Psalms 67 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. 1 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,achititse kuti nkhope yake itiwalire. 2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse. 3 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. 4 Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamondi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi. 5 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. 6 Nthaka yabereka zokolola zake;tidalitseni Mulungu wathu. 7 Mulungu atidalitsekuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.