Leviticus 4 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa ndi kuchita chilichonse chimene Yehova walamula kuti asachite, azichita izi: 3 “ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake. 4 Wansembeyo abwere nayo ngʼombeyo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova. Asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo ayiphe pamaso pa Yehova. 5 Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 6 Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika. 7 Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 8 Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo. 9 Achotsenso ndi kubwera ndi impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi ndi impsyo 10 monga momwe amachotsera mafuta a ngʼombe yoperekedwa kuti ikhale chopereka chachiyanjano. Tsono wansembe atenthe zimenezi pa guwa lansembe zopsereza. 11 Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo, 12 kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo. 13 “ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu. 14 Akazindikira tchimo limene achita, gulu lonse lipereke mwana wangʼombe wamphongo kuti akhale chopereka chopepesera tchimo ndipo abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 15 Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova. 16 Tsono wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 17 Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga. 18 Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 19 Kenaka achotse mafuta onse a ngʼombeyo ndi kuwatentha pa guwa, 20 ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa. 21 Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse. 22 “ ‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula. 23 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, iye abwere ndi mbuzi yayimuna yopanda chilema kuti ikhale chopereka chake. 24 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mbuziyo ndi kuyiphera pamalo pamene amaphera zopereka zopsereza pamaso pa Yehova. Ichi ndi chopereka chopepesera tchimo. 25 Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a chopereka chopepesera tchimocho ndi chala chake, ndipo awapake pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Athire magazi otsalawo pa tsinde la guwalo. 26 Wansembeyo atenthe mafuta onse pa guwapo monga amatenthera chopereka chachiyanjano. Pochita zimenezi, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo, ndipo adzakhululukidwa. 27 “ ‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula. 28 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo. 29 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 30 Ndipo wansembe atenge magazi ndi chala chake ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza ndi kuthira magazi wotsalawo pa tsinde la guwalo. 31 Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa. 32 “ ‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema. 33 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mwana wankhosayo ndipo amuphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 34 Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo. 35 Iye achotse mafuta onse, monga amachotsera mafuta a mwana wankhosa wa chopereka chachiyanjano, ndipo wansembe awatenthe pa guwa pamodzi ndi zopereka zina zopsereza za Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo limene munthuyo anachita ndipo adzakhululukidwa.