Genesis 42 (BOGWICC)

1 Yakobo atamva kuti ku Igupto kuli tirigu, anati kwa ana ake, “Nʼchifukwa chiyani mukungoyangʼanana wina ndi mnzake? 2 Ine ndamva kuti ku Igupto kuli tirigu. Pitani kumeneko mukatigulireko kuti tisafe ndi njala.” 3 Choncho abale ake khumi a Yosefe anapita kukagula tirigu ku Igupto. 4 Koma Yakobo sanamulole Benjamini mngʼono wake wa Yosefe kuti apite nawo chifukwa anaopa kuti choyipa chingamuchitikire. 5 Choncho ana a Israeli aja anapita pamodzi ndi gulu la anzawo kukagula tirigu pakuti ku Kanaani kunalinso njala. 6 Pakuti Yosefe anali nduna yayikulu yolamulira dziko la Igupto, ndiye kuti analinso amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse. Choncho abale ake a Yosefe nawonso anabwera, ndipo anamugwadira pansi. 7 Yosefe atangowaona abale ake anawazindikira, koma ananamizira kukhala ngati mlendo nawayankhula mwaukali kuwafunsa kuti, “Mwachokera kuti?”Iwo anayankha, “Ku dziko la Kanaani, tikudzagula chakudya.” 8 Ngakhale Yosefe anawazindikira abale ake, koma iwo sanamuzindikire. 9 Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.” 10 Iwo anayankha, “Ayi mbuye wathu, antchito anufe tabwera kudzagula chakudya. 11 Tonse ndife ana a munthu mmodzi. Ndife antchito anu okhulupirika osati akazitape.” 12 Iye anawawuza kuti, “Ayi! Inu mwabwera kudzaona pamene palibe chitetezo mʼdziko muno.” 13 Koma iwo anayankha, “Tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri. Abambo athu ndi mmodzi, ndipo kwathu ndi ku Kanaani. Panopo wotsiriza ali ndi abambo athu ndipo wina anamwalira.” 14 Yosefe anawawuza kuti, “Ndi momwe ndaneneramo: Inu ndinu akazitape. 15 Ndiye ndikuyesani motere: Ine ndikulumbira pali Farao ndithu, inuyo simudzachoka malo ano mpaka wotsirizayo atabwera kuno. 16 Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!” 17 Ndipo onse anawayika mʼndende kwa masiku atatu. 18 Pa tsiku lachitatu Yosefe anawawuza kuti, “Popeza ine ndimaopa Mulungu, ndipo inuyo ngati mukufuna kukhala ndi moyo muchite izi: 19 Ngati muli anthu achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndende, pamene ena nonse mupite kwanu kuti muwatengere chakudya anthu akwanu kuli njalako. 20 Mukabwere naye kuno mngʼono wanu wotsirizayo kuti titsimikizire zimene munanena kuti musafe.” Ndipo anachita zomwezo. 21 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Ndithu ife tinalakwira mʼbale wathu uja popeza kuti ngakhale tinaona kuvutika kwake ndi kumva kulira kwake pamene ankatidandaulira kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamvere. Nʼchifukwa chake masautso awa atigwera.” 22 Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.” 23 Koma sanadziwe kuti Yosefe ankawamva popeza kuti ankagwiritsa ntchito wotanthauzira poyankhula naye. 24 Yosefe anapita pambali payekha kukalira. Kenaka anabweranso nadzayankhula nawo. Iye anatenga Simeoni namumanga iwo akuona. 25 Yosefe analamula kuti awadzazire matumba awo ndi tirigu, awayikiremo ndalama zawo momwemo ndiponso awapatse chakudya cha panjira. Izi anawachitiradi. 26 Abale a Yosefe aja anasenzetsa abulu awo tirigu amene anagula uja ndipo ananyamuka ulendo wawo. 27 Atafika pamalo pena poti agone, mmodzi mwa iwo anatsekula thumba lake kuti atapemo chakudya cha bulu wake. Atangomasula anaona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumba. 28 Iye anati kwa abale akewo, “Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumba mwangamu.”Mitima yawo inachita ngati yachokamo ndipo anali ndi mantha ambiri, nati, “Ndi chiyani chimene Mulungu watichitira?” 29 Atafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani anafotokoza zonse zimene zinawachitikira nati, 30 “Nduna yayikulu ya mʼdzikomo inatiyankhula mwa ukali kwambiri ndipo inkatiyesa kuti ndife akazitape. 31 Koma tinamuwuza kuti, ‘Ndife anthu woona mtima osati akazitape. 32 Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri, abambo mmodzi. Mmodzi anamwalira, ndipo wamngʼono ali ndi abambo athu ku Kanaani.’ ” 33 Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako. 34 Koma mundibweretsere wotsirizayo kuti ndidziwedi kuti sindinu akazitape koma anthu achilungamo. Kenaka ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu ndipo mukhoza kuchita malonda mʼdzikoli.” 35 Pamene amakhuthula matumba awo a tirigu aliyense anapeza kuti kathumba kake ka ndalama kali momwemo. Ataona zimenezi, iwo pamodzi ndi abambo awo anachita mantha kwambiri. 36 Abambo awo Yakobo anawawuza kuti, “Mwandilanda ana anga ine. Yosefe anamwalira ndipo Simeoni palibenso, ndiye tsopano mukufuna mutengenso Benjamini. Zonsezi zandigwera ine!” 37 Koma Rubeni anati kwa abambo ake, “Ngati sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri. Muperekeni mʼmanja mwangamu ndipo ndidzamusamala ndi kubwera naye kwa inu.” 38 Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.”

In Other Versions

Genesis 42 in the ANGEFD

Genesis 42 in the ANTPNG2D

Genesis 42 in the AS21

Genesis 42 in the BAGH

Genesis 42 in the BBPNG

Genesis 42 in the BBT1E

Genesis 42 in the BDS

Genesis 42 in the BEV

Genesis 42 in the BHAD

Genesis 42 in the BIB

Genesis 42 in the BLPT

Genesis 42 in the BNT

Genesis 42 in the BNTABOOT

Genesis 42 in the BNTLV

Genesis 42 in the BOATCB

Genesis 42 in the BOATCB2

Genesis 42 in the BOBCV

Genesis 42 in the BOCNT

Genesis 42 in the BOECS

Genesis 42 in the BOHCB

Genesis 42 in the BOHCV

Genesis 42 in the BOHLNT

Genesis 42 in the BOHNTLTAL

Genesis 42 in the BOICB

Genesis 42 in the BOILNTAP

Genesis 42 in the BOITCV

Genesis 42 in the BOKCV

Genesis 42 in the BOKCV2

Genesis 42 in the BOKHWOG

Genesis 42 in the BOKSSV

Genesis 42 in the BOLCB

Genesis 42 in the BOLCB2

Genesis 42 in the BOMCV

Genesis 42 in the BONAV

Genesis 42 in the BONCB

Genesis 42 in the BONLT

Genesis 42 in the BONUT2

Genesis 42 in the BOPLNT

Genesis 42 in the BOSCB

Genesis 42 in the BOSNC

Genesis 42 in the BOTLNT

Genesis 42 in the BOVCB

Genesis 42 in the BOYCB

Genesis 42 in the BPBB

Genesis 42 in the BPH

Genesis 42 in the BSB

Genesis 42 in the CCB

Genesis 42 in the CUV

Genesis 42 in the CUVS

Genesis 42 in the DBT

Genesis 42 in the DGDNT

Genesis 42 in the DHNT

Genesis 42 in the DNT

Genesis 42 in the ELBE

Genesis 42 in the EMTV

Genesis 42 in the ESV

Genesis 42 in the FBV

Genesis 42 in the FEB

Genesis 42 in the GGMNT

Genesis 42 in the GNT

Genesis 42 in the HARY

Genesis 42 in the HNT

Genesis 42 in the IRVA

Genesis 42 in the IRVB

Genesis 42 in the IRVG

Genesis 42 in the IRVH

Genesis 42 in the IRVK

Genesis 42 in the IRVM

Genesis 42 in the IRVM2

Genesis 42 in the IRVO

Genesis 42 in the IRVP

Genesis 42 in the IRVT

Genesis 42 in the IRVT2

Genesis 42 in the IRVU

Genesis 42 in the ISVN

Genesis 42 in the JSNT

Genesis 42 in the KAPI

Genesis 42 in the KBT1ETNIK

Genesis 42 in the KBV

Genesis 42 in the KJV

Genesis 42 in the KNFD

Genesis 42 in the LBA

Genesis 42 in the LBLA

Genesis 42 in the LNT

Genesis 42 in the LSV

Genesis 42 in the MAAL

Genesis 42 in the MBV

Genesis 42 in the MBV2

Genesis 42 in the MHNT

Genesis 42 in the MKNFD

Genesis 42 in the MNG

Genesis 42 in the MNT

Genesis 42 in the MNT2

Genesis 42 in the MRS1T

Genesis 42 in the NAA

Genesis 42 in the NASB

Genesis 42 in the NBLA

Genesis 42 in the NBS

Genesis 42 in the NBVTP

Genesis 42 in the NET2

Genesis 42 in the NIV11

Genesis 42 in the NNT

Genesis 42 in the NNT2

Genesis 42 in the NNT3

Genesis 42 in the PDDPT

Genesis 42 in the PFNT

Genesis 42 in the RMNT

Genesis 42 in the SBIAS

Genesis 42 in the SBIBS

Genesis 42 in the SBIBS2

Genesis 42 in the SBICS

Genesis 42 in the SBIDS

Genesis 42 in the SBIGS

Genesis 42 in the SBIHS

Genesis 42 in the SBIIS

Genesis 42 in the SBIIS2

Genesis 42 in the SBIIS3

Genesis 42 in the SBIKS

Genesis 42 in the SBIKS2

Genesis 42 in the SBIMS

Genesis 42 in the SBIOS

Genesis 42 in the SBIPS

Genesis 42 in the SBISS

Genesis 42 in the SBITS

Genesis 42 in the SBITS2

Genesis 42 in the SBITS3

Genesis 42 in the SBITS4

Genesis 42 in the SBIUS

Genesis 42 in the SBIVS

Genesis 42 in the SBT

Genesis 42 in the SBT1E

Genesis 42 in the SCHL

Genesis 42 in the SNT

Genesis 42 in the SUSU

Genesis 42 in the SUSU2

Genesis 42 in the SYNO

Genesis 42 in the TBIAOTANT

Genesis 42 in the TBT1E

Genesis 42 in the TBT1E2

Genesis 42 in the TFTIP

Genesis 42 in the TFTU

Genesis 42 in the TGNTATF3T

Genesis 42 in the THAI

Genesis 42 in the TNFD

Genesis 42 in the TNT

Genesis 42 in the TNTIK

Genesis 42 in the TNTIL

Genesis 42 in the TNTIN

Genesis 42 in the TNTIP

Genesis 42 in the TNTIZ

Genesis 42 in the TOMA

Genesis 42 in the TTENT

Genesis 42 in the UBG

Genesis 42 in the UGV

Genesis 42 in the UGV2

Genesis 42 in the UGV3

Genesis 42 in the VBL

Genesis 42 in the VDCC

Genesis 42 in the YALU

Genesis 42 in the YAPE

Genesis 42 in the YBVTP

Genesis 42 in the ZBP