Psalms 39 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide. 1 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zangandipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekereronthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.” 2 Koma pamene ndinali cheteosanena ngakhale kanthu kalikonse kabwinomavuto anga anachulukirabe. 3 Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;kenaka ndinayankhula ndi lilime langa: 4 “Yehova ndionetseni mathero a moyo wangandi chiwerengero cha masiku anga;mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani. 5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;moyo wa munthu aliyense ndi waufupi. Sela 6 Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:Iye amangovutika koma popanda phindu;amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani. 7 “Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?Chiyembekezo changa chili mwa Inu. 8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;musandisandutse chonyozeka kwa opusa. 9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa pangapakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi. 10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu. 11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;mumawononga chuma chawo monga njenjete;munthu aliyense ali ngati mpweya. Sela 12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,mverani kulira kwanga kopempha thandizo;musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;monga anachitira makolo anga onse. 13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalalandisanafe ndi kuyiwalika.”