Jeremiah 7 (BOGWICC)

1 Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa, 2 “Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu:“ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova. 3 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano. 4 Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ 5 Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, 6 ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, 7 Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. 8 Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu. 9 “Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, 10 ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? 11 Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.” 12 “ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli. 13 Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha, 14 choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo. 15 Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ” 16 “Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera. 17 Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 18 Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. 19 Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.” 20 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika. 21 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo! 22 Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo, 23 koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 24 Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo. 25 Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri. 26 Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo. 27 “Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha. 28 Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’ 29 “Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.” 30 “Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa. 31 Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe. 32 Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika. 33 Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. 34 Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”

In Other Versions

Jeremiah 7 in the ANGEFD

Jeremiah 7 in the ANTPNG2D

Jeremiah 7 in the AS21

Jeremiah 7 in the BAGH

Jeremiah 7 in the BBPNG

Jeremiah 7 in the BBT1E

Jeremiah 7 in the BDS

Jeremiah 7 in the BEV

Jeremiah 7 in the BHAD

Jeremiah 7 in the BIB

Jeremiah 7 in the BLPT

Jeremiah 7 in the BNT

Jeremiah 7 in the BNTABOOT

Jeremiah 7 in the BNTLV

Jeremiah 7 in the BOATCB

Jeremiah 7 in the BOATCB2

Jeremiah 7 in the BOBCV

Jeremiah 7 in the BOCNT

Jeremiah 7 in the BOECS

Jeremiah 7 in the BOHCB

Jeremiah 7 in the BOHCV

Jeremiah 7 in the BOHLNT

Jeremiah 7 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 7 in the BOICB

Jeremiah 7 in the BOILNTAP

Jeremiah 7 in the BOITCV

Jeremiah 7 in the BOKCV

Jeremiah 7 in the BOKCV2

Jeremiah 7 in the BOKHWOG

Jeremiah 7 in the BOKSSV

Jeremiah 7 in the BOLCB

Jeremiah 7 in the BOLCB2

Jeremiah 7 in the BOMCV

Jeremiah 7 in the BONAV

Jeremiah 7 in the BONCB

Jeremiah 7 in the BONLT

Jeremiah 7 in the BONUT2

Jeremiah 7 in the BOPLNT

Jeremiah 7 in the BOSCB

Jeremiah 7 in the BOSNC

Jeremiah 7 in the BOTLNT

Jeremiah 7 in the BOVCB

Jeremiah 7 in the BOYCB

Jeremiah 7 in the BPBB

Jeremiah 7 in the BPH

Jeremiah 7 in the BSB

Jeremiah 7 in the CCB

Jeremiah 7 in the CUV

Jeremiah 7 in the CUVS

Jeremiah 7 in the DBT

Jeremiah 7 in the DGDNT

Jeremiah 7 in the DHNT

Jeremiah 7 in the DNT

Jeremiah 7 in the ELBE

Jeremiah 7 in the EMTV

Jeremiah 7 in the ESV

Jeremiah 7 in the FBV

Jeremiah 7 in the FEB

Jeremiah 7 in the GGMNT

Jeremiah 7 in the GNT

Jeremiah 7 in the HARY

Jeremiah 7 in the HNT

Jeremiah 7 in the IRVA

Jeremiah 7 in the IRVB

Jeremiah 7 in the IRVG

Jeremiah 7 in the IRVH

Jeremiah 7 in the IRVK

Jeremiah 7 in the IRVM

Jeremiah 7 in the IRVM2

Jeremiah 7 in the IRVO

Jeremiah 7 in the IRVP

Jeremiah 7 in the IRVT

Jeremiah 7 in the IRVT2

Jeremiah 7 in the IRVU

Jeremiah 7 in the ISVN

Jeremiah 7 in the JSNT

Jeremiah 7 in the KAPI

Jeremiah 7 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 7 in the KBV

Jeremiah 7 in the KJV

Jeremiah 7 in the KNFD

Jeremiah 7 in the LBA

Jeremiah 7 in the LBLA

Jeremiah 7 in the LNT

Jeremiah 7 in the LSV

Jeremiah 7 in the MAAL

Jeremiah 7 in the MBV

Jeremiah 7 in the MBV2

Jeremiah 7 in the MHNT

Jeremiah 7 in the MKNFD

Jeremiah 7 in the MNG

Jeremiah 7 in the MNT

Jeremiah 7 in the MNT2

Jeremiah 7 in the MRS1T

Jeremiah 7 in the NAA

Jeremiah 7 in the NASB

Jeremiah 7 in the NBLA

Jeremiah 7 in the NBS

Jeremiah 7 in the NBVTP

Jeremiah 7 in the NET2

Jeremiah 7 in the NIV11

Jeremiah 7 in the NNT

Jeremiah 7 in the NNT2

Jeremiah 7 in the NNT3

Jeremiah 7 in the PDDPT

Jeremiah 7 in the PFNT

Jeremiah 7 in the RMNT

Jeremiah 7 in the SBIAS

Jeremiah 7 in the SBIBS

Jeremiah 7 in the SBIBS2

Jeremiah 7 in the SBICS

Jeremiah 7 in the SBIDS

Jeremiah 7 in the SBIGS

Jeremiah 7 in the SBIHS

Jeremiah 7 in the SBIIS

Jeremiah 7 in the SBIIS2

Jeremiah 7 in the SBIIS3

Jeremiah 7 in the SBIKS

Jeremiah 7 in the SBIKS2

Jeremiah 7 in the SBIMS

Jeremiah 7 in the SBIOS

Jeremiah 7 in the SBIPS

Jeremiah 7 in the SBISS

Jeremiah 7 in the SBITS

Jeremiah 7 in the SBITS2

Jeremiah 7 in the SBITS3

Jeremiah 7 in the SBITS4

Jeremiah 7 in the SBIUS

Jeremiah 7 in the SBIVS

Jeremiah 7 in the SBT

Jeremiah 7 in the SBT1E

Jeremiah 7 in the SCHL

Jeremiah 7 in the SNT

Jeremiah 7 in the SUSU

Jeremiah 7 in the SUSU2

Jeremiah 7 in the SYNO

Jeremiah 7 in the TBIAOTANT

Jeremiah 7 in the TBT1E

Jeremiah 7 in the TBT1E2

Jeremiah 7 in the TFTIP

Jeremiah 7 in the TFTU

Jeremiah 7 in the TGNTATF3T

Jeremiah 7 in the THAI

Jeremiah 7 in the TNFD

Jeremiah 7 in the TNT

Jeremiah 7 in the TNTIK

Jeremiah 7 in the TNTIL

Jeremiah 7 in the TNTIN

Jeremiah 7 in the TNTIP

Jeremiah 7 in the TNTIZ

Jeremiah 7 in the TOMA

Jeremiah 7 in the TTENT

Jeremiah 7 in the UBG

Jeremiah 7 in the UGV

Jeremiah 7 in the UGV2

Jeremiah 7 in the UGV3

Jeremiah 7 in the VBL

Jeremiah 7 in the VDCC

Jeremiah 7 in the YALU

Jeremiah 7 in the YAPE

Jeremiah 7 in the YBVTP

Jeremiah 7 in the ZBP