Ecclesiastes 8 (BOGWICC)
1 Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu?Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthundipo imasintha maonekedwe ake awukali. 2 Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu. 3 Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho. 4 Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?” 5 Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse,ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake. 6 Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse,ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri. 7 Popeza palibe munthu amene amadziwa zamʼtsogolo,ndani angamuwuze zomwe zidzachitika mʼtsogolo? 8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yolamulira mpweya wa moyo kuti athe kuwusunga,choncho palibe amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa yake.Nkhondo sithawika; tsono anthu ochita zoyipa,kuyipa kwawoko sikudzawapulumutsa. 9 Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza. 10 Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake. 11 Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa. 12 Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu. 13 Koma popeza oyipa saopa Mulungu zinthu sizidzawayendera bwino, ndipo moyo wawo sudzakhalitsa monga mthunzi. 14 Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. 15 Nʼchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake amene Mulungu wamupatsa pansi pano. 16 Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku, 17 pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.
In Other Versions
Ecclesiastes 8 in the ANGEFD
Ecclesiastes 8 in the ANTPNG2D
Ecclesiastes 8 in the AS21
Ecclesiastes 8 in the BAGH
Ecclesiastes 8 in the BBPNG
Ecclesiastes 8 in the BBT1E
Ecclesiastes 8 in the BDS
Ecclesiastes 8 in the BEV
Ecclesiastes 8 in the BHAD
Ecclesiastes 8 in the BIB
Ecclesiastes 8 in the BLPT
Ecclesiastes 8 in the BNT
Ecclesiastes 8 in the BNTABOOT
Ecclesiastes 8 in the BNTLV
Ecclesiastes 8 in the BOATCB
Ecclesiastes 8 in the BOATCB2
Ecclesiastes 8 in the BOBCV
Ecclesiastes 8 in the BOCNT
Ecclesiastes 8 in the BOECS
Ecclesiastes 8 in the BOHCB
Ecclesiastes 8 in the BOHCV
Ecclesiastes 8 in the BOHLNT
Ecclesiastes 8 in the BOHNTLTAL
Ecclesiastes 8 in the BOICB
Ecclesiastes 8 in the BOILNTAP
Ecclesiastes 8 in the BOITCV
Ecclesiastes 8 in the BOKCV
Ecclesiastes 8 in the BOKCV2
Ecclesiastes 8 in the BOKHWOG
Ecclesiastes 8 in the BOKSSV
Ecclesiastes 8 in the BOLCB
Ecclesiastes 8 in the BOLCB2
Ecclesiastes 8 in the BOMCV
Ecclesiastes 8 in the BONAV
Ecclesiastes 8 in the BONCB
Ecclesiastes 8 in the BONLT
Ecclesiastes 8 in the BONUT2
Ecclesiastes 8 in the BOPLNT
Ecclesiastes 8 in the BOSCB
Ecclesiastes 8 in the BOSNC
Ecclesiastes 8 in the BOTLNT
Ecclesiastes 8 in the BOVCB
Ecclesiastes 8 in the BOYCB
Ecclesiastes 8 in the BPBB
Ecclesiastes 8 in the BPH
Ecclesiastes 8 in the BSB
Ecclesiastes 8 in the CCB
Ecclesiastes 8 in the CUV
Ecclesiastes 8 in the CUVS
Ecclesiastes 8 in the DBT
Ecclesiastes 8 in the DGDNT
Ecclesiastes 8 in the DHNT
Ecclesiastes 8 in the DNT
Ecclesiastes 8 in the ELBE
Ecclesiastes 8 in the EMTV
Ecclesiastes 8 in the ESV
Ecclesiastes 8 in the FBV
Ecclesiastes 8 in the FEB
Ecclesiastes 8 in the GGMNT
Ecclesiastes 8 in the GNT
Ecclesiastes 8 in the HARY
Ecclesiastes 8 in the HNT
Ecclesiastes 8 in the IRVA
Ecclesiastes 8 in the IRVB
Ecclesiastes 8 in the IRVG
Ecclesiastes 8 in the IRVH
Ecclesiastes 8 in the IRVK
Ecclesiastes 8 in the IRVM
Ecclesiastes 8 in the IRVM2
Ecclesiastes 8 in the IRVO
Ecclesiastes 8 in the IRVP
Ecclesiastes 8 in the IRVT
Ecclesiastes 8 in the IRVT2
Ecclesiastes 8 in the IRVU
Ecclesiastes 8 in the ISVN
Ecclesiastes 8 in the JSNT
Ecclesiastes 8 in the KAPI
Ecclesiastes 8 in the KBT1ETNIK
Ecclesiastes 8 in the KBV
Ecclesiastes 8 in the KJV
Ecclesiastes 8 in the KNFD
Ecclesiastes 8 in the LBA
Ecclesiastes 8 in the LBLA
Ecclesiastes 8 in the LNT
Ecclesiastes 8 in the LSV
Ecclesiastes 8 in the MAAL
Ecclesiastes 8 in the MBV
Ecclesiastes 8 in the MBV2
Ecclesiastes 8 in the MHNT
Ecclesiastes 8 in the MKNFD
Ecclesiastes 8 in the MNG
Ecclesiastes 8 in the MNT
Ecclesiastes 8 in the MNT2
Ecclesiastes 8 in the MRS1T
Ecclesiastes 8 in the NAA
Ecclesiastes 8 in the NASB
Ecclesiastes 8 in the NBLA
Ecclesiastes 8 in the NBS
Ecclesiastes 8 in the NBVTP
Ecclesiastes 8 in the NET2
Ecclesiastes 8 in the NIV11
Ecclesiastes 8 in the NNT
Ecclesiastes 8 in the NNT2
Ecclesiastes 8 in the NNT3
Ecclesiastes 8 in the PDDPT
Ecclesiastes 8 in the PFNT
Ecclesiastes 8 in the RMNT
Ecclesiastes 8 in the SBIAS
Ecclesiastes 8 in the SBIBS
Ecclesiastes 8 in the SBIBS2
Ecclesiastes 8 in the SBICS
Ecclesiastes 8 in the SBIDS
Ecclesiastes 8 in the SBIGS
Ecclesiastes 8 in the SBIHS
Ecclesiastes 8 in the SBIIS
Ecclesiastes 8 in the SBIIS2
Ecclesiastes 8 in the SBIIS3
Ecclesiastes 8 in the SBIKS
Ecclesiastes 8 in the SBIKS2
Ecclesiastes 8 in the SBIMS
Ecclesiastes 8 in the SBIOS
Ecclesiastes 8 in the SBIPS
Ecclesiastes 8 in the SBISS
Ecclesiastes 8 in the SBITS
Ecclesiastes 8 in the SBITS2
Ecclesiastes 8 in the SBITS3
Ecclesiastes 8 in the SBITS4
Ecclesiastes 8 in the SBIUS
Ecclesiastes 8 in the SBIVS
Ecclesiastes 8 in the SBT
Ecclesiastes 8 in the SBT1E
Ecclesiastes 8 in the SCHL
Ecclesiastes 8 in the SNT
Ecclesiastes 8 in the SUSU
Ecclesiastes 8 in the SUSU2
Ecclesiastes 8 in the SYNO
Ecclesiastes 8 in the TBIAOTANT
Ecclesiastes 8 in the TBT1E
Ecclesiastes 8 in the TBT1E2
Ecclesiastes 8 in the TFTIP
Ecclesiastes 8 in the TFTU
Ecclesiastes 8 in the TGNTATF3T
Ecclesiastes 8 in the THAI
Ecclesiastes 8 in the TNFD
Ecclesiastes 8 in the TNT
Ecclesiastes 8 in the TNTIK
Ecclesiastes 8 in the TNTIL
Ecclesiastes 8 in the TNTIN
Ecclesiastes 8 in the TNTIP
Ecclesiastes 8 in the TNTIZ
Ecclesiastes 8 in the TOMA
Ecclesiastes 8 in the TTENT
Ecclesiastes 8 in the UBG
Ecclesiastes 8 in the UGV
Ecclesiastes 8 in the UGV2
Ecclesiastes 8 in the UGV3
Ecclesiastes 8 in the VBL
Ecclesiastes 8 in the VDCC
Ecclesiastes 8 in the YALU
Ecclesiastes 8 in the YAPE
Ecclesiastes 8 in the YBVTP
Ecclesiastes 8 in the ZBP