Psalms 64 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 1 Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani. 2 Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa. 3 Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,amaponya mawu awo olasa ngati mivi. 4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha. 5 Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,amayankhula zobisa misampha yawo;ndipo amati, “Adzayiona ndani?” 6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,“Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo. 7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;mwadzidzidzi adzakanthidwa. 8 Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsandi kuwasandutsa bwinja;onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza. 9 Anthu onse adzachita mantha;adzalengeza ntchito za Mulungundi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita. 10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehovandi kubisala mwa Iye,owongoka mtima onse atamande Iye!