Psalms 112 (BOGWICC)
1 Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova,amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake. 2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. 3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima. 5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,amene amachita ntchito yake mwachilungamo. 6 Ndithu sadzagwedezeka;munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya. 7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova. 8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano. 9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. 10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.