOATCB2

Deuteronomy 1 in the BOBCV

Deuteronomy 1 in the BOCNT

Deuteronomy 1 in the BOECS

Deuteronomy 1 in the BOHCB

Deuteronomy 1 in the BOHCV

Deuteronomy 1 in the BOHLNT

Deuteronomy 1 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 1 in the BOICB

Deuteronomy 1 in the BOILNTAP

Deuteronomy 1 in the BOITCV

Deuteronomy 1 in the BOKCV

Deuteronomy 1 in the BOKCV2

Deuteronomy 1 in the BOKHWOG

Deuteronomy 1 in the BOKSSV

Deuteronomy 1 in the BOLCB

Deuteronomy 1 in the BOLCB2

Deuteronomy 1 in the BOMCV

Deuteronomy 1 in the BONAV

Deuteronomy 1 in the BONCB

Deuteronomy 1 in the BONLT

Deuteronomy 1 in the BONUT2

Deuteronomy 1 in the BOPLNT

Deuteronomy 1 in the BOSCB

Deuteronomy 1 in the BOSNC

Deuteronomy 1 in the BOTLNT

Deuteronomy 1 in the BOVCB

Deuteronomy 1 in the BOYCB

Deuteronomy 1 in the BPBB

Deuteronomy 1 in the BPH

Deuteronomy 1 in the BSB

Deuteronomy 1 in the CCB

Deuteronomy 1 in the CUV

Deuteronomy 1 in the CUVS

Deuteronomy 1 in the DBT

Deuteronomy 1 in the DGDNT

Deuteronomy 1 in the DHNT

Deuteronomy 1 in the DNT

Deuteronomy 1 in the ELBE

Deuteronomy 1 in the EMTV

Deuteronomy 1 in the ESV

Deuteronomy 1 in the FBV

Deuteronomy 1 in the FEB

Deuteronomy 1 in the GGMNT

Deuteronomy 1 in the GNT

Deuteronomy 1 in the HARY

Deuteronomy 1 in the HNT

Deuteronomy 1 in the IRVA

Deuteronomy 1 in the IRVB

Deuteronomy 1 in the IRVG

Deuteronomy 1 in the IRVH

Deuteronomy 1 in the IRVK

Deuteronomy 1 in the IRVM

Deuteronomy 1 in the IRVM2

Deuteronomy 1 in the IRVO

Deuteronomy 1 in the IRVP

Deuteronomy 1 in the IRVT

Deuteronomy 1 in the IRVT2

Deuteronomy 1 in the IRVU

Deuteronomy 1 in the ISVN

Deuteronomy 1 in the JSNT

Deuteronomy 1 in the KAPI

Deuteronomy 1 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 1 in the KBV

Deuteronomy 1 in the KJV

Deuteronomy 1 in the KNFD

Deuteronomy 1 in the LBA

Deuteronomy 1 in the LBLA

Deuteronomy 1 in the LNT

Deuteronomy 1 in the LSV

Deuteronomy 1 in the MAAL

Deuteronomy 1 in the MBV

Deuteronomy 1 in the MBV2

Deuteronomy 1 in the MHNT

Deuteronomy 1 in the MKNFD

Deuteronomy 1 in the MNG

Deuteronomy 1 in the MNT

Deuteronomy 1 in the MNT2

Deuteronomy 1 in the MRS1T

Deuteronomy 1 in the NAA

Deuteronomy 1 in the NASB

Deuteronomy 1 in the NBLA

Deuteronomy 1 in the NBS

Deuteronomy 1 in the NBVTP

Deuteronomy 1 in the NET2

Deuteronomy 1 in the NIV11

Deuteronomy 1 in the NNT

Deuteronomy 1 in the NNT2

Deuteronomy 1 in the NNT3

Deuteronomy 1 in the PDDPT

Deuteronomy 1 in the PFNT

Deuteronomy 1 in the RMNT

Deuteronomy 1 in the SBIAS

Deuteronomy 1 in the SBIBS

Deuteronomy 1 in the SBIBS2

Deuteronomy 1 in the SBICS

Deuteronomy 1 in the SBIDS

Deuteronomy 1 in the SBIGS

Deuteronomy 1 in the SBIHS

Deuteronomy 1 in the SBIIS

Deuteronomy 1 in the SBIIS2

Deuteronomy 1 in the SBIIS3

Deuteronomy 1 in the SBIKS

Deuteronomy 1 in the SBIKS2

Deuteronomy 1 in the SBIMS

Deuteronomy 1 in the SBIOS

Deuteronomy 1 in the SBIPS

Deuteronomy 1 in the SBISS

Deuteronomy 1 in the SBITS

Deuteronomy 1 in the SBITS2

Deuteronomy 1 in the SBITS3

Deuteronomy 1 in the SBITS4

Deuteronomy 1 in the SBIUS

Deuteronomy 1 in the SBIVS

Deuteronomy 1 in the SBT

Deuteronomy 1 in the SBT1E

Deuteronomy 1 in the SCHL

Deuteronomy 1 in the SNT

Deuteronomy 1 in the SUSU

Deuteronomy 1 in the SUSU2

Deuteronomy 1 in the SYNO

Deuteronomy 1 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 1 in the TBT1E

Deuteronomy 1 in the TBT1E2

Deuteronomy 1 in the TFTIP

Deuteronomy 1 in the TFTU

Deuteronomy 1 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 1 in the THAI

Deuteronomy 1 in the TNFD

Deuteronomy 1 in the TNT

Deuteronomy 1 in the TNTIK

Deuteronomy 1 in the TNTIL

Deuteronomy 1 in the TNTIN

Deuteronomy 1 in the TNTIP

Deuteronomy 1 in the TNTIZ

Deuteronomy 1 in the TOMA

Deuteronomy 1 in the TTENT

Deuteronomy 1 in the UBG

Deuteronomy 1 in the UGV

Deuteronomy 1 in the UGV2

Deuteronomy 1 in the UGV3

Deuteronomy 1 in the VBL

Deuteronomy 1 in the VDCC

Deuteronomy 1 in the YALU

Deuteronomy 1 in the YAPE

Deuteronomy 1 in the YBVTP

Deuteronomy 1 in the ZBP