Zechariah 12 (BOGWICC)
1 Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti, 2 “Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu. 3 Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka. 4 Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina. 5 Pamenepo atsogoleri a Yuda adzayankhula mʼmitima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu ndi amphamvu, chifukwa Yehova Wamphamvuzonse ndiye Mulungu wawo.’ 6 “Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake. 7 “Yehova adzapulumutsa malo okhala Yuda poyamba, kuti ulemu wa nyumba ya Davide ndi wa anthu okhala mu Yerusalemu usapambane ulemu wa Yuda. 8 Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera. 9 Pa tsiku limenelo ndidzawononga mitundu yonse yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu. 10 “Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa. 11 Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido. 12 Dziko lidzalira kwambiri, fuko lililonse pa lokha, akazi awo pa okhanso: fuko la Davide pamodzi ndi akazi awo, fuko la Natani pamodzi ndi akazi awo, 13 nyumba ya Levi pamodzi ndi akazi awo, fuko la Simei pamodzi ndi akazi awo, 14 ndiponso mafuko onse pamodzi ndi akazi awo.
In Other Versions
Zechariah 12 in the ANGEFD
Zechariah 12 in the ANTPNG2D
Zechariah 12 in the AS21
Zechariah 12 in the BAGH
Zechariah 12 in the BBPNG
Zechariah 12 in the BBT1E
Zechariah 12 in the BDS
Zechariah 12 in the BEV
Zechariah 12 in the BHAD
Zechariah 12 in the BIB
Zechariah 12 in the BLPT
Zechariah 12 in the BNT
Zechariah 12 in the BNTABOOT
Zechariah 12 in the BNTLV
Zechariah 12 in the BOATCB
Zechariah 12 in the BOATCB2
Zechariah 12 in the BOBCV
Zechariah 12 in the BOCNT
Zechariah 12 in the BOECS
Zechariah 12 in the BOHCB
Zechariah 12 in the BOHCV
Zechariah 12 in the BOHLNT
Zechariah 12 in the BOHNTLTAL
Zechariah 12 in the BOICB
Zechariah 12 in the BOILNTAP
Zechariah 12 in the BOITCV
Zechariah 12 in the BOKCV
Zechariah 12 in the BOKCV2
Zechariah 12 in the BOKHWOG
Zechariah 12 in the BOKSSV
Zechariah 12 in the BOLCB
Zechariah 12 in the BOLCB2
Zechariah 12 in the BOMCV
Zechariah 12 in the BONAV
Zechariah 12 in the BONCB
Zechariah 12 in the BONLT
Zechariah 12 in the BONUT2
Zechariah 12 in the BOPLNT
Zechariah 12 in the BOSCB
Zechariah 12 in the BOSNC
Zechariah 12 in the BOTLNT
Zechariah 12 in the BOVCB
Zechariah 12 in the BOYCB
Zechariah 12 in the BPBB
Zechariah 12 in the BPH
Zechariah 12 in the BSB
Zechariah 12 in the CCB
Zechariah 12 in the CUV
Zechariah 12 in the CUVS
Zechariah 12 in the DBT
Zechariah 12 in the DGDNT
Zechariah 12 in the DHNT
Zechariah 12 in the DNT
Zechariah 12 in the ELBE
Zechariah 12 in the EMTV
Zechariah 12 in the ESV
Zechariah 12 in the FBV
Zechariah 12 in the FEB
Zechariah 12 in the GGMNT
Zechariah 12 in the GNT
Zechariah 12 in the HARY
Zechariah 12 in the HNT
Zechariah 12 in the IRVA
Zechariah 12 in the IRVB
Zechariah 12 in the IRVG
Zechariah 12 in the IRVH
Zechariah 12 in the IRVK
Zechariah 12 in the IRVM
Zechariah 12 in the IRVM2
Zechariah 12 in the IRVO
Zechariah 12 in the IRVP
Zechariah 12 in the IRVT
Zechariah 12 in the IRVT2
Zechariah 12 in the IRVU
Zechariah 12 in the ISVN
Zechariah 12 in the JSNT
Zechariah 12 in the KAPI
Zechariah 12 in the KBT1ETNIK
Zechariah 12 in the KBV
Zechariah 12 in the KJV
Zechariah 12 in the KNFD
Zechariah 12 in the LBA
Zechariah 12 in the LBLA
Zechariah 12 in the LNT
Zechariah 12 in the LSV
Zechariah 12 in the MAAL
Zechariah 12 in the MBV
Zechariah 12 in the MBV2
Zechariah 12 in the MHNT
Zechariah 12 in the MKNFD
Zechariah 12 in the MNG
Zechariah 12 in the MNT
Zechariah 12 in the MNT2
Zechariah 12 in the MRS1T
Zechariah 12 in the NAA
Zechariah 12 in the NASB
Zechariah 12 in the NBLA
Zechariah 12 in the NBS
Zechariah 12 in the NBVTP
Zechariah 12 in the NET2
Zechariah 12 in the NIV11
Zechariah 12 in the NNT
Zechariah 12 in the NNT2
Zechariah 12 in the NNT3
Zechariah 12 in the PDDPT
Zechariah 12 in the PFNT
Zechariah 12 in the RMNT
Zechariah 12 in the SBIAS
Zechariah 12 in the SBIBS
Zechariah 12 in the SBIBS2
Zechariah 12 in the SBICS
Zechariah 12 in the SBIDS
Zechariah 12 in the SBIGS
Zechariah 12 in the SBIHS
Zechariah 12 in the SBIIS
Zechariah 12 in the SBIIS2
Zechariah 12 in the SBIIS3
Zechariah 12 in the SBIKS
Zechariah 12 in the SBIKS2
Zechariah 12 in the SBIMS
Zechariah 12 in the SBIOS
Zechariah 12 in the SBIPS
Zechariah 12 in the SBISS
Zechariah 12 in the SBITS
Zechariah 12 in the SBITS2
Zechariah 12 in the SBITS3
Zechariah 12 in the SBITS4
Zechariah 12 in the SBIUS
Zechariah 12 in the SBIVS
Zechariah 12 in the SBT
Zechariah 12 in the SBT1E
Zechariah 12 in the SCHL
Zechariah 12 in the SNT
Zechariah 12 in the SUSU
Zechariah 12 in the SUSU2
Zechariah 12 in the SYNO
Zechariah 12 in the TBIAOTANT
Zechariah 12 in the TBT1E
Zechariah 12 in the TBT1E2
Zechariah 12 in the TFTIP
Zechariah 12 in the TFTU
Zechariah 12 in the TGNTATF3T
Zechariah 12 in the THAI
Zechariah 12 in the TNFD
Zechariah 12 in the TNT
Zechariah 12 in the TNTIK
Zechariah 12 in the TNTIL
Zechariah 12 in the TNTIN
Zechariah 12 in the TNTIP
Zechariah 12 in the TNTIZ
Zechariah 12 in the TOMA
Zechariah 12 in the TTENT
Zechariah 12 in the UBG
Zechariah 12 in the UGV
Zechariah 12 in the UGV2
Zechariah 12 in the UGV3
Zechariah 12 in the VBL
Zechariah 12 in the VDCC
Zechariah 12 in the YALU
Zechariah 12 in the YAPE
Zechariah 12 in the YBVTP
Zechariah 12 in the ZBP