Esther 9 (BOGWICC)

1 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. 2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. 3 Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. 4 Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe. 5 Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. 6 Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. 7 Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo. 11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.” 13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.” 14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo. 16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero. 18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero. 19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso. 20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka. 23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira. 29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.

In Other Versions

Esther 9 in the ANGEFD

Esther 9 in the ANTPNG2D

Esther 9 in the AS21

Esther 9 in the BAGH

Esther 9 in the BBPNG

Esther 9 in the BBT1E

Esther 9 in the BDS

Esther 9 in the BEV

Esther 9 in the BHAD

Esther 9 in the BIB

Esther 9 in the BLPT

Esther 9 in the BNT

Esther 9 in the BNTABOOT

Esther 9 in the BNTLV

Esther 9 in the BOATCB

Esther 9 in the BOATCB2

Esther 9 in the BOBCV

Esther 9 in the BOCNT

Esther 9 in the BOECS

Esther 9 in the BOHCB

Esther 9 in the BOHCV

Esther 9 in the BOHLNT

Esther 9 in the BOHNTLTAL

Esther 9 in the BOICB

Esther 9 in the BOILNTAP

Esther 9 in the BOITCV

Esther 9 in the BOKCV

Esther 9 in the BOKCV2

Esther 9 in the BOKHWOG

Esther 9 in the BOKSSV

Esther 9 in the BOLCB

Esther 9 in the BOLCB2

Esther 9 in the BOMCV

Esther 9 in the BONAV

Esther 9 in the BONCB

Esther 9 in the BONLT

Esther 9 in the BONUT2

Esther 9 in the BOPLNT

Esther 9 in the BOSCB

Esther 9 in the BOSNC

Esther 9 in the BOTLNT

Esther 9 in the BOVCB

Esther 9 in the BOYCB

Esther 9 in the BPBB

Esther 9 in the BPH

Esther 9 in the BSB

Esther 9 in the CCB

Esther 9 in the CUV

Esther 9 in the CUVS

Esther 9 in the DBT

Esther 9 in the DGDNT

Esther 9 in the DHNT

Esther 9 in the DNT

Esther 9 in the ELBE

Esther 9 in the EMTV

Esther 9 in the ESV

Esther 9 in the FBV

Esther 9 in the FEB

Esther 9 in the GGMNT

Esther 9 in the GNT

Esther 9 in the HARY

Esther 9 in the HNT

Esther 9 in the IRVA

Esther 9 in the IRVB

Esther 9 in the IRVG

Esther 9 in the IRVH

Esther 9 in the IRVK

Esther 9 in the IRVM

Esther 9 in the IRVM2

Esther 9 in the IRVO

Esther 9 in the IRVP

Esther 9 in the IRVT

Esther 9 in the IRVT2

Esther 9 in the IRVU

Esther 9 in the ISVN

Esther 9 in the JSNT

Esther 9 in the KAPI

Esther 9 in the KBT1ETNIK

Esther 9 in the KBV

Esther 9 in the KJV

Esther 9 in the KNFD

Esther 9 in the LBA

Esther 9 in the LBLA

Esther 9 in the LNT

Esther 9 in the LSV

Esther 9 in the MAAL

Esther 9 in the MBV

Esther 9 in the MBV2

Esther 9 in the MHNT

Esther 9 in the MKNFD

Esther 9 in the MNG

Esther 9 in the MNT

Esther 9 in the MNT2

Esther 9 in the MRS1T

Esther 9 in the NAA

Esther 9 in the NASB

Esther 9 in the NBLA

Esther 9 in the NBS

Esther 9 in the NBVTP

Esther 9 in the NET2

Esther 9 in the NIV11

Esther 9 in the NNT

Esther 9 in the NNT2

Esther 9 in the NNT3

Esther 9 in the PDDPT

Esther 9 in the PFNT

Esther 9 in the RMNT

Esther 9 in the SBIAS

Esther 9 in the SBIBS

Esther 9 in the SBIBS2

Esther 9 in the SBICS

Esther 9 in the SBIDS

Esther 9 in the SBIGS

Esther 9 in the SBIHS

Esther 9 in the SBIIS

Esther 9 in the SBIIS2

Esther 9 in the SBIIS3

Esther 9 in the SBIKS

Esther 9 in the SBIKS2

Esther 9 in the SBIMS

Esther 9 in the SBIOS

Esther 9 in the SBIPS

Esther 9 in the SBISS

Esther 9 in the SBITS

Esther 9 in the SBITS2

Esther 9 in the SBITS3

Esther 9 in the SBITS4

Esther 9 in the SBIUS

Esther 9 in the SBIVS

Esther 9 in the SBT

Esther 9 in the SBT1E

Esther 9 in the SCHL

Esther 9 in the SNT

Esther 9 in the SUSU

Esther 9 in the SUSU2

Esther 9 in the SYNO

Esther 9 in the TBIAOTANT

Esther 9 in the TBT1E

Esther 9 in the TBT1E2

Esther 9 in the TFTIP

Esther 9 in the TFTU

Esther 9 in the TGNTATF3T

Esther 9 in the THAI

Esther 9 in the TNFD

Esther 9 in the TNT

Esther 9 in the TNTIK

Esther 9 in the TNTIL

Esther 9 in the TNTIN

Esther 9 in the TNTIP

Esther 9 in the TNTIZ

Esther 9 in the TOMA

Esther 9 in the TTENT

Esther 9 in the UBG

Esther 9 in the UGV

Esther 9 in the UGV2

Esther 9 in the UGV3

Esther 9 in the VBL

Esther 9 in the VDCC

Esther 9 in the YALU

Esther 9 in the YAPE

Esther 9 in the YBVTP

Esther 9 in the ZBP