Psalms 4 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. 1 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,Inu Mulungu wa chilungamo changa.Pumulitseni ku zowawa zanga;chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa. 2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?Sela. 3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana. 4 Kwiyani koma musachimwe;pamene muli pa mabedi anu,santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela 5 Perekani nsembe zolungamandipo dalirani Yehova. 6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova. 7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulukuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano. 8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,pakuti Inu nokha, Inu Yehova,mumandisamalira bwino.