Ezekiel 35 (BOGWICC)
1 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo 3 awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu. 4 Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 5 “Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake. 6 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola. 7 Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko. 8 Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse. 9 Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 10 “Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo. 11 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo. 12 Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’ 13 Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva. 14 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja. 15 Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
In Other Versions
Ezekiel 35 in the ANGEFD
Ezekiel 35 in the ANTPNG2D
Ezekiel 35 in the AS21
Ezekiel 35 in the BAGH
Ezekiel 35 in the BBPNG
Ezekiel 35 in the BBT1E
Ezekiel 35 in the BDS
Ezekiel 35 in the BEV
Ezekiel 35 in the BHAD
Ezekiel 35 in the BIB
Ezekiel 35 in the BLPT
Ezekiel 35 in the BNT
Ezekiel 35 in the BNTABOOT
Ezekiel 35 in the BNTLV
Ezekiel 35 in the BOATCB
Ezekiel 35 in the BOATCB2
Ezekiel 35 in the BOBCV
Ezekiel 35 in the BOCNT
Ezekiel 35 in the BOECS
Ezekiel 35 in the BOHCB
Ezekiel 35 in the BOHCV
Ezekiel 35 in the BOHLNT
Ezekiel 35 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 35 in the BOICB
Ezekiel 35 in the BOILNTAP
Ezekiel 35 in the BOITCV
Ezekiel 35 in the BOKCV
Ezekiel 35 in the BOKCV2
Ezekiel 35 in the BOKHWOG
Ezekiel 35 in the BOKSSV
Ezekiel 35 in the BOLCB
Ezekiel 35 in the BOLCB2
Ezekiel 35 in the BOMCV
Ezekiel 35 in the BONAV
Ezekiel 35 in the BONCB
Ezekiel 35 in the BONLT
Ezekiel 35 in the BONUT2
Ezekiel 35 in the BOPLNT
Ezekiel 35 in the BOSCB
Ezekiel 35 in the BOSNC
Ezekiel 35 in the BOTLNT
Ezekiel 35 in the BOVCB
Ezekiel 35 in the BOYCB
Ezekiel 35 in the BPBB
Ezekiel 35 in the BPH
Ezekiel 35 in the BSB
Ezekiel 35 in the CCB
Ezekiel 35 in the CUV
Ezekiel 35 in the CUVS
Ezekiel 35 in the DBT
Ezekiel 35 in the DGDNT
Ezekiel 35 in the DHNT
Ezekiel 35 in the DNT
Ezekiel 35 in the ELBE
Ezekiel 35 in the EMTV
Ezekiel 35 in the ESV
Ezekiel 35 in the FBV
Ezekiel 35 in the FEB
Ezekiel 35 in the GGMNT
Ezekiel 35 in the GNT
Ezekiel 35 in the HARY
Ezekiel 35 in the HNT
Ezekiel 35 in the IRVA
Ezekiel 35 in the IRVB
Ezekiel 35 in the IRVG
Ezekiel 35 in the IRVH
Ezekiel 35 in the IRVK
Ezekiel 35 in the IRVM
Ezekiel 35 in the IRVM2
Ezekiel 35 in the IRVO
Ezekiel 35 in the IRVP
Ezekiel 35 in the IRVT
Ezekiel 35 in the IRVT2
Ezekiel 35 in the IRVU
Ezekiel 35 in the ISVN
Ezekiel 35 in the JSNT
Ezekiel 35 in the KAPI
Ezekiel 35 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 35 in the KBV
Ezekiel 35 in the KJV
Ezekiel 35 in the KNFD
Ezekiel 35 in the LBA
Ezekiel 35 in the LBLA
Ezekiel 35 in the LNT
Ezekiel 35 in the LSV
Ezekiel 35 in the MAAL
Ezekiel 35 in the MBV
Ezekiel 35 in the MBV2
Ezekiel 35 in the MHNT
Ezekiel 35 in the MKNFD
Ezekiel 35 in the MNG
Ezekiel 35 in the MNT
Ezekiel 35 in the MNT2
Ezekiel 35 in the MRS1T
Ezekiel 35 in the NAA
Ezekiel 35 in the NASB
Ezekiel 35 in the NBLA
Ezekiel 35 in the NBS
Ezekiel 35 in the NBVTP
Ezekiel 35 in the NET2
Ezekiel 35 in the NIV11
Ezekiel 35 in the NNT
Ezekiel 35 in the NNT2
Ezekiel 35 in the NNT3
Ezekiel 35 in the PDDPT
Ezekiel 35 in the PFNT
Ezekiel 35 in the RMNT
Ezekiel 35 in the SBIAS
Ezekiel 35 in the SBIBS
Ezekiel 35 in the SBIBS2
Ezekiel 35 in the SBICS
Ezekiel 35 in the SBIDS
Ezekiel 35 in the SBIGS
Ezekiel 35 in the SBIHS
Ezekiel 35 in the SBIIS
Ezekiel 35 in the SBIIS2
Ezekiel 35 in the SBIIS3
Ezekiel 35 in the SBIKS
Ezekiel 35 in the SBIKS2
Ezekiel 35 in the SBIMS
Ezekiel 35 in the SBIOS
Ezekiel 35 in the SBIPS
Ezekiel 35 in the SBISS
Ezekiel 35 in the SBITS
Ezekiel 35 in the SBITS2
Ezekiel 35 in the SBITS3
Ezekiel 35 in the SBITS4
Ezekiel 35 in the SBIUS
Ezekiel 35 in the SBIVS
Ezekiel 35 in the SBT
Ezekiel 35 in the SBT1E
Ezekiel 35 in the SCHL
Ezekiel 35 in the SNT
Ezekiel 35 in the SUSU
Ezekiel 35 in the SUSU2
Ezekiel 35 in the SYNO
Ezekiel 35 in the TBIAOTANT
Ezekiel 35 in the TBT1E
Ezekiel 35 in the TBT1E2
Ezekiel 35 in the TFTIP
Ezekiel 35 in the TFTU
Ezekiel 35 in the TGNTATF3T
Ezekiel 35 in the THAI
Ezekiel 35 in the TNFD
Ezekiel 35 in the TNT
Ezekiel 35 in the TNTIK
Ezekiel 35 in the TNTIL
Ezekiel 35 in the TNTIN
Ezekiel 35 in the TNTIP
Ezekiel 35 in the TNTIZ
Ezekiel 35 in the TOMA
Ezekiel 35 in the TTENT
Ezekiel 35 in the UBG
Ezekiel 35 in the UGV
Ezekiel 35 in the UGV2
Ezekiel 35 in the UGV3
Ezekiel 35 in the VBL
Ezekiel 35 in the VDCC
Ezekiel 35 in the YALU
Ezekiel 35 in the YAPE
Ezekiel 35 in the YBVTP
Ezekiel 35 in the ZBP