Psalms 36 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. 1 Uthenga uli mu mtima mwangawonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:Mu mtima mwakemulibe kuopa Mulungu. 2 Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri,sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake. 3 Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo;iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino. 4 Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa;iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimondipo sakana cholakwa chilichonse. 5 Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo. 6 Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama. 7 Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthuamapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu. 8 Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero. 9 Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala. 10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,chilungamo chanu kwa olungama mtima. 11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa. 12 Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa,aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!