Psalms 122 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Ndinakondwera atandiwuza kuti,“Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” 2 Mapazi athu akuyima mʼzipatazako, Iwe Yerusalemu. 3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzindaumene uli wothithikana pamodzi. 4 Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko,mafuko a Yehova,umboni wa kwa Israeli,kuti atamande dzina la Yehova. 5 Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo,mipando yaufumu ya nyumba ya Davide. 6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu:“Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino. 7 Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako,ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.” 8 Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi angandidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.” 9 Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu,ndidzakufunira zabwino.