Judges 16 (BOGWICC)

1 Tsiku lina Samsoni anapita ku Gaza. Kumeneko anaonako mkazi wachiwerewere, ndipo analowa mu nyumba yake. 2 Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.” 3 Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni. 4 Pambuyo pake, Samsoni anayamba kukonda mtsikana wina wa ku chigwa cha Soreki dzina lake Delila. 5 Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.” 6 Choncho Delila anati kwa Samsoni, “Inu tandiwuzani pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi ndi mmene anthu akhoza kukumangirani kuti akugonjetseni.” 7 Samsoni anamuyankha kuti, “Ngati wina atandimanga ndi zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndidzafowoka ndi kusanduka ngati munthu wina aliyense.” 8 Tsono atsogoleri a Afilisti aja anapita kwa mkazi uja namupatsa zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndipo mkaziyo anamanga nazo Samsoni. 9 Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike. 10 Kenaka Delila anati kwa Samsoni, “Inu mwandipusitsa ndi kundiwuza zabodza. Chonde tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.” 11 Iye anati, “Ngati aliyense atandimanga ine ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritseko ntchito, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala monga munthu wina aliyense.” 12 Choncho Delila anatenga zingwe zatsopano namumanga nazo. Kenaka anati “Amuna anga, Afilisti aja afikanso!” Nthawi iyi nʼkuti anthu omubisalira aja ali mʼchipinda chamʼkati. Koma iye anadulanso zingwe mʼmanja ake ngati akudula ulusi wa thonje. 13 Ndipo Delila anati kwa Samsoni, “Mpaka tsopano mwakhala mukundipusitsa ndi kumandiwuza zabodza. Chonde, tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.”Iye anayankha kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziwiri za kumutu kwanga utazilukira mu cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala wofanana ndi munthu wina aliyense.” 14 Choncho iye akugona, Delila analukira njombi za ku mutu kwa Samsoni mu cholukira nsalu nachimanga molimba ndi chikhomo.Pambuyo pake anati kwa Samsoni, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Tsono iye anadzuka ku tulo, nazula chikhomo chija ndipo njombi zinachoka mu cholukira chija. 15 Tsono mkaziyo ananenanso kwa iye kuti, “Munganene bwanji kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Aka ndi kachitatu mukundipusitsa ndipo simunandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.” 16 Tsono popeza anamupanikiza ndi mawu ake tsiku ndi tsiku ndi kumukakamiza, mtima wa Samsoni unatopa pafupi kufa. 17 Choncho anamuwuza mkaziyo zonse za mu mtima mwake nati “Lumo silinapitepo pa mutu wanga chifukwa ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu chibadwire. Ngati nditametedwa mphamvu zanga zidzandichokera, ndidzasanduka wofowoka ndipo ndidzafanana ndi munthu wina aliyense.” 18 Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo. 19 Mkazi uja anagoneka Samsoni pa miyendo yake. Kenaka anayitana munthu wina ndipo anadzameta Samsoni njombi zisanu ndi ziwiri zija kumutu kwake. Pamenepo anayamba kufowoka, ndipo mphamvu zake zinamuchokera. 20 Pambuyo pake mkaziyo anamuyitana kuti, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!”Iye anadzuka kutuloko, naganiza kuti, “Ndituluka monga ndimachitira nthawi zonse ndi kudzimasula.” Koma sanadziwe kuti Yehova wamuchokera. 21 Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende. 22 Pambuyo pake tsitsi la pa mutu wake, monga linametedwa, linayambanso kumera. 23 Tsono atsogoleri a Afilisti anasonkhana kuti adzapereke nsembe yayikulu kwa Dagoni mulungu wawo ndi kukondwerera popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu mʼmanja mwathu.” 24 Anthuwo atamuona Samsoni, anayamba kutamanda mulungu wawo popeza ankanena kuti,“Mulungu wathu wapereka mdani wathumʼmanja mwathu,ndiye amene anawononga dziko lathu,napha anthu athu ambirimbiri.” 25 Ali mʼkati mosangalala, anthu aja amafuwula kuti, “Mutulutseni Samsoniyo kuti adzatisangalatse.” Choncho anamutulutsadi Samsoni mʼndende, ndipo anawasangalatsadi.Ndipo anamuyimiritsa pakati pa mizati. 26 Pambuyo pake Samsoni anawuza mnyamata amene anamugwira dzanja kuti, “Ndilole kuti ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi kuti ndiyitsamire.” 27 Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera. 28 Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri.” 29 Choncho Samsoni anagwira mizati iwiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Anayitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja ku mzati wina ndi dzanja lamanzere ku mzati winanso, 30 ndipo Samsoni anati, “Ndife nawo pamodzi!” Nthawi yomweyo anakankha ndi mphamvu zake zonse ndipo mizati inagwera atsogoleri a Afilisti ndi anthu onse anali mʼmenemo. Tsono chiwerengero cha anthu amene Samsoni anapha pa nthawi ya imfa yake chinaposa cha iwo amene anawapha akanali ndi moyo. 31 Kenaka abale ake ndi onse a pa banja la abambo ake anapita kukamutenga. Ndipo anakamuyika pakati pa Zora ndi Esitaoli mʼmanda a abambo ake, Manowa. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka makumi awiri.

In Other Versions

Judges 16 in the ANGEFD

Judges 16 in the ANTPNG2D

Judges 16 in the AS21

Judges 16 in the BAGH

Judges 16 in the BBPNG

Judges 16 in the BBT1E

Judges 16 in the BDS

Judges 16 in the BEV

Judges 16 in the BHAD

Judges 16 in the BIB

Judges 16 in the BLPT

Judges 16 in the BNT

Judges 16 in the BNTABOOT

Judges 16 in the BNTLV

Judges 16 in the BOATCB

Judges 16 in the BOATCB2

Judges 16 in the BOBCV

Judges 16 in the BOCNT

Judges 16 in the BOECS

Judges 16 in the BOHCB

Judges 16 in the BOHCV

Judges 16 in the BOHLNT

Judges 16 in the BOHNTLTAL

Judges 16 in the BOICB

Judges 16 in the BOILNTAP

Judges 16 in the BOITCV

Judges 16 in the BOKCV

Judges 16 in the BOKCV2

Judges 16 in the BOKHWOG

Judges 16 in the BOKSSV

Judges 16 in the BOLCB

Judges 16 in the BOLCB2

Judges 16 in the BOMCV

Judges 16 in the BONAV

Judges 16 in the BONCB

Judges 16 in the BONLT

Judges 16 in the BONUT2

Judges 16 in the BOPLNT

Judges 16 in the BOSCB

Judges 16 in the BOSNC

Judges 16 in the BOTLNT

Judges 16 in the BOVCB

Judges 16 in the BOYCB

Judges 16 in the BPBB

Judges 16 in the BPH

Judges 16 in the BSB

Judges 16 in the CCB

Judges 16 in the CUV

Judges 16 in the CUVS

Judges 16 in the DBT

Judges 16 in the DGDNT

Judges 16 in the DHNT

Judges 16 in the DNT

Judges 16 in the ELBE

Judges 16 in the EMTV

Judges 16 in the ESV

Judges 16 in the FBV

Judges 16 in the FEB

Judges 16 in the GGMNT

Judges 16 in the GNT

Judges 16 in the HARY

Judges 16 in the HNT

Judges 16 in the IRVA

Judges 16 in the IRVB

Judges 16 in the IRVG

Judges 16 in the IRVH

Judges 16 in the IRVK

Judges 16 in the IRVM

Judges 16 in the IRVM2

Judges 16 in the IRVO

Judges 16 in the IRVP

Judges 16 in the IRVT

Judges 16 in the IRVT2

Judges 16 in the IRVU

Judges 16 in the ISVN

Judges 16 in the JSNT

Judges 16 in the KAPI

Judges 16 in the KBT1ETNIK

Judges 16 in the KBV

Judges 16 in the KJV

Judges 16 in the KNFD

Judges 16 in the LBA

Judges 16 in the LBLA

Judges 16 in the LNT

Judges 16 in the LSV

Judges 16 in the MAAL

Judges 16 in the MBV

Judges 16 in the MBV2

Judges 16 in the MHNT

Judges 16 in the MKNFD

Judges 16 in the MNG

Judges 16 in the MNT

Judges 16 in the MNT2

Judges 16 in the MRS1T

Judges 16 in the NAA

Judges 16 in the NASB

Judges 16 in the NBLA

Judges 16 in the NBS

Judges 16 in the NBVTP

Judges 16 in the NET2

Judges 16 in the NIV11

Judges 16 in the NNT

Judges 16 in the NNT2

Judges 16 in the NNT3

Judges 16 in the PDDPT

Judges 16 in the PFNT

Judges 16 in the RMNT

Judges 16 in the SBIAS

Judges 16 in the SBIBS

Judges 16 in the SBIBS2

Judges 16 in the SBICS

Judges 16 in the SBIDS

Judges 16 in the SBIGS

Judges 16 in the SBIHS

Judges 16 in the SBIIS

Judges 16 in the SBIIS2

Judges 16 in the SBIIS3

Judges 16 in the SBIKS

Judges 16 in the SBIKS2

Judges 16 in the SBIMS

Judges 16 in the SBIOS

Judges 16 in the SBIPS

Judges 16 in the SBISS

Judges 16 in the SBITS

Judges 16 in the SBITS2

Judges 16 in the SBITS3

Judges 16 in the SBITS4

Judges 16 in the SBIUS

Judges 16 in the SBIVS

Judges 16 in the SBT

Judges 16 in the SBT1E

Judges 16 in the SCHL

Judges 16 in the SNT

Judges 16 in the SUSU

Judges 16 in the SUSU2

Judges 16 in the SYNO

Judges 16 in the TBIAOTANT

Judges 16 in the TBT1E

Judges 16 in the TBT1E2

Judges 16 in the TFTIP

Judges 16 in the TFTU

Judges 16 in the TGNTATF3T

Judges 16 in the THAI

Judges 16 in the TNFD

Judges 16 in the TNT

Judges 16 in the TNTIK

Judges 16 in the TNTIL

Judges 16 in the TNTIN

Judges 16 in the TNTIP

Judges 16 in the TNTIZ

Judges 16 in the TOMA

Judges 16 in the TTENT

Judges 16 in the UBG

Judges 16 in the UGV

Judges 16 in the UGV2

Judges 16 in the UGV3

Judges 16 in the VBL

Judges 16 in the VDCC

Judges 16 in the YALU

Judges 16 in the YAPE

Judges 16 in the YBVTP

Judges 16 in the ZBP