Psalms 149 (BOGWICC)
1 Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. 2 Israeli asangalale mwa mlengi wake;anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. 3 Atamande dzina lake povinandi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. 4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. 5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wakendi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. 6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, 7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina,ndi kulanga anthu a mitundu yonse, 8 kumanga mafumu awo ndi zingwe,anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, 9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawoUwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.