Leviticus 23 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano. 3 “ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova. 4 “ ‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake: 5 Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. 6 Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 7 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse. 8 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ” 9 Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu. 11 Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata. 12 Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 13 Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka. 14 Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 15 “ ‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu. 16 Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova. 17 Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha. 18 Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova. 19 Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano. 20 Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe. 21 Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 22 “ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” 23 Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga. 25 Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’ ” 26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. 28 Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 30 Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake. 31 Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 32 Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.” 33 Yehova anawuza Mose kuti, 34 “Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova. 35 Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa. 36 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa. 37 (“ ‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku. 38 Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.) 39 “ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso. 40 Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri. 41 Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri. 42 Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa 43 kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” 44 Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.

In Other Versions

Leviticus 23 in the ANGEFD

Leviticus 23 in the ANTPNG2D

Leviticus 23 in the AS21

Leviticus 23 in the BAGH

Leviticus 23 in the BBPNG

Leviticus 23 in the BBT1E

Leviticus 23 in the BDS

Leviticus 23 in the BEV

Leviticus 23 in the BHAD

Leviticus 23 in the BIB

Leviticus 23 in the BLPT

Leviticus 23 in the BNT

Leviticus 23 in the BNTABOOT

Leviticus 23 in the BNTLV

Leviticus 23 in the BOATCB

Leviticus 23 in the BOATCB2

Leviticus 23 in the BOBCV

Leviticus 23 in the BOCNT

Leviticus 23 in the BOECS

Leviticus 23 in the BOHCB

Leviticus 23 in the BOHCV

Leviticus 23 in the BOHLNT

Leviticus 23 in the BOHNTLTAL

Leviticus 23 in the BOICB

Leviticus 23 in the BOILNTAP

Leviticus 23 in the BOITCV

Leviticus 23 in the BOKCV

Leviticus 23 in the BOKCV2

Leviticus 23 in the BOKHWOG

Leviticus 23 in the BOKSSV

Leviticus 23 in the BOLCB

Leviticus 23 in the BOLCB2

Leviticus 23 in the BOMCV

Leviticus 23 in the BONAV

Leviticus 23 in the BONCB

Leviticus 23 in the BONLT

Leviticus 23 in the BONUT2

Leviticus 23 in the BOPLNT

Leviticus 23 in the BOSCB

Leviticus 23 in the BOSNC

Leviticus 23 in the BOTLNT

Leviticus 23 in the BOVCB

Leviticus 23 in the BOYCB

Leviticus 23 in the BPBB

Leviticus 23 in the BPH

Leviticus 23 in the BSB

Leviticus 23 in the CCB

Leviticus 23 in the CUV

Leviticus 23 in the CUVS

Leviticus 23 in the DBT

Leviticus 23 in the DGDNT

Leviticus 23 in the DHNT

Leviticus 23 in the DNT

Leviticus 23 in the ELBE

Leviticus 23 in the EMTV

Leviticus 23 in the ESV

Leviticus 23 in the FBV

Leviticus 23 in the FEB

Leviticus 23 in the GGMNT

Leviticus 23 in the GNT

Leviticus 23 in the HARY

Leviticus 23 in the HNT

Leviticus 23 in the IRVA

Leviticus 23 in the IRVB

Leviticus 23 in the IRVG

Leviticus 23 in the IRVH

Leviticus 23 in the IRVK

Leviticus 23 in the IRVM

Leviticus 23 in the IRVM2

Leviticus 23 in the IRVO

Leviticus 23 in the IRVP

Leviticus 23 in the IRVT

Leviticus 23 in the IRVT2

Leviticus 23 in the IRVU

Leviticus 23 in the ISVN

Leviticus 23 in the JSNT

Leviticus 23 in the KAPI

Leviticus 23 in the KBT1ETNIK

Leviticus 23 in the KBV

Leviticus 23 in the KJV

Leviticus 23 in the KNFD

Leviticus 23 in the LBA

Leviticus 23 in the LBLA

Leviticus 23 in the LNT

Leviticus 23 in the LSV

Leviticus 23 in the MAAL

Leviticus 23 in the MBV

Leviticus 23 in the MBV2

Leviticus 23 in the MHNT

Leviticus 23 in the MKNFD

Leviticus 23 in the MNG

Leviticus 23 in the MNT

Leviticus 23 in the MNT2

Leviticus 23 in the MRS1T

Leviticus 23 in the NAA

Leviticus 23 in the NASB

Leviticus 23 in the NBLA

Leviticus 23 in the NBS

Leviticus 23 in the NBVTP

Leviticus 23 in the NET2

Leviticus 23 in the NIV11

Leviticus 23 in the NNT

Leviticus 23 in the NNT2

Leviticus 23 in the NNT3

Leviticus 23 in the PDDPT

Leviticus 23 in the PFNT

Leviticus 23 in the RMNT

Leviticus 23 in the SBIAS

Leviticus 23 in the SBIBS

Leviticus 23 in the SBIBS2

Leviticus 23 in the SBICS

Leviticus 23 in the SBIDS

Leviticus 23 in the SBIGS

Leviticus 23 in the SBIHS

Leviticus 23 in the SBIIS

Leviticus 23 in the SBIIS2

Leviticus 23 in the SBIIS3

Leviticus 23 in the SBIKS

Leviticus 23 in the SBIKS2

Leviticus 23 in the SBIMS

Leviticus 23 in the SBIOS

Leviticus 23 in the SBIPS

Leviticus 23 in the SBISS

Leviticus 23 in the SBITS

Leviticus 23 in the SBITS2

Leviticus 23 in the SBITS3

Leviticus 23 in the SBITS4

Leviticus 23 in the SBIUS

Leviticus 23 in the SBIVS

Leviticus 23 in the SBT

Leviticus 23 in the SBT1E

Leviticus 23 in the SCHL

Leviticus 23 in the SNT

Leviticus 23 in the SUSU

Leviticus 23 in the SUSU2

Leviticus 23 in the SYNO

Leviticus 23 in the TBIAOTANT

Leviticus 23 in the TBT1E

Leviticus 23 in the TBT1E2

Leviticus 23 in the TFTIP

Leviticus 23 in the TFTU

Leviticus 23 in the TGNTATF3T

Leviticus 23 in the THAI

Leviticus 23 in the TNFD

Leviticus 23 in the TNT

Leviticus 23 in the TNTIK

Leviticus 23 in the TNTIL

Leviticus 23 in the TNTIN

Leviticus 23 in the TNTIP

Leviticus 23 in the TNTIZ

Leviticus 23 in the TOMA

Leviticus 23 in the TTENT

Leviticus 23 in the UBG

Leviticus 23 in the UGV

Leviticus 23 in the UGV2

Leviticus 23 in the UGV3

Leviticus 23 in the VBL

Leviticus 23 in the VDCC

Leviticus 23 in the YALU

Leviticus 23 in the YAPE

Leviticus 23 in the YBVTP

Leviticus 23 in the ZBP