Genesis 13 (BOGWICC)

1 Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. 2 Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide. 3 Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, 4 ndiponso kumene Abramu anamangira Yehova guwa lansembe kwa nthawi yoyamba ndi kupemphera mʼdzina la Yehova. 5 Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. 6 Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi. 7 Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo. 8 Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. 9 Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.” 10 Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). 11 Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. 12 Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. 13 Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri. 14 Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. 15 Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya. 16 Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako. 17 Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.” 18 Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.

In Other Versions

Genesis 13 in the ANGEFD

Genesis 13 in the ANTPNG2D

Genesis 13 in the AS21

Genesis 13 in the BAGH

Genesis 13 in the BBPNG

Genesis 13 in the BBT1E

Genesis 13 in the BDS

Genesis 13 in the BEV

Genesis 13 in the BHAD

Genesis 13 in the BIB

Genesis 13 in the BLPT

Genesis 13 in the BNT

Genesis 13 in the BNTABOOT

Genesis 13 in the BNTLV

Genesis 13 in the BOATCB

Genesis 13 in the BOATCB2

Genesis 13 in the BOBCV

Genesis 13 in the BOCNT

Genesis 13 in the BOECS

Genesis 13 in the BOHCB

Genesis 13 in the BOHCV

Genesis 13 in the BOHLNT

Genesis 13 in the BOHNTLTAL

Genesis 13 in the BOICB

Genesis 13 in the BOILNTAP

Genesis 13 in the BOITCV

Genesis 13 in the BOKCV

Genesis 13 in the BOKCV2

Genesis 13 in the BOKHWOG

Genesis 13 in the BOKSSV

Genesis 13 in the BOLCB

Genesis 13 in the BOLCB2

Genesis 13 in the BOMCV

Genesis 13 in the BONAV

Genesis 13 in the BONCB

Genesis 13 in the BONLT

Genesis 13 in the BONUT2

Genesis 13 in the BOPLNT

Genesis 13 in the BOSCB

Genesis 13 in the BOSNC

Genesis 13 in the BOTLNT

Genesis 13 in the BOVCB

Genesis 13 in the BOYCB

Genesis 13 in the BPBB

Genesis 13 in the BPH

Genesis 13 in the BSB

Genesis 13 in the CCB

Genesis 13 in the CUV

Genesis 13 in the CUVS

Genesis 13 in the DBT

Genesis 13 in the DGDNT

Genesis 13 in the DHNT

Genesis 13 in the DNT

Genesis 13 in the ELBE

Genesis 13 in the EMTV

Genesis 13 in the ESV

Genesis 13 in the FBV

Genesis 13 in the FEB

Genesis 13 in the GGMNT

Genesis 13 in the GNT

Genesis 13 in the HARY

Genesis 13 in the HNT

Genesis 13 in the IRVA

Genesis 13 in the IRVB

Genesis 13 in the IRVG

Genesis 13 in the IRVH

Genesis 13 in the IRVK

Genesis 13 in the IRVM

Genesis 13 in the IRVM2

Genesis 13 in the IRVO

Genesis 13 in the IRVP

Genesis 13 in the IRVT

Genesis 13 in the IRVT2

Genesis 13 in the IRVU

Genesis 13 in the ISVN

Genesis 13 in the JSNT

Genesis 13 in the KAPI

Genesis 13 in the KBT1ETNIK

Genesis 13 in the KBV

Genesis 13 in the KJV

Genesis 13 in the KNFD

Genesis 13 in the LBA

Genesis 13 in the LBLA

Genesis 13 in the LNT

Genesis 13 in the LSV

Genesis 13 in the MAAL

Genesis 13 in the MBV

Genesis 13 in the MBV2

Genesis 13 in the MHNT

Genesis 13 in the MKNFD

Genesis 13 in the MNG

Genesis 13 in the MNT

Genesis 13 in the MNT2

Genesis 13 in the MRS1T

Genesis 13 in the NAA

Genesis 13 in the NASB

Genesis 13 in the NBLA

Genesis 13 in the NBS

Genesis 13 in the NBVTP

Genesis 13 in the NET2

Genesis 13 in the NIV11

Genesis 13 in the NNT

Genesis 13 in the NNT2

Genesis 13 in the NNT3

Genesis 13 in the PDDPT

Genesis 13 in the PFNT

Genesis 13 in the RMNT

Genesis 13 in the SBIAS

Genesis 13 in the SBIBS

Genesis 13 in the SBIBS2

Genesis 13 in the SBICS

Genesis 13 in the SBIDS

Genesis 13 in the SBIGS

Genesis 13 in the SBIHS

Genesis 13 in the SBIIS

Genesis 13 in the SBIIS2

Genesis 13 in the SBIIS3

Genesis 13 in the SBIKS

Genesis 13 in the SBIKS2

Genesis 13 in the SBIMS

Genesis 13 in the SBIOS

Genesis 13 in the SBIPS

Genesis 13 in the SBISS

Genesis 13 in the SBITS

Genesis 13 in the SBITS2

Genesis 13 in the SBITS3

Genesis 13 in the SBITS4

Genesis 13 in the SBIUS

Genesis 13 in the SBIVS

Genesis 13 in the SBT

Genesis 13 in the SBT1E

Genesis 13 in the SCHL

Genesis 13 in the SNT

Genesis 13 in the SUSU

Genesis 13 in the SUSU2

Genesis 13 in the SYNO

Genesis 13 in the TBIAOTANT

Genesis 13 in the TBT1E

Genesis 13 in the TBT1E2

Genesis 13 in the TFTIP

Genesis 13 in the TFTU

Genesis 13 in the TGNTATF3T

Genesis 13 in the THAI

Genesis 13 in the TNFD

Genesis 13 in the TNT

Genesis 13 in the TNTIK

Genesis 13 in the TNTIL

Genesis 13 in the TNTIN

Genesis 13 in the TNTIP

Genesis 13 in the TNTIZ

Genesis 13 in the TOMA

Genesis 13 in the TTENT

Genesis 13 in the UBG

Genesis 13 in the UGV

Genesis 13 in the UGV2

Genesis 13 in the UGV3

Genesis 13 in the VBL

Genesis 13 in the VDCC

Genesis 13 in the YALU

Genesis 13 in the YAPE

Genesis 13 in the YBVTP

Genesis 13 in the ZBP