Leviticus 16 (BOGWICC)

1 Atafa ana awiri a Aaroni amene anaphedwa atapita pamaso pa Yehova mosayenera, Yehova anayankhula ndi Mose. 2 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano. 3 “Aaroni azilowa Malo Wopatulika Kwambiri motere: azitenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. 4 Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi. 5 Kuchokera pa gulu la Aisraeli, Aaroni azitenga mbuzi zazimuna ziwiri kuti zikhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. 6 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale yopepesera machimo a iye mwini kuti achite mwambo wopepesera machimo ake pamodzi ndi a banja lake. 7 Kenaka atenge mbuzi ziwiri zija ndipo aziyimike pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 8 Aaroni ndiye achite maere pa mbuzi ziwirizo kuti imodzi ikhale ya Yehova, ndipo inayo ikhale ya Azazele. 9 Aaroni abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Yehova, ndipo apereke kuti ikhale nsembe yopereka chifukwa cha tchimo. 10 Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele. 11 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja. 12 Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani. 13 Athire lubani pa moto pamaso pa Yehova kuti utsi wa lubaniyo uphimbe chivundikiro chimene chili pamwamba pa Bokosi la Chipangano, kuti Aaroniyo asafe. 14 Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho. 15 “Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. 16 Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika chifukwa cha kudetsedwa ndi kuwukira kwa Aisraeli pa machimo ena aliwonse amene achita. Achite chimodzimodzi ndi tenti ya msonkhano imenenso ili yodetsedwa chifukwa cha machimo awo. 17 Mu tenti ya msonkhano musakhale munthu ndi mmodzi yemwe nthawi imene Aaroni akupita kukachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika mpaka atatulukako. Musakhale munthu mu tenti ya msonkhano mpaka atachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake, banja lake ndi gulu lonse la Aisraeli. 18 “Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe. 19 Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli. 20 “Aaroni akatsiriza mwambo wopepesera Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa, azibwera ndi mbuzi yamoyo kudzayipereka nsembe. 21 Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu. 22 Mbuziyo isenze machimo awo onse ndi kupita nawo kutali ndipo munthuyo aleke mbuziyo kuti ipite ku chipululuko. 23 “Pambuyo pake Aaroni alowe mu tenti ya msonkhano ndi kuvula zovala zosalala zija zimene anavala polowa ku Malo Wopatulika ndi kuzisiya komweko. 24 Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu. 25 Mafuta a nyama yopepesera machimo awatenthe pa guwa lansembe. 26 “Tsono munthu amene anaperekeza mbuzi yosenza machimo ija achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe ku msasa. 27 Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe. 28 Munthu amene azitenthe achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe mu msasa. 29 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu, 30 chifukwa tsiku limeneli kudzachitika mwambo wopepesera machimo anu, kukuyeretsani kuti mukhale oyeretsedwa ku machimo anu pamaso pa Yehova. 31 Limeneli ndi tsiku lanu la Sabata lopumula, ndipo muzigonja pamaso pa Yehova. Limeneli ndi lamulo lanu la muyaya. 32 Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika. 33 Adzachite mwambo wopepesera machimo Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Adzachitenso mwambo wopepesera anzake ndi gulu lonse la anthu. 34 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.”Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.

In Other Versions

Leviticus 16 in the ANGEFD

Leviticus 16 in the ANTPNG2D

Leviticus 16 in the AS21

Leviticus 16 in the BAGH

Leviticus 16 in the BBPNG

Leviticus 16 in the BBT1E

Leviticus 16 in the BDS

Leviticus 16 in the BEV

Leviticus 16 in the BHAD

Leviticus 16 in the BIB

Leviticus 16 in the BLPT

Leviticus 16 in the BNT

Leviticus 16 in the BNTABOOT

Leviticus 16 in the BNTLV

Leviticus 16 in the BOATCB

Leviticus 16 in the BOATCB2

Leviticus 16 in the BOBCV

Leviticus 16 in the BOCNT

Leviticus 16 in the BOECS

Leviticus 16 in the BOHCB

Leviticus 16 in the BOHCV

Leviticus 16 in the BOHLNT

Leviticus 16 in the BOHNTLTAL

Leviticus 16 in the BOICB

Leviticus 16 in the BOILNTAP

Leviticus 16 in the BOITCV

Leviticus 16 in the BOKCV

Leviticus 16 in the BOKCV2

Leviticus 16 in the BOKHWOG

Leviticus 16 in the BOKSSV

Leviticus 16 in the BOLCB

Leviticus 16 in the BOLCB2

Leviticus 16 in the BOMCV

Leviticus 16 in the BONAV

Leviticus 16 in the BONCB

Leviticus 16 in the BONLT

Leviticus 16 in the BONUT2

Leviticus 16 in the BOPLNT

Leviticus 16 in the BOSCB

Leviticus 16 in the BOSNC

Leviticus 16 in the BOTLNT

Leviticus 16 in the BOVCB

Leviticus 16 in the BOYCB

Leviticus 16 in the BPBB

Leviticus 16 in the BPH

Leviticus 16 in the BSB

Leviticus 16 in the CCB

Leviticus 16 in the CUV

Leviticus 16 in the CUVS

Leviticus 16 in the DBT

Leviticus 16 in the DGDNT

Leviticus 16 in the DHNT

Leviticus 16 in the DNT

Leviticus 16 in the ELBE

Leviticus 16 in the EMTV

Leviticus 16 in the ESV

Leviticus 16 in the FBV

Leviticus 16 in the FEB

Leviticus 16 in the GGMNT

Leviticus 16 in the GNT

Leviticus 16 in the HARY

Leviticus 16 in the HNT

Leviticus 16 in the IRVA

Leviticus 16 in the IRVB

Leviticus 16 in the IRVG

Leviticus 16 in the IRVH

Leviticus 16 in the IRVK

Leviticus 16 in the IRVM

Leviticus 16 in the IRVM2

Leviticus 16 in the IRVO

Leviticus 16 in the IRVP

Leviticus 16 in the IRVT

Leviticus 16 in the IRVT2

Leviticus 16 in the IRVU

Leviticus 16 in the ISVN

Leviticus 16 in the JSNT

Leviticus 16 in the KAPI

Leviticus 16 in the KBT1ETNIK

Leviticus 16 in the KBV

Leviticus 16 in the KJV

Leviticus 16 in the KNFD

Leviticus 16 in the LBA

Leviticus 16 in the LBLA

Leviticus 16 in the LNT

Leviticus 16 in the LSV

Leviticus 16 in the MAAL

Leviticus 16 in the MBV

Leviticus 16 in the MBV2

Leviticus 16 in the MHNT

Leviticus 16 in the MKNFD

Leviticus 16 in the MNG

Leviticus 16 in the MNT

Leviticus 16 in the MNT2

Leviticus 16 in the MRS1T

Leviticus 16 in the NAA

Leviticus 16 in the NASB

Leviticus 16 in the NBLA

Leviticus 16 in the NBS

Leviticus 16 in the NBVTP

Leviticus 16 in the NET2

Leviticus 16 in the NIV11

Leviticus 16 in the NNT

Leviticus 16 in the NNT2

Leviticus 16 in the NNT3

Leviticus 16 in the PDDPT

Leviticus 16 in the PFNT

Leviticus 16 in the RMNT

Leviticus 16 in the SBIAS

Leviticus 16 in the SBIBS

Leviticus 16 in the SBIBS2

Leviticus 16 in the SBICS

Leviticus 16 in the SBIDS

Leviticus 16 in the SBIGS

Leviticus 16 in the SBIHS

Leviticus 16 in the SBIIS

Leviticus 16 in the SBIIS2

Leviticus 16 in the SBIIS3

Leviticus 16 in the SBIKS

Leviticus 16 in the SBIKS2

Leviticus 16 in the SBIMS

Leviticus 16 in the SBIOS

Leviticus 16 in the SBIPS

Leviticus 16 in the SBISS

Leviticus 16 in the SBITS

Leviticus 16 in the SBITS2

Leviticus 16 in the SBITS3

Leviticus 16 in the SBITS4

Leviticus 16 in the SBIUS

Leviticus 16 in the SBIVS

Leviticus 16 in the SBT

Leviticus 16 in the SBT1E

Leviticus 16 in the SCHL

Leviticus 16 in the SNT

Leviticus 16 in the SUSU

Leviticus 16 in the SUSU2

Leviticus 16 in the SYNO

Leviticus 16 in the TBIAOTANT

Leviticus 16 in the TBT1E

Leviticus 16 in the TBT1E2

Leviticus 16 in the TFTIP

Leviticus 16 in the TFTU

Leviticus 16 in the TGNTATF3T

Leviticus 16 in the THAI

Leviticus 16 in the TNFD

Leviticus 16 in the TNT

Leviticus 16 in the TNTIK

Leviticus 16 in the TNTIL

Leviticus 16 in the TNTIN

Leviticus 16 in the TNTIP

Leviticus 16 in the TNTIZ

Leviticus 16 in the TOMA

Leviticus 16 in the TTENT

Leviticus 16 in the UBG

Leviticus 16 in the UGV

Leviticus 16 in the UGV2

Leviticus 16 in the UGV3

Leviticus 16 in the VBL

Leviticus 16 in the VDCC

Leviticus 16 in the YALU

Leviticus 16 in the YAPE

Leviticus 16 in the YBVTP

Leviticus 16 in the ZBP