Exodus 31 (BOGWICC)
1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 2 “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. 3 Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 4 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 5 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. 6 Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi: 7 Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti, 8 tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani, 9 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake, 10 ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe, 11 ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.” 12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 13 “Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani. 14 “Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake. 15 Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. 16 Aisraeli onse komanso zidzukulu zawo mʼtsogolo azidzasunga tsiku la Sabata ngati pangano lamuyaya. 17 Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.” 18 Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.
In Other Versions
Exodus 31 in the ANGEFD
Exodus 31 in the ANTPNG2D
Exodus 31 in the AS21
Exodus 31 in the BAGH
Exodus 31 in the BBPNG
Exodus 31 in the BBT1E
Exodus 31 in the BDS
Exodus 31 in the BEV
Exodus 31 in the BHAD
Exodus 31 in the BIB
Exodus 31 in the BLPT
Exodus 31 in the BNT
Exodus 31 in the BNTABOOT
Exodus 31 in the BNTLV
Exodus 31 in the BOATCB
Exodus 31 in the BOATCB2
Exodus 31 in the BOBCV
Exodus 31 in the BOCNT
Exodus 31 in the BOECS
Exodus 31 in the BOHCB
Exodus 31 in the BOHCV
Exodus 31 in the BOHLNT
Exodus 31 in the BOHNTLTAL
Exodus 31 in the BOICB
Exodus 31 in the BOILNTAP
Exodus 31 in the BOITCV
Exodus 31 in the BOKCV
Exodus 31 in the BOKCV2
Exodus 31 in the BOKHWOG
Exodus 31 in the BOKSSV
Exodus 31 in the BOLCB
Exodus 31 in the BOLCB2
Exodus 31 in the BOMCV
Exodus 31 in the BONAV
Exodus 31 in the BONCB
Exodus 31 in the BONLT
Exodus 31 in the BONUT2
Exodus 31 in the BOPLNT
Exodus 31 in the BOSCB
Exodus 31 in the BOSNC
Exodus 31 in the BOTLNT
Exodus 31 in the BOVCB
Exodus 31 in the BOYCB
Exodus 31 in the BPBB
Exodus 31 in the BPH
Exodus 31 in the BSB
Exodus 31 in the CCB
Exodus 31 in the CUV
Exodus 31 in the CUVS
Exodus 31 in the DBT
Exodus 31 in the DGDNT
Exodus 31 in the DHNT
Exodus 31 in the DNT
Exodus 31 in the ELBE
Exodus 31 in the EMTV
Exodus 31 in the ESV
Exodus 31 in the FBV
Exodus 31 in the FEB
Exodus 31 in the GGMNT
Exodus 31 in the GNT
Exodus 31 in the HARY
Exodus 31 in the HNT
Exodus 31 in the IRVA
Exodus 31 in the IRVB
Exodus 31 in the IRVG
Exodus 31 in the IRVH
Exodus 31 in the IRVK
Exodus 31 in the IRVM
Exodus 31 in the IRVM2
Exodus 31 in the IRVO
Exodus 31 in the IRVP
Exodus 31 in the IRVT
Exodus 31 in the IRVT2
Exodus 31 in the IRVU
Exodus 31 in the ISVN
Exodus 31 in the JSNT
Exodus 31 in the KAPI
Exodus 31 in the KBT1ETNIK
Exodus 31 in the KBV
Exodus 31 in the KJV
Exodus 31 in the KNFD
Exodus 31 in the LBA
Exodus 31 in the LBLA
Exodus 31 in the LNT
Exodus 31 in the LSV
Exodus 31 in the MAAL
Exodus 31 in the MBV
Exodus 31 in the MBV2
Exodus 31 in the MHNT
Exodus 31 in the MKNFD
Exodus 31 in the MNG
Exodus 31 in the MNT
Exodus 31 in the MNT2
Exodus 31 in the MRS1T
Exodus 31 in the NAA
Exodus 31 in the NASB
Exodus 31 in the NBLA
Exodus 31 in the NBS
Exodus 31 in the NBVTP
Exodus 31 in the NET2
Exodus 31 in the NIV11
Exodus 31 in the NNT
Exodus 31 in the NNT2
Exodus 31 in the NNT3
Exodus 31 in the PDDPT
Exodus 31 in the PFNT
Exodus 31 in the RMNT
Exodus 31 in the SBIAS
Exodus 31 in the SBIBS
Exodus 31 in the SBIBS2
Exodus 31 in the SBICS
Exodus 31 in the SBIDS
Exodus 31 in the SBIGS
Exodus 31 in the SBIHS
Exodus 31 in the SBIIS
Exodus 31 in the SBIIS2
Exodus 31 in the SBIIS3
Exodus 31 in the SBIKS
Exodus 31 in the SBIKS2
Exodus 31 in the SBIMS
Exodus 31 in the SBIOS
Exodus 31 in the SBIPS
Exodus 31 in the SBISS
Exodus 31 in the SBITS
Exodus 31 in the SBITS2
Exodus 31 in the SBITS3
Exodus 31 in the SBITS4
Exodus 31 in the SBIUS
Exodus 31 in the SBIVS
Exodus 31 in the SBT
Exodus 31 in the SBT1E
Exodus 31 in the SCHL
Exodus 31 in the SNT
Exodus 31 in the SUSU
Exodus 31 in the SUSU2
Exodus 31 in the SYNO
Exodus 31 in the TBIAOTANT
Exodus 31 in the TBT1E
Exodus 31 in the TBT1E2
Exodus 31 in the TFTIP
Exodus 31 in the TFTU
Exodus 31 in the TGNTATF3T
Exodus 31 in the THAI
Exodus 31 in the TNFD
Exodus 31 in the TNT
Exodus 31 in the TNTIK
Exodus 31 in the TNTIL
Exodus 31 in the TNTIN
Exodus 31 in the TNTIP
Exodus 31 in the TNTIZ
Exodus 31 in the TOMA
Exodus 31 in the TTENT
Exodus 31 in the UBG
Exodus 31 in the UGV
Exodus 31 in the UGV2
Exodus 31 in the UGV3
Exodus 31 in the VBL
Exodus 31 in the VDCC
Exodus 31 in the YALU
Exodus 31 in the YAPE
Exodus 31 in the YBVTP
Exodus 31 in the ZBP