Isaiah 12 (BOGWICC)
1 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;chifukwa ngakhale munandipsera mtima,mkwiyo wanu wachoka,ndipo mwanditonthoza. 2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Iye wakhala chipulumutso changa.” 3 Mudzakondwera popeza Yehovaali ngati chitsime cha chipulumutso chanu. 4 Tsiku limenelo mudzati:“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. 5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi. 6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”